Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 5

Kodi Mudzaona Ciani Mukabwela ku Misonkhano Yathu

Kodi Mudzaona Ciani Mukabwela ku Misonkhano Yathu

Ku Argentina

Ku Sierra Leone

Ku Belgium

Ku Malaysia

Anthu ambili analeka kupita ku machalichi cifukwa cakuti sapezako thandizo lauzimu kapena citonthozo. Nanga n’cifukwa ciani mufunika kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova? Kodi mudzapezako ciani kumeneko?

Mudzasangala kukhala ndi anthu amene amakondana ndi kusamalilana. Akristu a m’zaka za zana loyamba, anali m’mipingo yosiyana-siyana ndipo anali kusonkhana kuti alambile Mulungu, aphunzile Malemba, ndi kulimbikitsana. (Aheberi 10:24, 25) Popeza kuti pamisonkhano yao anali kukondana, io anali kuona kuti ali pakati pa mabwenzi eni-eni, inde, abale ndi alongo ao auzimu. (2 Atesalonika 1:3; 3 Yohane 14) Ifenso timatsatila citsanzo cao ndipo timasangalala.

Ubwino wotsatila mfundo za m’Baibo. Pa nthawi ya m’Baibo, amuna, akazi, ndi ana anali kusonkhana pamodzi. Ndi mmene zilili masiku ano. Aphunzitsi ofikapo amagwilitsila nchito Baibo kutithandiza kuzindikila mmene tingagwilitsile nchito mfundo za m’Baibo paumoyo wathu. (Deuteronomo 31:12; Nehemiya 8:8) Pa nkhani zokambilana ndi omvela ndi poimba nyimbo, onse amakhala ndi mwai wotengako mbali. Zimenezi zimatipatsa mwai wofotokoza za ciyembekezo cathu cacikristu.—Aheberi 10:23.

Mudzakhala ndi mwai wolimbitsa cikhulupililo canu mwa Mulungu. Pa nthawi ina mtumwi Paulo anauza mpingo wina kuti: “Ndikulakalaka kukuonani . . . kuti tidzalimbikitsane mwa cikhulupililo, canu ndi canga.” (Aroma 1:11, 12) Pamisonkhano yathu timayanjana ndi abale athu auzimu nthawi zonse, ndipo izi zimalimbitsa cikhulupililo cathu ndi cikhumbo cathu cotsatila mfundo za Cikristu.

Bwanji osabwela kumsonkhano umene mpingo wathu udzakhala nao mlungu uno, kuti mukaone nokha zimene takambitsilana? Tidzakulandilani ndi manja aŵili. Misonkhano yathu ni yaulele ndipo sipakhala kuyendetsa mbale ya zopeleka iyai.

  • Kodi misonkhano yathu imatsatila citsanzo citi?

  • Kodi kupezeka kwathu pamisonkhano yacikristu kuli ndi ubwino wanji?