Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 40

Tiyenela Kucita Ciyani Kuti Tikhale Oyela Pamaso pa Mulungu?

Tiyenela Kucita Ciyani Kuti Tikhale Oyela Pamaso pa Mulungu?

Tiyelekeze kuti mayi akukonzekeletsa mwana wake wamng’ono kupita ku sukulu. Mayiyo akuonetsetsa kuti mwana wakeyo wasamba, zovala zake n’zoyela, ndipo akuoneka waukhondo. Izi zimathandiza mwanayo kukhala na thanzi labwino, ndipo zimaonetsa kuti makolo ake amam’samalila bwino. Yehova naye n’cimodzi-modzi. Pokhala Tate wathu wacikondi iye amafuna kuti tizikhala oyela, kuthupi komanso m’makhalidwe athu. Ngati tikhala aukhondo, timapindula ife eni, ndiponso Mulungu amalemekezeka.

1. Kodi tingakhale bwanji oyela kuthupi?

Yehova akutiuza kuti: “Mukhale oyela.” (1 Petulo 1:16) Ciyelo cimagwilizana na ukhondo wa kuthupi komanso wa makhalidwe. Tingakhale oyela kuthupi mwa kusamba nthawi zonse, kapena tsiku lililonse ngati n’kotheka. Tiyenelanso kumacapa zovala zathu, kusamalila nyumba zathu, komanso mamotoka athu. Cina, tiyenelanso kuthandiza kuyeletsa Nyumba ya Ufumu. Tikamakhala oyela kuthupi, timapeleka ulemu kwa Yehova.—2 Akorinto 6:3, 4.

2. Kuti tikhale oyela, kodi tiyenela kupewa zinthu ziti?

Baibo imatilimbikitsa kuti “ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi kapena mzimu.” (2 Akorinto 7:1) Conco, timayesetsa kupewa cinthu ciliconse cimene cingawononge thupi lathu kapena maganizo athu. Kuti tikhale na malingalilo okondweletsa Yehova, tiyenela kucotsa mwamsanga malingalilo alionse osayenela amene angabwele mwa ife. (Salimo 104:34) Tiyenela kulimbikilanso kukhala oyela m’malankhulidwe athu.—Ŵelengani Akolose 3:8.

Kodi ni zinthu zinanso ziti zimene zingatidetse kuthupi komanso m’makhalidwe athu? Zilipo zinthu zina zimene zingadetse thupi lathu. Mwa ici, tiyenela kupewa fodya wokoka, wa m’mphuno, wa m’kamwa, komanso mtundu uliwonse wa mankhwala osokoneza bongo. Popewa zinthu zimenezi, timakhala athanzi labwinopo, ndipo timalemekeza mphatso ya moyo. Timakhalanso oyela m’makhalidwe athu tikamapewa mcitidwe wosayenela wodzipukusa malisece, kapenanso kutamba zolaula. (Salimo 119:37; Aefeso 5:5) N’zoona kuti cingakhale covuta kupewa macitidwe amenewa, koma Yehova akhoza kutithandiza.—Ŵelengani Yesaya 41:13.

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani cifukwa cake timalemekeza Yehova tikakhala oyela kuthupi, na mmene tingagonjetsele macitidwe onyansa.

3. Ukhondo wa pathupi umalemekeza Yehova

Tikhoza kuona mmene Yehova amaionela nkhani ya ukhondo tikaŵelenga malamulo amene anapatsa Aisiraeli akale. Ŵelengani Ekisodo 19:10, komanso 30:17-19, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Malemba aya amaonetsa ciyani za mmene Yehova amaonela ciyelo ca pathupi?

  • Kodi ni macitidwe abwino ati amene angakuthandizeni kukhalabe woyela pathupi?

Kukhala oyela pathupi kumafuna nthawi komanso khama. Koma zimenezi n’zotheka ndithu kulikonse kumene tikukhala, olo tikhale na ndalama zocepa. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

  • Zinthu zathu zikamakhala zaudongo komanso zaukhondo, kodi zimalemekeza bwanji nchito yathu yolalikila?

4. Gonjetsani macitidwe oipa

Yehova angatithandize kugonjetsa mcitidwe woipa uliwonse

Ngati mumakoka fodya kapena kugwilitsila nchito mankhwala osokoneza bongo, mukudziŵa kuti cimakhala covuta kuti muleke. Kodi cingathandize n’ciyani? Ganizilani mavuto amene mcitidwe umenewo ungabweletse pa inu. Ŵelengani Mateyu 22:37-39, na kukambilana mmene fodya kapena mankhwala osokoneza bongo amakhudzila . . .

  • ubwenzi wa munthu na Yehova.

  • banja la munthu komanso anthu ena omuyandikila.

Konzekelani mmene mungagonjetsele mcitidwe woipa uliwonse. a Tambani VIDIYO.

Ŵelengani Afilipi 4:13, na kukambilana funso ili:

  • Kodi kupemphela nthawi zonse, kuŵelenga Baibo, na kumapezeka pamisonkhano, kungapatse bwanji munthu mphamvu zofunikila kuti agonjetse mcitidwe woipa umene unamuloŵelela?

5. Menyani nkhondo kuti mugonjetse malingalilo osayenela komanso macitidwe oipa

Ŵelengani Akolose 3:5, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi timadziŵa bwanji kuti zamalisece, kutumizilana zolaula, kapena kudzipukusa malisece, ni zinthu zosayenela pamaso pa Yehova?

  • Kodi muona kuti n’zabwino Yehova kutiyembekezela kukhala oyela m’makhalidwe athu? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?

Dziŵani mmene mungamenyele nkhondo yogonjetsa malingalilo osayenela. Tambani VIDIYO.

Yesu anafotokoza fanizo loonetsa kuti tiyenela kucita zonse zotheka kuti tikhalebe oyela m’makhalidwe athu. Ŵelengani Mateyu 5:29, 30, na kukambilana funso ili:

  • Yesu sanatanthauze kuti tizidzivulaza kuthupi. M’malo mwake, anaonetsa kuti tifunika kucitapo kanthu. Kodi munthu ayenela kuyesetsa kucita ciyani kuti apewe malingalilo osayenela? b

Ngati mulimbikila kuti mugonjetse malingalilo osayenela, Yehova amayamikila kuyesetsa kwanu. Ŵelengani Salimo 103:13, 14, na kukambilana funso ili:

  • Ngati mukuyesetsa kuti muleke mcitidwe wina wake wosayenela, n’cifukwa ciyani lemba ili n’lolimbikitsa kuti musaleke kumenya nkhondoyo?

Dzedzele-dzedzele si kugwa!

N’capafupi kuganiza kuti ‘paja n’nalephelanso, nivutikilanji, ningoleka kulimbana nazo.’ Koma ganizilani izi: Kodi munthu wocita mpikisano wothamanga akapunthwa n’kugwa, kodi ndiye kuti walephela mpikisanowo? Kapena kodi amabwelela n’kukayambilanso mwatsopano? Iyayi. Mukalephela kamodzi kapena kangapo, sindiye kuti basi mwalephela nkhondo yolimbana na mcitidwe woipawo. Sizikutanthauzanso kuti kupita patsogolo konse kumene mwacita kumbuyoku kwafafanizika ayi. Poyamba, kulephela kudzacitika ndithu, mwina kangapo konse. Koma pothela pake mudzapambana nkhondoyo. Musafulumile kutaya mtima! Mwa thandizo la Yehova, mungathe kuugonjetsa mcitidwe woipawo.

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Mcitidwe umenewu unaniloŵelela. Siningakwanitse kuleka.”

  • Kodi munthu wotelo mungamuŵelengele lemba liti lomuonetsa kuti mwa thandizo la Yehova, akhoza kuuleka mcitidwe woipawo?

CIDULE CAKE

Timakondweletsa Yehova tikamakhala oyela pathupi pathu, m’maganizo mwathu, komanso m’makhalidwe athu.

Mafunso Obweleza

  • Kodi kukhala oyela n’kofunika cifukwa ciyani?

  • Muyenela kucita ciyani kuti muzikhala oyela pathupi?

  • Kuti malingalilo anu komanso makhalidwe anu azikhala oyela, muyenela kucita ciyani?

Colinga

FUFUZANI

Ni zinthu ziti zapafupi zimene mungacite kuti mukhale woyela pathupi, ngakhale kuti ndinu wosaukila?

Thanzi na Ukhondo—Kusamba M’manja (3:01)

Onani masitepe amene mungatenge kuti muleke kukoka fodya.

“Mmene Mungalekele Kukoka Fodya” (Galamuka!, May 2010)

Onani mmene mwamuna wina anagonjetsela mcitidwe wotamba zamalisece umene unamuloŵelela.

“Zinanitengela Nthawi Yaitali Kuti Nisinthe” (Nsanja ya Mlonda Na. 4 2016)

a Nkhani yakuti “Mmene Mungalekele Kukoka Fodya,” yopezeka pa mbali yakuti Fufuzani m’phunzilo lino, ifotokoza masitepe amene munthu angatenge kuti aleke mcitidwe woipa uliwonse umene unamuloŵelela.