Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuonetsa Kukoma Mtima Kamodzi Cabe

Kuonetsa Kukoma Mtima Kamodzi Cabe

ATATE ake John anabatizika n’kukhala Mboni ya Yehova cakumapeto kwa zaka za m’ma 1950, m’tauni yaing’ono ku Gujarat, m’dziko la India. John pamodzi na abale ake ndi alongo ake asanu, kuphatikizapo amayi awo, onse anali Akatolika odzipeleka ndipo anali kutsutsa zimene atate awo anali kukhulupilila.

Tsiku lina, atate ake John anam’tuma kuti akapeleke kalata kwa m’bale wina wa mumpingo mwawo. Koma m’maŵa mwa tsiku limenelo, John anadziceka kwambili pa cala pamene anali kutsegula lidi ya cithini. Ngakhale zinali conco, iye anali kufuna kucita zimene atate ake anam’tuma. Conco, anatenga kansalu n’kumanga cala cimene anadzicekaco, ndipo anayenda wapansi kukapeleka kalatayo.

Pamene John anafika, mkazi wa m’baleyo, amenenso anali wa Mboni za Yehova, analandila kalatayo. Mlongoyo anaona kuti John anali atadziceka pacala. Conco, anaganiza zakuti am’thandize. Anatenga mankhwala na zina zothandizila munthu akavulala, ndipo anatsuka cilondaco ndi mankhwala n’kumangapo na bandeji. Kenako anam’pangila tiyi. Pamene anali kucita zonsezi, anali kukamba naye nkhani za m’Baibo mwaubwenzi.

Kufika panthawi imeneyi, John anayamba kusintha mmene anali kuonela a Mboni. Conco, anafunsa mafunso mlongoyo pa nkhani ziŵili zimene cikhulupililo cake ndi ca atate ake cinali kusiyana. Anafunsa ngati Yesu ni Mulungu, komanso ngati n’koyenela kuti Akhristu azipemphela kwa Mariya. Popeza kuti mlongoyo anali kudziŵa kukamba citundu ca John ca Cigujarati, anamuyankha poseŵenzetsa Baibo, ndipo anam’patsa kabuku kakuti, “This Good News of the Kingdom,(“Uthenga Uwu Wabwino wa Ufumu”).

Pambuyo pakuti waŵelenga kabuku kameneko, John anazindikila kuti zimene anali kuŵelengazo ni coonadi ca m’Baibo. Iye anapita kwa wansembe wa ku chechi kwawo kukam’funsa mafunso amodzi-modzi amene anakambilana ndi mlongo uja. Pamene anali kumufunsa, wansembeyo anakwiya ngako cakuti anam’ponyela Baibo, uku akukalipa, amvekele: “Wasanduka Satana iwe! Ni pati m’Baibo pamene pamakamba kuti Yesu si Mulungu? Nanga ni pati pamene pamakamba kuti sitifunika kulambila Mariya? Nilongoze!” John anakhumudwa ngako na zimene wansembeyo anacita cakuti anamuuza kuti: “Sinidzapondamonso phazi m’chechi ya Akatolika.” Ndipo analekadi.

John anayamba kuphunzila Baibo ndi Mboni za Yehova, ndipo anatsimikiza mtima kuyamba kutumikila Yehova. M’kupita kwa nthawi, ena a m’banjalo anacitanso cimodzi-modzi. Mpaka lomba, John akali na cipsela ku cala cake ca kudzanja lamanja cimene anadziceka zaka 60 zapitazo. Iye amakondwela akakumbukila cinthu cimodzi coonetsa kukoma mtima cimene cinam’thandiza kuti ayambe kulambila koona.—2 Akor. 6:4, 6.