Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NSANJA YA MLONDA Na. 1 2023 | Baibo Ingathandize Odwala Matenda a Maganizo

Pa dziko lonse lapansi, anthu mamiliyoni ambili akudwala matenda a maganizo. Matendawa akuvutitsa anthu osiyanasiyana, akulu na ana omwe, olemela kapena osauka, ophunzila na osaphunzila, komanso anthu a mtundu uliwonse, na cipembedzo ciliconse. Kodi matenda a maganizo n’ciyani? Nanga amawakhudza motani anthu? Magazini ino ifotokoza kufunika kolandila cithandizo coyenela ca cipatala, komanso mmene mfundo za m’Baibo zingathandizile anthu odwala matendawa.

 

Matenda a Maganizo ni Mlili wa Padziko Lonse

Munthu aliyense angadwale matenda a maganizo mosasamala kanthu za msinkhu wake kapena mmene anakulila. Onani mmene malangizo a m’Baibo angakuthandizileni kukhala na thanzi labwino la maganizo.

Mulungu Amasamala za Inu

Mungatsimikize bwanji kuti Yehova Mulungu amamvetsa maganizo anu na mmene mumamvela kuposa wina aliyense?

1 | Pemphelo—“Mutulileni Nkhawa Zanu Zonse”

Kodi mungamuuzedi Mulungu m’pemphelo nkhawa iliyonse imene muli nayo? Kodi pemphelo lingawathandize bwanji anthu amene amavutika na nkhawa?

2 | “Malemba . . . Amatilimbikitsa”

Uthenga wa m’Baibo umatipatsa ciyembekezo codalilika cakuti zinthu zopweteka mtima zidzatha posacedwa.

3 | Mmene Zitsanzo za m’Baibo Zingakuthandizileni

Nkhani za m’Baibo za amuna na akazi amene anamvelapo mmene ife timavelela zingatithandize kuona kuti sitili tokha tikamalimbana na maganizo osautsa.

4 | Baibo Ili na Malangizo Othandiza

Onani mmene kuganizila mavesi a m’Baibo na kudziikila zolinga zimene mungathe kuzikwanilitsitsa kungakuthandizileni kupilila matenda anu a maganizo.

Mmene Tingathandizile Odwala Matenda a Maganizo

Mungathe kuthandiza mnzanu amene ali na matenda a maganizo.