Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Anthu Ofatsa Adzalandila Dziko Lapansi”

“Anthu Ofatsa Adzalandila Dziko Lapansi”

Ambili a ise taonako zinthu zopanda cilungamo zicitika, anthu abwino ndi osalakwa kupondelezewa na anthu oipa. Kodi nthawi idzafika pamene kuipa na kupanda cilungamo zidzasila?

M’Baibo, Salimo 37 imapeleka yankho na citsogozo kwa ise masiku ano. Onani zimene imakamba pa mafunso ofunika kwambili otsatilawa.

  • Kodi tifunika kucita ciani ngati ena akutipondeleza?—Vesi 1, na 2.

  • N’ciani cidzacitikila anthu oipa?—Vesi 10.

  • Kodi anthu ocita zabwino ali na tsogolo yabwanji?—Vesi 11, na 29.

  • Kodi manje tiyenela kucita ciani?—Vesi 34.

Mau ouzilidwa a mu Salimo 37 aonetselatu kuti anthu amene ‘ayembekezela Yehova, ndi kusunga njila zake’ ali na tsogolo labwino. A Mboni za Yehova ni okonzeka kukuthandizani kuphunzila Baibo. Komanso angakuthandizeni kudziŵa zimene mungacite kuti imwe na okondedwa anu mukhale na tsogolo labwino.