Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mapeto Adzafika Liti? Zimene Yesu Anakamba

Kodi Mapeto Adzafika Liti? Zimene Yesu Anakamba

Monga taonela m’nkhani yapita, Baibo ikamakamba za kutha kwa dziko, sitanthauza kutha kwa dziko lapansili kapena kutha kwa mtundu wa anthu. Koma imatanthauza kutha kwa dongosolo loipali la zinthu na onse amene amalicilikiza. Koma kodi Baibo imafotokoza nthawi pamene dongosolo loipali la zinthu lidzatha?

ONANI MFUNDO ZIŴILI ZIMENE YESU ANAKAMBA PONENA ZA MAPETO:

“Cotelo khalanibe maso cifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.”—MATEYU 25:13.

“Khalani maso, khalani chelu, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwilatu idzafika.”—MALIKO 13:33.

Conco padziko lapansi palibe aliyense amene adziŵa nthawi imene dongosolo loipali la zinthu lidzawonongedwa. Koma Mulungu anakhazikitsa nthawi yoikidwilatu, ‘inde tsiku ndi ola’ limene mapeto adzafika. (Mateyu 24:36) Kodi izi zitanthauza kuti palibiletu njila imene tingadziŵile kuti mapeto ali pafupi? Iyai. Yesu anauza ophunzila ake kuti ayenela kukhala chelu kuti aone zocitika zoonetsa kuti mapeto ali pafupi.

CIZINDIKILO CAKUTI MAPETO ALI PAFUPI

Yesu anakamba kuti zocitika zimenezi zidzakhala cizindikilo ca “mapeto a nthawi ino.” Iye anati: “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.” (Mateyu 24:3, 7) Anakambanso kuti kudzakhala “milili”, kutanthauza matenda ofalikila okhudza anthu ambili. (Luka 21:11) Kodi mumaziona zocitika zimene Yesu anakamba?

Masiku ano, anthu amavutika na nkhondo zoopsa, njala, zivomezi, komanso matenda osiyanasiyana. Mwacitsanzo mu 2004, civomezi coopsa cimene cinacitikila pa nyanja ya Indian Ocean cinayambitsa tsunami amene anapha anthu pafupifupi 225,000. Mʼzaka zitatu mlili wa COVID-19 unapha anthu pafupifupi 6.9 miliyoni. Yesu anakamba kuti zocitika ngati zimenezi zidzaonetsa kuti mapeto a dzikoli ali pafupi.

“MASIKU OTSILIZA”

M’Baibo, nthawi imene mapeto ali pafupi kufika imachedwa “masiku otsiliza.” (2 Petulo 3:3, 4) Lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 linakambilatu kuti m’masiku otsiliza anthu adzakhala na makhalidwe oipa. (Onani bokosi lakuti “Mmene Anthu Adzakhalila Mapeto a Dzikoli Atatsala Pang’ono Kufika.”) Kodi masiku ano mumawaona anthu odzikonda, adyela, oopsa, komanso opanda cikondi? Zimenezi nazonso ni umboni wakuti mapeto a dzikoli ali pafupi kwambili.

Kodi masiku otsiliza adzatenga utali wotani? Baibo imakamba kuti adzatenga “kanthawi kocepa” cabe. Kenako, Mulungu adzawononga “amene akuwononga dziko lapansi.”—Chivumbulutso 11:15-18; 12:12.

DZIKO LA PARADAISO LILI PAFUPI

Mulungu anaika kale tsiku na ola pamene adzawononga dongosolo loipali la zinthu. (Mateyu 24:36) Koma palinso uthenga wina wabwino wakuti Mulungu “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe.” (2 Petulo 3:9) Iye wapatsa anthu mwayi wophunzila za cifunilo cake na kuyamba kumumvela. Cifukwa ciani? Cifukwa afuna kuti tidzapulumuke pamene dzikoli lidzawongedwa. Afunanso kuti tikakhalemo m’dziko lake latsopano pamene lidzakhala paradaiso.

Mulungu anayambitsa nchito yapadziko lonse yophunzitsa anthu kuti adziŵe zimene angacite kuti akakhalemo m’dziko latsopano lolamulidwa na Ufumu wake. Yesu anakamba kuti Uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu udzalalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyu 24:14) Mboni za Yehova zimathela maola mabiliyoni polalikila na kuphunzitsa anthu za uthenga wa m’Baibo wopatsa ciyembekezo. Yesu anakamba kuti nchito yolalikila imeneyi idzacitika padziko lonse lapansi mapeto asanafike.

Nthawi yakuti ulamulilo wa anthu uthe yatsala pang’ono. Koma uthenga wabwino ni wakuti mungathe kupulumuka mapeto a dzikoli na kudzakhala m’dziko la Paradaiso limene Mulungu analonjeza. Nkhani yotsatila idzafotokoza zimene mungacite kuti mudzakhalemo m’dziko latsopano limenelo.

Ulosi wa Yesu wokamba za masiku otsiliza umatipatsa ciyembekezo