Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NSANJA YA MLONDA Na. 3 2021 | Kodi Mungacite Ciani Kuti Mukhale na Tsogolo Labwino?

N’ciani cimene mungacite kuti mukhale na tsogolo labwino? Nkhani za m’magazini ino zifotokoza zinthu zosiyana-siyana zimene anthu amacita pofuna kukhala na tsogolo labwino. Zikuthandizaninso kudziŵa gwelo lokhalo la malangizo odalilika amene angakuthandizeni kukhala na tsogolo labwino.

 

Aliyense Amafuna Kukhala na Tsogolo Labwino

Ngati zinthu zosayembekezeleka zasokoneza umoyo wa anthu, kodi mungapeze kuti malangizo odalilika?

Kodi Tsogolo Lanu Limadalila Ciani Maka-maka?

Ambili amene amapenda nyenyezi, kukhulupilila feng shui, kapena kulambila mizimu ya makolo, komanso amene amakhulupilila za kubadwanso kukhala cinthu cina, amaganiza kuti mphamvu inayake yosaoneka imalamulila tsogolo lawo.

Kodi Maphunzilo na Ndalama Zingakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?

Ambili aona kuti maphunzilo apamwamba na cuma siziwathandiza kupeza zimene anali kuyembekezela.

Kodi Kukhala Munthu Wabwino Kungakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?

Kukhala munthu wabwino n’kofunika, koma si kokwanila kuti munthu akhale na tsogolo labwino.

N’ciani Cingatithandize Kukhala na Tsogolo Labwino?

Popanga zisankho, nthawi zambili timafunsila malangizo kwa munthu wamkulu komanso wanzelu kuposa ife. Mofananamo, tingapeze malangizo odalilika otithandiza kukhala na tsogolo labwino.

Mungasankhe Mmene Tsogolo Lanu Lidzakhalile

Kodi tingasankhe kukhala na tsogolo lotani?

Mmene Mungakhalile na Tsogolo Labwino

Muona kuti n’ciani cingatithandize kukhala na tsogolo labwino?