Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | BAIBULO—MMENE YAPULUMUKILA

Baibulo Siinawole

Baibulo Siinawole

VUTO LIMENE LINALIPO: Olemba Baibulo ndi okopela malemba, nthawi zambili anali kuseŵenzetsa gumbwa ndi zikopa (zikumba) za nyama. * (2 Timoteyo 4:13) Kodi zinthu zimenezi zikanapangitsa bwanji kuti Baibulo iwonongeke?

Gumbwa imang’ambika mosavuta, imasintha maonekedwe, ndipo imawonongeka. Akatswili odziŵa mbili ya ku Iguputo, Richard Parkinson ndi Stephen Quirke, anakamba kuti: “Gumbwa amawola mwamsanga ndi kusanduka dothi. Akasungidwa, akhoza kuwola ndi cinyontho kapena kudyewa ndi makoswe kapenanso tuzilombo twina, makamaka ciswe ngati amubisa m’nthaka.” Ofufuza anapeza kuti akaika gumbwa padzuŵa kapena pamalo a cinyontho, amawonongeka mofulumila.

Cikumba ca nyama n’colimba kupambana gumbwa, koma cimawonongeka ngati sicinasamalidwe bwino, kapena ngati caikidwa pamalo otentha kwambili, a cinyontho, kapena padzuŵa. * Cikumba naconso cimadyewa na tuzilombo. Ndiye cifukwa cake zolemba zambili zakale kulibe masiku ano. Baibulo ikanawonongeka, sembe uthenga wake kulibe.

MMENE BAIBULO INATETEZEKELA: M’cilamulo cimene Ayuda anapatsidwa, munali lamulo lakuti mfumu iliyonse iyenela “kukopela buku lakelake la Cilamulo,” kutanthauza mabuku asanu oyambilila a m’Baibulo. (Deuteronomo 17:18) Kuonjezela apo, okopela malemba aluso analemba mipukutu yambili cakuti pofika m’nthawi ya atumwi, Malemba anali kupezeka m’masunagoge a m’dziko lonse la Isiraeli, ngakhale kutali kwambili ku Makedoniya. (Luka 4:16, 17; Machitidwe 17:11) Kodi mipukutu yakale imeneyo inapulumuka bwanji?

Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inapezeka m’mitsuko imene anaisungila m’mapanga a m’zipululu. Mipukutuyi yakhalapo kwa zaka zambili

Katswili wa Cipangano Catsopano dzina lake Philip W. Comfort anati: “Ayuda anali kukonda kuika mipukutu ya Malemba m’mitsuko kuti isungike bwino.” Mwacionekele, Akhiristu anapitiliza kucita zimenezo. Ndipo mipukutu ina yoyambilila ya Baibulo inapezeka m’mitsuko, m’zipinda zosungilamo zinthu, ndi m’mapanga. Ina anaipeza m’zipululu.

ZOTSATILAPO ZAKE: Mipukutu ya Baibulo masauzande ambili ikalipo. Ina mwa mipukutu imeneyo inalembedwa zaka zoposa 2,000 zapitazo. Palibe buku lina lakale limene lili ndi mipukutu yambili imene inalembedwa kale kwambili monga ya Baibulo.

^ par. 3 Gumbwa ndi zomela zinazake za m’madzi zimene kale anali kupangila mapepala.

^ par. 5 Mwacitsanzo, cikalata ca boma la United States coonetsa kuti dzikolo lalandila ufulu wodzilamulila cinalembedwa pa cikumba ca nyama. Koma tsopano n’cowonongeka kwambili cakuti mawu ambili anafutika ngakhale kuti papita zaka zosakwana 250.