Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Baibo ni Gwelo Lodalilika la Coonadi

Baibo ni Gwelo Lodalilika la Coonadi

M’mbili yonse, anthu a zikhalidwe zosiyana-siyana amaona kuti Baibo ni gwelo lodalilika la coonadi. Masiku ano, anthu mamiliyoni amatsatila ziphunzitso za m’Baibo. Koma ena amakamba kuti Baibo ni buku la nthano, ndipo mfundo zake n’zosathandiza masiku ano. Nanga imwe muganiza bwanji? Kodi m’Baibo mungapezeke coonadi?

CIFUKWA CAKE MUYENELA KUIDALILA BAIBO

Kodi mungadziŵe bwanji ngati Baibo ni bukudi lodalilika? Tiyelekeze motele: Tinene kuti muli na mnzanu amene wakhala akukuzani zoona nthawi zonse kwa zaka zambili, kodi simungamudalile? Mofanana na mnzanuyo, kodi Baibo imakamba zoona nthawi zonse? Onani zitsanzo izi.

Olemba Baibo Anali Oona Mtima

Olemba Baibo anali oona mtima kwambili, cakuti analemba zimene analakwitsa na zolephela zawo. Mwacitsanzo, mneneli Yona analemba za kusamvela kwake. (Yona 1:1-3) Ndipo m’mawu otsiliza a buku la m’Baibo lodziŵika na dzina lake, analemba za uphungu umene Mulungu anam’patsa. Koma cifukwa ca kudzicepetsa, sanalembe mmene anasinthila maganizo olakwika amene anali nawo. (Yona 4:1, 4, 10, 11) Kuona mtima kwa onse olemba Baibo, kuonetsa kuti anali kukonda kwambili coonadi.

Malangizo Ake ni Othandiza

Kodi nthawi zonse Baibo imapeleka malangizo othandiza pa umoyo? Inde. Mwacitsanzo, onani zimene Baibo imakamba pa nkhani ya kukhala pa ubale wabwino ndi ena. Imati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.” (Mateyu 7:12) Imakambanso kuti: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Inde, mfundo za coonadi za m’Baibo zikali zothandiza, kucokela pamene zinalembedwa mpaka pano.

Ili na Mbili Yodalilika

Kwa zaka zambili, akatswili ofukula zinthu zakale apeza maumboni otsimikizila kuti anthu na malo osiyana-siyana ochulidwa m’Baibo analikodi. Apezanso maumboni otsimikizila kuti nthawi ya zocitika za m’Baibo ni yolondola. Mwacitsanzo, ganizilani umboni umodzi uwu. Baibo imakamba kuti m’nthawi ya Nehemiya, anthu a ku Turo (Afoinike a ku Turo) amene anali kukhala mu Yerusalemu anali kubweletsa ku Yerusalemu “nsomba ndi malonda osiyanasiyana.”—Nehemiya 13:16.

Kodi pali umboni uliwonse wotsimikizila kuti zimene zili pa vesi ya m’Baibo imeneyi n’zoona? Inde ulipo. Akatswili ofukula zinthu zakale apeza zinthu za ku Foinike m’dziko la Israel. Izi zionetsa kuti panali kucitika malonda pakati pa maiko aŵiliwa. Kuwonjezela apo, ku Yerusalemu anafukula minga za nsomba za ku Nyanja ya Mediterranean. Akatswili ofukula zinthu zakale amakamba kuti amalonda ndiwo anali kubweletsa nsombazo kucokela kutali ku maiko a m’mbali mwa nyanjayo. Pambuyo poona bwino-bwino umboniwo, katswili wina wa Baibo dzina lake Benjamin Noonan anati: “Mawu a pa Nehemiya 13:16 akuti anthu a ku Turo anali kugulitsa nsomba ku Yerusalemu aoneka ni azoona.”

Imakamba Zoona pa za Sayansi

Baibo ni buku yokamba za kulambila komanso mbili yakale. Koma ikakamba pa nkhani za sayansi, imakamba zoona. Onani citsanzo cimodzi ici.

Zaka pafupi-fupi 3,500 zapitazo, Baibo inakamba kuti dziko lapansi lili “m’malele.” (Yobu 26:7) Izi zinali zosiyana kwambili na zimene ena anali kukamba, zakuti dziko lapansi linayangalala pamadzi kapena zakuti lili pa msana pa cifulu cacikulu. Patapita zaka 1,100 kucokela pamene buku la Yobu inalembedwa, anthu anali kukambabe kuti n’zosatheka dziko lapansi kukhala m’malele, koma kuti linakhazikika pa cinacake. Koma m’caka ca 1687, wasayansi wina dzina lake Isaac Newton anafalitsa zimene anapeza zokhudza mphamvu yokoka zinthu. Iye anafotokoza kuti pali mphamvu yosaoneka imene imapangitsa kuti dziko lisacoke mu mpita wake (m’njila yake yoyendamo). Izi zinatsimikizila kuti zimene Baibo inakamba zaka zoposa 3,000 zapitazo n’zoona!

Ili na Maulosi Odalilika

Kodi maulosi a m’Baibo amakwanilitsikadi ndendende malinga na mmene analoseledwela? Ganizilani citsanzo ca ulosi wa Yesaya wokamba za kuwonongedwa kwa Babulo.

Ulosi: Ca m’ma 732 B.C.E., wolemba Baibo Yesaya anakambilatu kuti mzinda wa Babulo udzawonongedwa, ndipo mu mzindamo simudzakhalanso anthu. Anakamba izi mzinda wa Babulo usanafike pokhala likulu la ufumu wamphamvu. (Yesaya 13:17-20) Yesaya anachula ngakhale dzina la munthu amene adzagonjetsa mzindawo kuti adzakhala Koresi. Anafotokozanso na njila imene Koresi adzaseŵenzetsa mwa kukamba kuti mitsinje ‘idzauma.’ Komanso, anakambilatu kuti mageti a mzindawo adzasiyidwa otseguka.—Yesaya 44:27–45:1.

Kukwanilitsika Kwake: Patapita zaka 200 kucokela pamene Yesaya analemba ulosiwo, mfumu ya Perisiya inaukila Babulo. Kodi mfumuyo inali ndani? Inali Koresi. Popeza kuti Babulo unali mzinda wotetezeka kwambili, Koresi anaganiza zopatutsa madzi a Mtsinje wa Firate, umene unali kudutsa pakati pa mzindawo komanso kuzungulila Babulo. Asilikali ake anakumba cimfolo na kupatutsila madzi ku dambo. Izi zinapangitsa kuti madzi a mu mtsinjewo apunguke kwambili, moti asilikali a Koresi anakwanitsa kuwoloka bwino-bwino mtsinjewo umene unali m’mbali mweni-mweni mwa mpanda wa mzindawo, madzi akulekezela m’viŵelo (ena amati nchafu). Komanso n’zocititsa cidwi kuti pa nthawiyo, Ababulo anasiya mageti ali otseguka! Asilikali a Koresi analoŵa mu mzinda wa Babulo magetiwo ali otseguka na kuwononga mzindawo.

Koma mbali imodzi ya ulosi inali isanakwanilitsike. Kodi anthu analekadi kukhala mu mzinda wa Babulo? Kwa zaka mahandiledi, anthu anapitiliza kukhala mu mzindawo. Koma masiku ano, Babulo ni matongwe okha-okha. Ndipo malo amenewa ali pafupi na mzinda wa Baghdad ku Iraq. Umenewu ni umboni wotsimikizila kuti mbali zonse za ulosi wa Yesaya zinakwanilitsikadi. Inde, Baibo ni yodalilika ngakhale pa nkhani ya zimene zidzacitika kutsogolo.