Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

Anthu ambili amapemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele. Koma kodi munadzifunsapo kuti Ufumu wa Mulungu n’ciani? Nanga udzacita ciani?

ONANI ZIMENE BAIBO IMAKAMBA:

  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

    Ni boma la kumwamba limene wolamulila wake ni Yesu Khristu monga Mfumu.—Yesaya 9:6, 7; Mateyu 5:3; Luka 1:31-33.

  • Kodi Ufumu wa Mulungu udzacita ciani?

    Udzacotsapo zoipa zonse na kubweletsa mtendele wamuyaya kwa anthu padziko lapansi.—Danieli 2:44; Mateyu 6:10.

  • Kodi kufuna-funa Ufumu coyamba kumatanthauza ciani?

    Kumatanthauza kucilikiza Ufumu wa Mulungu, na kukhulupilila kuti iwo wokha ndiwo udzakonza zinthu padziko lapansi kuti zikhale mmene Mulungu amafunila.—Mateyu 6:33; 13:44.