Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mlengi Wathu Wacikondi Amasamala za Ife

Mlengi Wathu Wacikondi Amasamala za Ife

1. MLENGI WATHU AMAWALITSA DZUŴA

Kodi muganiza umoyo padziko lapansi ukanakhala bwanji popanda dzuŵa? Dzuŵa limapeleka mphamvu ku mitengo kuti itulutse masamba, maluŵa, zipatso, njele, komanso mbewu. Limapangitsanso mitengo kukoka madzi m’nthaka kupitila m’mizu n’kuwapeleka ku masamba, mpaka kufika mu mlenga-lenga monga nthunzi.

2. MLENGI WATHU AMAGWETSA MVULA

Mvula ni mphatso yamtengo wapatali yocokela kwa Mulungu imene imapangitsa kuti tikhale na cakudya. Mulungu amatipatsa mvula kucokela kumwamba na nyengo zimene zokolola zathu zimakhala zambili. Amatipatsa cakudya cokwanila komanso cimwemwe.

3. MLENGI WATHU AMATIPATSA CAKUDYA NA ZOVALA

Pafupi-fupi munthu aliyense amene ni tate amayesetsa kupezela a m’banja lake cakudya cokwanila na zovala. Onani zimene Malemba amakamba: “Onetsetsani mbalame zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga cakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?”—Mateyu 6:25, 26.

“Phunzilani pa mmene maluwa akuchile amakulila. . . . Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale [Mfumu] Solomo mu ulemelelo wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa. Tsopano ngati Mulungu amaveka cotelo zomela zakuchile . . . , kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo?”—Mateyu 6:28-30.

Popeza kuti Mulungu angatipatse cakudya na zovala, mosakaikila angatithandizenso kupeza zofunikila za mu umoyo wathu. Ngati tiyesetsa kucita cifunilo ca Mulungu, iye adzadalitsa zoyesa-yesa zathu pa kulima cakudya, kapena angatithandize kupeza nchito kuti tikwanitse kugula zimene tifunikila.—Mateyu 6:32, 33.

Kukamba zoona, tili na zifukwa zabwino zokondela Mulungu tikaganizila za dzuŵa, mvula, mbalame, komanso maluŵa. Nkhani yokonkhapo ifotokoza mmene Mlengi wathu amakambila na anthu.