Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Gwilitsilani Nchito Bwino Lilime Lanu

Gwilitsilani Nchito Bwino Lilime Lanu

‘Mau a pakamwa panga . . . akukondweletseni, inu Yehova.’—SALIMO 19:14.

NYIMBO: 82, 77

1, 2. N’cifukwa ciani Baibulo limayelekezela lilime ndi moto?

MU 1871, moto unabuka m’nkhalango ya Wisconsin, ku United States. Motowo unafalikila mwamsanga m’madela ambili ndipo unaononga mitengo pafupifupi 2 biliyoni. Motowo unaphanso anthu oposa 1,200. Palibe moto umene unapha anthu ambili ku United States kuposa moto umenewo. Zikuoneka kuti cimoto coopsaco cinayamba cifukwa ca tumalaŵi twa moto tocoka m’sitima imene inali kudutsa m’nkhalangoyo. Zimenezi zikutikumbutsa mau a m’Baibulo akuti: “Tangoganizani mmene kamoto kakang’onong’ono kamayatsila nkhalango yaikulu.” (Yakobo 3:5) N’cifukwa ciani Yakobo anakamba mau amenewa?

2 Yakobo anati: “Lilimenso ndi moto.” (Yakobo 3:6) “Lilime” likutanthauza luso lathu lokamba zinthu. Ndipo mofanana ndi moto, zimene timakamba zingabweletse mavuto aakulu. Mau athu angakhudze kwambili anthu ena. Ndiye cifukwa cake Baibulo limanena kuti zokamba zathu zili ndi mphamvu ya imfa ndi ya moyo. (Miyambo 18:21) Koma kodi zimenezi zitanthauza kuti tiyenela kukhala duu osakamba ciliconse cifukwa coopa kukamba mau oipa? Iyai. Sitingaleke kugwilitsila nchito moto cifukwa coopa kuti utishoka. M’malomwake, timaugwilitsila nchito mosamala. Mwacitsanzo, timaphikila, kuotha, ndi kuunikila. Mofananamo, ngati tikamba mosamala, timagwilitsila nchito lilime lathu kulemekeza Yehova ndi kulimbikitsa ena.—Salimo 19:14.

3. Ndi zinthu zitatu ziti zimene zingatithandize kukamba zinthu zolimbikitsa kwa ena?

3 Yehova anatipatsa luso loti tizitha kuuza anzathu maganizo athu ndi mmene tikumvela. Timacita zimenezi mwa kukamba nao kapena kucita zizindikilo ndi manja. Kodi tingagwilitsile nchito bwanji mphatso imeneyi kuti tilimbikitse ena? (Ŵelengani Yakobo 3:9, 10.) Tiyenela kudziŵa nthawi yabwino imene tiyenela kukamba, zimene tiyenela kukamba, ndi mmene tiyenela kukambila.

NTHAWI IMENE TIYENELA KUKAMBA

4. Ndi nthawi iti pamene tiyenela kukhala cete?

4 Nthawi zina ndi bwino kukhala cete. Baibulo limanena kuti pali “nthawi yokhala cete.” (Mlaliki 3:7) Mwacitsanzo, timakhala cete pamene ena akulankhula pofuna kuonetsa ulemu. (Yobu 6:24) Ndiponso sitiyenela kuulula nkhani zacinsinsi zimene ena sayenela kumva. (Miyambo 20:19) Komanso munthu wina akatikhumudwitsa, cingakhale canzelu kudziletsa osakamba ciliconse.—Salimo 4:4.

5. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila Yehova cifukwa cotipatsa mphatso ya kulankhula?

5 Koma nthawi zina ndi bwino kulankhula. (Mlaliki 3:7) Pali nthawi yotamanda Yehova, yolimbikitsa ena, yokamba maganizo athu, ndi youza ena zimene tikufuna. (Salimo 51:15) Tikamagwilitsila nchito mphatso yathu ya kulankhula mwanjila imeneyi, ndiye kuti tikuyamikila Yehova cifukwa cotipatsa mphatsoyi. Ndi mmene timacitila bwenzi lathu likatipatsa mphatso yabwino. Timayesetsa kuigwilitsila nchito bwino.

6. N’cifukwa ciani tiyenela kusankha nthawi yabwino yokamba zinthu?

6 N’cifukwa ciani tifunika kusankha nthawi yabwino yokamba zinthu? Lemba la Miyambo 25:11 limati: “Mau olankhulidwa pa nthawi yoyenela ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” Maapozi agolide amaoneka okongola, koma amaoneka okongola kwambili akakhala m’mbale ya siliva. Mofanana ndi zimenezi, tingakhale ndi zinazake zabwino zimene tifuna kuuza munthu. Koma tiyenela kusankha nthawi yabwino yomuuzila zinthuzo kuti apindule kwambili. Kodi tingacite bwanji zimenezi?

7, 8. Kodi abale athu a ku Japan anatengela bwanji citsanzo ca Yesu?

7 Ngati takamba zinthu panthawi yolakwika, anthu sangamvetsetse zimene takamba kapena kuzivomeleza. (Ŵelengani Miyambo 15:23.) Mwacitsanzo, mu March 2011, civomezi ndi tsunami zinaononga matauni ambili kum’maŵa kwa dziko la Japan. Anthu oposa 15,000 anafa. Acibale ndi mabwenzi ena a Mboni za Yehova anafa. Ngakhale n’conco, io anali kufuna kutonthoza anzao amene anakhudzidwa ndi ngoziyo mwa kuwauza uthenga wa m’Baibulo. Koma anadziŵa kuti ambili mwa anthuwo ndi Abuda ndipo sadziŵa kwenikweni zimene Baibulo limanena. Conco, m’malo mowauza za ciukililo pa nthawi imeneyo, abale anangowatonthoza ndi kuwafotokozela cifukwa cake anthu abwino naonso amavutika.

8 Abale amenewo anatengela citsanzo ca Yesu. Yesu anali kudziŵa nthawi yoyenela kukhala cete ndi nthawi yoyenela kulankhula. (Yohane 18:33-37; 19:8-11) Iye anali kuyembekezela nthawi yabwino kuti afotokozele ophunzila ake zinthu zina. (Yohane 16:12) Naonso abale a ku Japan anayembekeza nthawi yabwino youza anthu za ciukililo. Patapita zaka ziŵili ndi hafu kucokela pamene kunacitika tsunami, io anagaŵila kapepala kauthenga ka mutu wakuti Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo? Anthu ambili analandila kapepalako ndipo analimbikitsidwa ndi zimene anaŵelenga. Ifenso tiyenela kuganizila cikhalidwe ndi zikhulupililo za anthu a m’gawo lathu kuti tidziŵe nthawi yabwino yokamba nao.

Tiyenela kukhala oleza mtima ndi kukamba ndi anthu panthawi imene angamvetsele

9. Ndi pa zocitika zina ziti pamene tiyenela kusankha nthawi yabwino yokamba?

9 Ndi pa zocitika zina ziti pamene tiyenela kusankha nthawi yabwino yolankhula? Nthawi zina munthu angakambe zinthu zotikhumudwitsa. M’malo momuyankha mosaganizila bwino, coyamba tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi wacitila dala zimenezi? Kodi ndikambilane naye za nkhaniyi?’ Nthawi zambili ndi bwino kungokhala cete. Koma ngati mwaona kuti pali cifukwa comveka cokambila naye, muyenela kuyembekezela mpaka mtima wanu utakhala pansi. (Ŵelengani Miyambo 15:28.) Ndiponso ngati mufuna kuthandiza abale anu amene si Mboni kuti adziŵe Yehova, mufunika kucita zinthu moleza mtima. Mufunika kuganizila mosamala zimene mufuna kukamba, ndi kupeza nthawi yabwino yokamba nao.

ZIMENE TIYENELA KUKAMBA

10. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kusankha bwino mau okamba? (b) Kodi tiyenela kupewa kakambidwe kotani?

10 Zimene timakamba zingasangalatse ena kapena kuwakhumudwitsa. (Ŵelengani Miyambo 12:18.) Anthu ambili m’dziko la Satanali amakamba “mau owawa” amene ali ngati “mivi” kapena “lupanga” pofuna kukhaulitsa anzao kapena kuwakhumudwitsa. (Salimo 64:3) Ambili amaphunzila kukamba mwanjila imeneyi cifukwa coonelela mafilimu kapena mapulogalamu ena a pa TV. Koma Akristu sayenela kukamba mau aukali kapena oipa, ngakhale moseka cabe. Nthabwala ndi zabwino ndipo zimakometsa nkhani. Koma sitiyenela kunyodola ena, kuwacititsa manyazi, kapena kuwatukwana pofuna kuseketsa anzathu. Baibulo limalangiza Akristu kuti sayenela kukamba “mau acipongwe.” Limati: “Mau alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikile, kuti asangalatse owamva.”—Aefeso 4:29, 31.

11. N’ciani cingatithandize kusankha mau abwino pokambilana ndi anthu?

11 Yesu anakamba kuti “pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima.” (Mateyu 12:34) Izi zitanthauza kuti zimene timakamba zimaonetsa zimene zili mumtima mwathu. Ngati timakonda anthu ndi kuwaganizila, timasankha bwino mau pokambilana nao. Ndipo zimene tingakambe zingawalimbikitse.

12. Ndi zinthu zina ziti zimene zingatithandize kusankha mau abwino?

12 Pamafunika khama kuti tipeze mau abwino amene tingakambe. Ngakhale kuti Solomo anali Mfumu yanzelu, “anali kusinkhasinkha ndi kufufuza zinthu mosamala” n’colinga cakuti zolemba zake zikhale zolondola ndi zosangalatsa. (Mlaliki 12:9, 10) N’ciani cingatithandize kudziŵa mau abwino? Tiyenela kufufuza m’Baibulo ndi m’zofalitsa zathu kuti tipeze mau abwino amene tingakambe. Tingaphunzilenso matanthauzo a mau ena amene sitiwadziŵa bwino. Ndiponso tiyenela kuphunzila mmene Yesu anali kukambila ndi anthu kuti nafenso tizitha kukamba mau olimbikitsa ena. Iye anali kudziŵa bwino zoyenela kukamba cifukwa cakuti Yehova anamuphunzitsa ‘mmene angayankhile munthu wotopa.’ (Yesaya 50:4) Tiyenelanso kuganizila mmene mau athu angakhudzile ena. (Yakobo 1:19) Tisanakambe ndi munthu, tingadzifunse kuti: ‘Kodi iye angamvetsetse zimene ndifuna kukamba? Nanga zingamukhudze bwanji?’

13. N’cifukwa ciani tiyenela kukamba momveka bwino?

13 Aisiraeli anali kuliza lipenga pofuna kupeleka uthenga. Panali mamvekedwe a lipenga amene anali kusonyeza kuti anthu afunika kusonkhana pamodzi. Ndipo mamvekedwe ena anali kusonyeza kuti asilikali afunika kumenya nkhondo. Kodi muganiza kuti n’ciani cikanacitikila asilikali ngati mamvekedwe a lipenga sanadziŵike bwino? Baibulo limayelekezela mamvekedwe odziŵika bwino a lipenga ndi mau osavuta kumva. Ngati sitinafotokoze zinthu momveka bwino, anthu sangamvetsetse kapena angakhulupilile zinthu zabodza. Tifunika kukamba zinthu momveka bwino, koma tiyenela kupewa kukamba mwamwano kapena mopanda ulemu.—Ŵelengani 1 Akorinto 14:8, 9.

14. Ndi citsanzo citi cimene cionetsa kuti Yesu anali kukamba m’njila yosavuta kumva?

14 Pa Mateyu caputala 5 mpaka 7, Yesu anagwilitsila nchito mau omveka bwino kwambili. M’nkhani imeneyi, iye sanakambe mau ozama kapena osafunika kwenikweni pofuna kugometsa anthu. Komanso sanakambe zinthu zimene zikanakhumudwitsa ena. Yesu anaphunzitsa anthu zinthu zofunika kwambili ndiponso zozama, koma anagwilitsila nchito mau osavuta kumva. Mwacitsanzo, iye anafotokoza mmene Yehova amadyetsela mbalame pofuna kutsimikizila ophunzila ake kuti sayenela kuda nkhawa kuti adzadya ciani. Kenako anawafunsa kuti: “Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?” (Mateyu 6:26) Ndi mau amenewa, Yesu analimbikitsa ophunzila ake ndi kuwathandiza kumvetsetsa mfundo yofunika kwambili.

MMENE TIYENELA KUKAMBILA NDI ANTHU

15. N’cifukwa ciani tifunika kukamba mokoma mtima?

15 Tifunikanso kukhala osamala ndi zimene timakamba ndiponso mmene timakambila ndi ena. Anthu anali kukonda kumvetsela zokamba za Yesu cifukwa cakuti anali kulankhula ‘mogwila mtima,’ ndi mokoma mtima. (Luka 4:22) Tikamakamba mokoma mtima ndi anthu, io angamvetsele zonena zathu ndi kuzikhulupilila. (Miyambo 25:15) Ngati timalemekeza anthu ndi kuwaganizila, cimakhala cosavuta kukamba nao mokoma mtima. Izi n’zimene Yesu anali kucita. Mwacitsanzo, ataona anthu ambili akumulondola kuti amve mau ake, anapatula nthawi yokhala nao ndi kuwaphunzitsa. (Maliko 6:34) Ngakhale pamene anthu anali kumunenela zacipongwe, Yesu sanabwezele zacipongwe.—1 Petulo 2:23.

16, 17. (a) Tikamakamba ndi acibale kapena anzathu, kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) N’ciani cinacitika mai wina atayankha mnzake mokoma mtima?

16 Ngakhale kuti acibale ndi mabwenzi athu timawakonda, nthawi zina tingawalankhule mau okhumudwitsa. Cifukwa cakuti timawadziŵa bwino, mwina tingaganize kuti sangakhumudwe ngakhale titakamba nao mosasamala. Koma Yesu nthawi zonse anali kukamba mokoma mtima ndi mabwenzi ake. Pamene ena mwa ophunzila ake anali kukangana kuti wamkulu ndani, iye anawalangiza mokoma mtima ndipo anawauza citsanzo ca mwana wang’ono pofuna kuwaongolela. (Maliko 9:33-37) Akulu angatengele citsanzo ca Yesu mwa kulangiza ena mokoma mtima.—Agalatiya 6:1.

17 Ngati munthu wina wakamba mau oipa amene atikhumudwitsa, tingacite bwino kukamba naye mokoma mtima. (Miyambo 15:1) Mwacitsanzo, mnyamata wina amene anali kuleledwa ndi amai ake a Mboni anali kucita zoipa kwinaku akutumikila Yehova. Mlongo wina wa mumpingo mwao anamvela cifundo amai a mnyamatayo ndipo anawauza kuti: “N’zomvetsa cisoni kuti mwalephela kuphunzitsa mwana wanu.” Asanayankhe, amaiwo anayamba aganiza, kenako anakamba kuti: “N’zoona kuti mwanayu sakundimvela, koma ndikali kumuphunzitsa. Tiyeni tiyembekezele. Mwina adzasintha ndi kupulumuka Aramagedo.” Popeza kuti amai a mnyamatayo anayankha modekha ndi mokoma mtima, alongowo anakhalabe mabwenzi. Mnyamatayo atamva zimene amai ake anakamba, anadziŵa kuti anali kukhulupililabe kuti angathe kusintha. Conco, analeka kugwilizana ndi anzake oipa, kenako anabatizidwa, ndipo pambuyo pake anatumikila pa Beteli. Kaya tikukambilana ndi Akristu anzathu, acibale athu, kapena anthu amene sitiwadziŵa, nthawi zonse mau athu ayenela kukhala ‘acisomo, okoma ngati kuti tawathila mcele.’—Akolose 4:6.

18. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu pokamba ndi anthu?

18 Luso limene tili nalo lotha kuuza ena maganizo athu ndi mmene tikumvela ndi mphatso yapadela yocokela kwa Yehova. Mofanana ndi Yesu, tiyenela kusankha nthawi yabwino yokamba zinthu, kusankha bwino zokamba, ndi kuyesetsa kukamba mokoma mtima nthawi zonse. Conco, tiyeni tizikamba mau olimbikitsa kwa ena. Tikatelo, Yehova adzasangalala.