Onani zimene zilipo

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupemphela M’dzina la Yesu?

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupemphela M’dzina la Yesu?

NTHAWI zambili Yesu anali kuphunzitsa za kupemphela. M’masiku ake, atsogoleli acipembedzo aciyuda anali kupemphela “m’mphambano za misewu ikulu-ikulu.” N’cifukwa ciani anali kucita zimenezi? Anali kufuna kuti “anthu aziwaona.” Ndithudi, iwo anali kufuna kudzionetsela kuti anali anthu opemphela kwambili. Ambili a iwo anali kupemphela mapemphelo atali-atali, obweleza-bweleza, ngati kuti “mawu ambili-mbili” ni amene amapangitsa mapemphelo kumvedwa. (Mateyo 6:5-8) Yesu ananena poyela kuti khalidwe limeneli n’losafunika, cotelo anaphunzitsa anthu oona mtima kuti apewe zimenezi popemphela. Komabe, sikuti anangowaphunzitsa zoti apewe popemphela basi.

Yesu anaphunzitsa kuti mapemphelo athu ayenela kusonyeza kuti tikufunitsitsa kuti dzina la Mulungu liyeletsedwe, Ufumu Wake ubwele ndiponso kuti cifunilo Cake cicitike. Iye anaphunzitsanso kuti n’kofunika kupempha Mulungu kuti atithandize pa zinthu zokhudza moyo wathu. (Mateyo 6:9-13; Luka 11:2-4) Yesu anagwilitsa nchito fanizo posonyeza kuti popemphela tifunika kulimbikila, kukhala na cikhulupililo ndiponso kudzicepetsa ngati tikufuna kuti mapemphelo athu amvedwe. (Luka 11:5-13; 18:1-14) Ndipo Yesu popemphela anasonyeza bwino kwambili zimene anali kuphunzitsazo.—Mateyo 14:23; Maliko 1:35.

Sitikukayikila kuti malangizo amenewa anawathandiza ophunzila a Yesu kuti mapemphelo awo akhale abwino. Komabe, Yesu anadikila mpaka usiku wake womaliza padziko lino lapansi kuti aphunzitse ophunzila ake zinthu zofunika kwambili popemphela.

“Pamene Panasinthila Zinthu Pankhani ya Pemphelo”

Yesu anathela nthawi yoculuka usiku wake womaliza padziko lapansi akulimbikitsa atumwi ake okhulupilika. Imeneyi inali nthawi yoyenela kuwauza kanthu kena katsopano. Yesu anati: “Ine ndine njila ndi coonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.” Kenako anawalonjeza zinthu zolimbikitsa izi: “Ciliconse cimene mudzapempha m’dzina langa, ndidzacita cimeneco, kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana wake. Ngati mupempha ciliconse m’dzina langa, ndidzacita cimeneco.” Atatsala pang’ono kumaliza kukambilanako, iye anati: “Kufikila nthawi ino simunapemphepo ciliconse m’dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandila, kuti cimwemwe canu cisefukile.”—Yohane 14:6, 13, 14; 16:24.

Mawu amenewa anali ofunika kwambili. Buku lina lotanthauzila mawu a m’Baibo limati “pamenepa m’pamene panasinthila zinthu pankhani ya pemphelo.” Yesu sanatanthauze kuti anthu asiye kupemphela kwa Mulungu n’kumapemphela kwa iye. M’malo mwake, iye anali kuwasonyeza njila yatsopano yopemphelela kwa Yehova Mulungu.

Kunena zoona Mulungu nthawi zonse amamvetsela mapemphelo a atumiki ake okhulupilika. (1 Samueli 1:9-19; Salmo 65:2) Komabe, kuyambila nthawi imene Mulungu anacita pangano na Aisiraeli, anthu amene anali kufuna kuti Mulungu amve mapemphelo awo anayenela kuvomeleza kuti Aisiraeli anali mtundu wosankhidwa na Mulungu. Kenako, kuyambila nthawi ya Solomo, anafunika kuvomeleza kuti kacisi anali malo amene Mulungu anawasankha kupelekelako nsembe. (Deuteronomo 9:29; 2 Mbiri 6:32, 33) Komabe, kulambila mu njila imeneyi kunali kwa kanthawi. Malinga n’kunena kwa mtumwi Paulo, Cilamulo cimene cinapelekedwa kwa Aisiraeli ndiponso nsembe zimene anali kupeleka pa kacisi zinali “mthunzi cabe wa zinthu zabwino zimene zikubwela, osati kuti [cinali] na zinthu zenizenizo.” (Aheberi 10:1, 2) Mthunziwu unafunika kulowedwa m’malo na zinthu zenizeni. (Akolose 2:17) Kuyambila mu 33 C.E., kuti munthu akhale paubwenzi na Yehova sizinadalilenso kutsatila Cilamulo ca Mose koma zimadalila kumvela Khristu Yesu, popeza Cilamuloco cinali kutsogolela anthu kwa Khristu Yesu.—Yohane 15:14-16; Agalatiya 3:24, 25.

Dzina “Loposa Lina Lililonse”

Yesu anakhazikitsa njila yapadela kwambili yopemphelela kwa Yehova. Ndipo anazichula kuti ni bwenzi lamphamvu, limene limatsegula njila kuti Mulungu amve na kuyankha mapemphelo athu. Kodi n’ciani cimam’pangitsa Yesu kuticitila zimenezi?

Popeza tonsefe tinabadwa ocimwa, zimene timacita ndiponso nsembe zimene timapeleka sizingacotse macimo amenewa kapena kutipangitsa kukhala paubwenzi na Mulungu wathu woyela, Yehova. (Aroma 3:20, 24; Aheberi 1:3, 4) Komatu, Yesu anapeleka moyo wake wangwilo kuwombola anthu amene angafune kukhala paubwenzi na Mulungu. (Aroma 5:12, 18, 19) Conco anthu onse amene akufuna kuti macimo awo akhululukidwe ali na mwayi wokhala paubwenzi wabwino na Yehova ndiponso kusangalala na ‘ufulu wa kulankhula’ na Mulungu. Koma izi n’zotheka pokha-pokha ngati munthu amasonyeza cikhulupililo mu nsembe ya Yesu ndiponso ngati amapemphela m’dzina lake.—Aefeso 3:11, 12.

Tikamapemphela m’dzina la Yesu timakhala tikusonyeza cikhulupililo coti iye amakwanilitsa cifunilo ca Mulungu m’njila zitatu izi: (1) Iye ni “Mwanawankhosa wa Mulungu,” amene nsembe yake imacititsa kuti macimo athu akhululukidwe. (2) Anaukitsidwa na Yehova ndipo tsopano ni “mkulu wa ansembe” amene akutithandiza kuti tipindule na dipo. (3) Ndiye yekha amene ali “njila” yofikila kwa Yehova m’pemphelo.—Yohane 1:29; 14:6; Aheberi 4:14, 15.

Tikamapemphela m’dzina la Yesu timasonyeza kuti timamulemekeza. Iye ayeneladi kulemekezedwa popeza cifunilo ca Yehova n’cakuti “m’dzina la Yesu, onse apinde maondo awo, . . . aliyense avomeleze poyela ndi lilime lake kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.” (Afilipi 2:10, 11) Komabe, cofunika kwambili tikamapemphela m’dzina la Yesu n’cakuti timalemekeza Yehova, amene anapeleka Mwana wake kuti zinthu zitiyendele bwino.—Yohane 3:16.

Pofuna kuti timvetse kukula kwa udindo wa Yesu, Baibo imagwilitsa nchito mawu osiyana-siyana omulemekezela.

Usakhale Mwambo Cabe

Inde, tiyenela kupemphela m’dzina la Yesu ngati tikufuna kuti Yehova amve mapemphelo athuwo. (Yohane 14:13, 14) Koma sitikufuna kuti tizibweleza mawu akuti “m’dzina la Yesu” cifukwa cakuti tinazolowela. Cifukwa ciani?

Taonani citsanzo ici. Mukalandila kalata, kaŵili-kaŵili imatha na mawu akuti “nditha ine wanu.” Kodi mukuganiza kuti mawu amenewa amasonyeza maganizo a munthu wolemba kalatayo, kapena wangolemba cifukwa coti anthu anazolowela kulemba mawu amenewa? Zoonadi, tizigwilitsa nchito dzina la Yesu popemphela mwatanthauzo osati ngati mawu akumapeto kwa kalata aja. Ngakhale kuti tifunika ‘kupemphela mosalekeza,’ ticite zimenezi ‘ndi mtima wathu wonse,’ osati mwamwambo cabe.—1 Atesalonika 5:17; Salmo 119:145.

Kodi inuyo mungapewe bwanji kugwilitsa nchito mawu akuti “m’dzina la Yesu” mwamwambo cabe? Bwanji osaganizila kaye makhalidwe abwino a Yesu? Ganizilani zimene wakucitilani kale na zimene akufuna kukucitilani. Popemphela, yamikilani Yehova na kum’tamanda cifukwa ca mmene wagwilitsila nchito Mwana wake. Mukacita zimenezi, mudzaona kuti lonjezo la Yesu ili n’lodalilika kwambili: “Ngati mupempha ciliconse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.”—Yohane 16:23.

Tizipemphela na mtima wathu wonse, osati mwamwambo cabe