Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | KODI IMFA NDI MAPETO A ZONSE?

Zimene Anthu Acita Pofuna Kugonjetsa Imfa

Zimene Anthu Acita Pofuna Kugonjetsa Imfa

EMPEROR QIN SHI HUANG

EXPLORER PONCE DE LEÓN

Imfa ndi mdani woopsa kwambili. Timayesetsa kulimbana nayo ndi mphamvu zathu zonse. Timalephela kukhulupilila ngati amene wamwalila ndi wokondedwa wathu. Ndipo pamene tikali acinyamata amphamvu, timaganiza kuti mdani wathu ameneyu sangatifikile. Timakhala ndi maganizo amenewa kwa nthaŵi yaitali.

Afarao akale a ku Iguputo anayesetsa kwambili kufuna-funa njila yakuti azikhala ndi moyo wosafa. Iwo anagwilitsila nchito nthawi yaitali ya moyo wao ndi anchito ao masauzande ambili poyesa-yesa kulimbana ndi imfa. Mapilamidi amene io anamanga amapeleka umboni wakuti anali kufuna-funa moyo wosafa koma analephela.

Mafumu a ku China naonso anafuna-funa moyo wosafa ngakhale kuti anagwilitsila nchito njila ina. Iwo anali kugwilitsila nchito mankhwala amene anali kuganiza kuti ndi mankhwala a moyo. Mfumu Qin Shi Huang anafuna kuti akatswili asayansi apeze mankhwala amene angacititse kuti iye asafe. Koma msakanizo wamankhwala amene anakonza unali ndi poizoni inayake, ndipo zikuoneka kuti msakanizo monga umenewu ndi umene unamupha.

Mu 1513 C.E., wofufuza malo wina wa ku Spain, Juan Ponce de León anayenda ulendo wa panyanja m’zilumba za Caribbean n’colinga cofufuza mankhwala a moyo ochedwa kasupe wa unyamata. Ali paulendo umenewu anapeza dziko la Florida, U.S.A., ndipo anamwalila patapita zaka zocepa atamenyana ndi mbadwa za ku America. Kunena zoona palibe amene anapezapo mankhwala a moyo.

Afarao a ku Iguputo, mafumu, ndi ofufuza malo, onsewa anali kufuna kugonjetsa imfa. Ngakhale kuti sitingakonde njila zimene anagwilitsila nchito, palibe amene angasulize colinga cao. Zoonadi n’zakuti palibe aliyense amene amafuna kufa.

KODI IMFA INGAGONJETSEDWE?

N’cifukwa ciani timadana ndi imfa? Baibo imafotokoza cifukwa cake. Ponena za Mlengi wathu, Yehova Mulungu, a Baibo imati: “Ciliconse iye anacipanga cokongola pa nthawi yake. Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kale-kale.” (Mlaliki 3:11) Timafuna kusangalala ndi moyo padziko lapansi lokongola kosatha, osati cabe kwa zaka 80 kapena kuposelapo. (Salimo 90:10) Zimenezo n’zimene mtima wathu umalaka-laka.

N’cifukwa ciani Mulungu anatipatsa mtima wofuna kukhala ndi moyo “mpaka kale-kale”? Kodi anacita zimenezi n’colinga cofuna kutigwilitsa mwala? Iyai. Mulungu sangacite zimenezo. Iye amatilonjeza kuti imfa idzagonjetsedwa. Kaŵili-kaŵili Baibo imakamba kuti Mulungu adzacotsa imfa ndi kubweletsa moyo wosatha.—Onani bokosi lakuti,  “Kugonjetsa Imfa,” m’nkhani ino.

Yesu Kristu ananena momveka bwino kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Kristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Conco, n’zotheka kugonjetsa imfa. Koma Yesu ananena kuti ndi Mulungu yekha amene adzagonjetsa imfa.

a Yehova ndi dzina la Mulungu monga mmene lalembedwela m’Baibo.