Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | MUNGACITE CIANI KUTI MUZISANGALALA NDI NCHITO YANU?

Mungacite Ciani Kuti Muzisangalala Ngati Mumagwila Nchito Yolimba?

Mungacite Ciani Kuti Muzisangalala Ngati Mumagwila Nchito Yolimba?

Baibulo limati: “Munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, cifukwa coti wagwila nchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yocokela kwa Mulungu.” (Mlaliki 3:13) Popeza kuti Mulungu amafuna kuti tizisangalala pa nchito, iye amatiuza zimene zingatithandize kukhala osangalala ndi nchito yathu. (Yesaya 48:17) Iye amatiuza zimenezi kudzela m’Mau ake, Baibulo. Tsopano onani malangizo awa ocokela m’Baibulo amene angakuthandizeni kukhala wosangalala ndi nchito yanu.

KHALANI NDI MAGANIZO OYENELA PA NCHITO

Kaya mumagwila nchito ya muofesi, yamanja, kapena nchito zina, dziŵani kuti “kugwila nchito iliyonse kumapindulitsa.” (Miyambo 14:23) Kodi kumapindulitsa bwanji? Coyamba, kugwila nchito mwakhama kumatithandiza kupeza zofunikila pa umoyo. N’zoona kuti Mulungu analonjeza kuti adzapatsa atumiki ake okhulupilika zinthu zofunikila pa umoyo wao. (Mateyu 6:31, 32) Komabe, iye amatiyembekezela kucita mbali yathu mwa kugwila nchito mwakhama kuti tipeze zosowa zathu.—2 Atesalonika 3:10.

Conco, tiyenela kuona nchito yathu monga njila yabwino yotithandiza kukwanilitsa zolinga zathu ndi udindo wathu. Joshua, amene ali ndi zaka 25, anati: “Kudzipezela zinthu zofunikila pa umoyo n’kofunika. Ngati nchito yanu imakuthandizani kupeza ndalama zogulila zinthu zofunika, ndiye kuti ndi yabwino.”

Komanso kugwila nchito mwakhama kumathandiza munthu kuti azidziona kuti ndi wofunika. N’zoona kuti kugwila nchito yolemetsa si kopepuka. Koma ngati timayesetsa kugwila nchito yathu mwakhama, ngakhale ioneke yosasangalatsa kapena yovuta, timakhala osangalala cifukwa codziŵa kuti tacita zamphamvu. Timadziŵanso kuti sindife aulesi. (Miyambo 26:14) Mwanjila imeneyi, nchito imathandiza munthu kukhala wosangalala. Aaron, amene tamuchula m’nkhani yapita, anati: “Ndimakhala wosangalala pambuyo pogwila nchito kwa maola ambili patsiku. Nthawi zina ndimatopa kwambili, ndipo anthu sangadziŵe nchito imene ndagwila, koma ndimadziŵa kuti ndacita zinthu zofunika.”

KHALANI WODZIPELEKA PA NCHITO YANU

Baibulo limatamanda mwamuna amene ndi “waluso pa nchito yake” ndiponso mkazi amene “manja ake amagwila nchito iliyonse mosangalala.” (Miyambo 22:29; 31:13) Koma pamafunika khama kuti munthu akhale ndi luso panchito. Ndipo ndi anthu ocepa amene amasangalala kugwila nchito imene saidziŵa bwino. Zioneka kuti anthu ambili sasangalala ndi nchito yao cifukwa cakuti sacita khama kuti aidziŵe bwino nchitoyo.

Kunena zoona, munthu angasangalale ndi nchito iliyonse malinga ngati amaiona moyenela, kutanthauza kuti ngati amayesetsa kuiphunzila n’colinga cakuti aidziŵe bwino. William, mnyamata wa zaka 24, anati: “Munthu akagwila nchito mwaluso ndi kuona zotsatila zake zabwino, amakhala wosangalala. Koma ngati amangocita zinthu mwacidule panchito kapena kugwilako pang’ono cabe, sakhala wosangalala.”

MUZIGANIZILA MMENE NCHITO YANU IMAPINDULITSILA ENA

Pewani kuganizila cabe za ndalama zimene mumapeza cifukwa cogwila nchitoyo. M’malo mwake, dzifunseni kuti: ‘N’cifukwa ciani nchito imeneyi ndi yofunika? N’ciani cingacitike ngati sindinagwile nchitoyi kapena ngati sindinaigwile moyenela? Kodi nchito yanga imapindulitsa bwanji anthu ena?’

Kuganizila funso lomalizali n’kothandiza kwambili cifukwa cakuti munthu amasangalala kwambili ndi nchito yake ngati akuona kuti ikupindulitsa anthu ena. Yesu anati: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Machitidwe 20:35) Tikamagwila nchito, pali anthu amene amapindula monga makasitomala ndiponso anthu amene anatilemba nchito. Kuonjezela pamenepa, palinso anthu ena amene amapindula ndi nchito imene timagwila. Anthu amenewa ndi a m’banja lathu ndiponso anthu ena ovutika.

Anthu a m’banja lathu. Mwamuna amene amagwila nchito mwamphamvu kuti asamalile banja lake amathandiza anthu a m’banjalo m’njila ziŵili. Coyamba, amawapezela zinthu zofunika monga cakudya, zovala, ndi malo ogona. Mwanjila imeneyi, iye amakwanilitsa udindo wake wocokela kwa Mulungu wosamalila “anthu amene ndi udindo wake kuwasamalila.” (1 Timoteyo 5:8) Caciŵili, munthu amene amasamalila banja lake mwakhama amathandiza a m’banja lake kuona kuti kugwila nchito mwamphamvu n’kofunika. Shane, amene tamuchula m’nkhani yapita, anati: “Atate anga ndi munthu wolimbikila nchito kwambili. Iwo ndi munthu woona mtima amene wakhala akugwila nchito mwamphamvu nthawi zonse, ndipo nchito imene agwila kwa nthawi yaitali ndi ya ukalipentala. Cifukwa ca citsanzo cao, ndaphunzila kuti ndiyenela kugwila nchito mwamphamvu kuti ndicite zinthu zimene zingathandize ena.”

Anthu ena ovutika. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake ‘kugwila nchito molimbikila . . . kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.’ (Aefeso 4:28) Kunena zoona, ngati tigwila nchito mwamphamvu timapeza zosowa zathu ndi za banja lathu, ndipo tingathandizenso anthu ena ovutika. (Miyambo 3:27) Conco kugwila nchito mwamphamvu kungatithandize kukhala wosangalala kwambili ngati timathandizanso ena.

MUZIGWILA NCHITO MOFUNITSITSA

Pa ulaliki wake wochuka wa pa phiri, Yesu anati: “Winawake waudindo akakulamula kuti umunyamulile katundu mtunda wa kilomita imodzi, umunyamulile mtunda wa makilomita aŵili.” (Mateyu 5:41) Kodi mungagwilitsile nchito bwanji mfundo imeneyi pa nchito yanu? M’malo mocita zimene akuuzani cabe, muzicita zambili kuposa pamenepo. Khalani ndi colinga cogwila nchitoyo mwaluso ndiponso mwamsanga kwambili. Muzisangalala ndi nchito iliyonse imene mumagwila ngakhale ndi yaing’ono.

Mukamagwila nchito mofunitsitsa, mumakhala acimwemwe pa nchito yanu. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti mumacita zimenezo mwa kufuna kwanu osati cifukwa cakuti munthu wina wakukakamizani. (Filimoni 14) Zimenezi zikutikumbutsa mfundo ya pa Miyambo 12:24, imene imati: “Dzanja la anthu akhama n’limene lidzalamulile, koma dzanja laulesi lidzagwila nchito yaukapolo.” N’zoona kuti ambili a ife sindife akapolo ndipo sitigwila nchito yaukapolo. Ngakhale ndi conco, munthu amene safuna kugwila nchito yambili amakhala ngati kapolo cifukwa cakuti amacita zinthu mokakamizika. Koma amene amagwila nchito yoculuka mwa kufuna kwake, amakhala womasuka cifukwa amacita kusankha yekha kugwila nchitoyo.

MUZIGWILA NCHITO PAMLINGO WOYENELA

Kugwila nchito mwamphamvu n’kofunika, koma sitiyenela kuiwala kuti pali zinthu zina zofunika kwambili pa umoyo kuposa nchito. Ndithudi, Baibulo limatilimbikitsa kugwila nchito mwakhama. (Miyambo 13:4) Koma silitimbikitsa kugwila nchito monyanyila. Lemba la Mlaliki 4:6 limati: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwila nchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” Kodi lembali limatanthauza ciani? Limatanthauza kuti munthu amene amagwila nchito popanda kupuma sasangalala ndi nchito yake cifukwa cakuti amatopa kwambili. Conco, nchito yake imakhala yopanda phindu mofanana ndi “kuthamangitsa mphepo.”

Baibulo lingatithandize kuona nchito moyenela. Ngakhale kuti Baibulo limatilimbikitsa kugwila nchito modzipeleka, limanenanso kuti tifunika “kutsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Kodi zinthu zofunika kwambili ndi ziti? Zinthu zimenezi zimaphatikizapo kuceza ndi banja lathu ndiponso mabwenzi athu. Koma zofunika kuposa zonse ndi zinthu za kuuzimu, monga kuŵelenga Mau a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha.

Anthu amene amagwila nchito pamlingo woyenela amasangalala ndi nchito yao. William, amene tamuchula m’nkhani yapita, anati: “Munthu amene ndinali kumuseŵenzela kale amagwila nchito pamlingo woyenela. Iye amagwila nchito mwakhama, ndipo anthu amamukonda cifukwa cakuti amagwila nchito mwaluso. Koma akamaliza nchito yake, amaweluka ndi kupita kunyumba kukakhala ndi banja lake ndi kucita zinthu za kuuzimu. Ndipo iye ndi mmodzi mwa anthu osangalala kwambili.”