Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupilila Ciani?
Mboni za Yehova zimakhulupilila kuti “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Timoteyo 3:16) Baibulo limatithandiza kudziŵa zambili zokhudza Mlengi komanso kuti tikhale ndi umoyo wabwino.
Baibulo limati: “Kuti anthu adziŵe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulila dziko lonse lapansi.” (Salimo 83:18) Conco, timalambila Yehova Mulungu yekha ndipo monga Mboni zake, timauzako ena za dzina lake.—Yesaya 43:10-12.
Monga Akristu, timakhulupilila kuti Yesu, “Mwana wa Mulungu” * anabwela padziko lapansi n’kukhala Mesiya. (Yohane 1:34, 41; 4:25, 26) Yesu ataphedwa, anaukitsidwa n’kupita kumwamba. (1 Akorinto 15:3, 4) Patapita nthawi anakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 11:15) Ufumu umenewo ndi boma lenileni limene lidzabwezeletsa Paradaiso padziko lapansi. (Danieli 2:44) Baibulo limati: “Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, Ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—Salimo 37:11, 29.
“Akamaŵelenga Baibulo amakhulupilila kuti Mulungu akulankhula nao. Akakumana ndi mavuto amafufuza m’Mau a Mulungu kuti apeze njila yothetsela mavutowo. . . . Kwa io Mau a Mulungu ndi amphamvu.”—Anatelo Benjamin Cherayath, Papa wa chalichi ca katolika m’nyuzipepala ya Münsterländische Volkszeitung ya ku Germany
Mboni za Yehova zimakhulupilila kuti mfundo za m’Baibulo n’zopindulitsa. (Yesaya 48:17, 18) Conco, timatsatila kwambili mfundo zimenezo. Mwacitsanzo, Baibulo limaticenjeza pa zinthu zimene zingaononge maganizo ndi matupi athu. Conco, timapewa kukoka fodya kapena kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza bongo. (2 Akorinto 7:1) Timapewanso zinthu zimene Baibulo limaletsa, monga kuledzela, ciwelewele, ndi kuba.—1 Akorinto 6:9-11.
^ par. 4 Baibulo limacha Yesu kuti “Mwana wobadwa yekha wa Mulungu” cifukwa analengedwa mwacindunji ndi Yehova.—Yohane 3:18; Akolose 1:13-15.