Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pemphani Thandizo Kuti Mumvetsetse Baibulo

Pemphani Thandizo Kuti Mumvetsetse Baibulo

Yelekezani kuti mwapita kukaceza kudziko lacilendo kwa nthawi yoyamba. Ndiyeno, kumeneko mwapeza anthu, zikhalidwe, zakudya, ndi ndalama zimene inu simunazionepo. Mosakaikila, mungakhumudwe kwambili.

Mungamve cimodzimodzi pamene muŵelenga Baibulo kwa nthawi yoyamba. Mukamaliŵelenga, limakubwezani kumbuyo kudziko lakale limene lingaoneke ngati lacilendo kwa inu. Kudzikolo, mwapezako anthu ochedwa Afilisiti, zikhalidwe zacilendo monga ‘kung’amba zovala,’ cakudya cochedwa mana, ndi ndalama yodziŵika kuti dalakima. (Ekisodo 16:31; Yoswa 13:2; 2 Samueli 3:31; Luka 15:9) Zinthu zimenezi zingakhale zosamvetsetseka kwa inu. Mofanana ndi mmene zingakhalile mukapita kudziko lacilendo, mosakaikila inunso mungayamikile kwambili munthu wina atafotokozelani zinthu zina ndi zina za m’Baibulo.

THANDIZO LIMENE LINALIPO M’NTHAWI YAKALE

Kucokela mu 1500 B.C.E., pamene malemba opatulika anayamba kulembedwa, thandizo lakhala likupelekedwa n’colinga cakuti anthu amvetsetse malemba. Mwacitsanzo, Mose, mtsogoleli woyamba wa mtundu wa Isiraeli, “anayamba kufotokoza” zinthu zolembedwa.—Deuteronomo 1:5.

Zaka 1,000 zapitazo, aphunzitsi odziŵa bwino Malemba analipo. Mu 455 B.C E., gulu la Ayuda, kuphatikizapo ana ambili, anasonkhana m’bwalo lalikulu mu mzinda wa Yelusalemu. Aphunzitsi a Baibulo anali “kuŵelenga bukulo [lopatulika] mokweza.” Koma anacitanso zambili. “Iwo anapitiliza kuthandiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene anali kuŵelenga.”—Nehemiya 8:1-8.

Pambuyo pa zaka 500, Yesu Kristu nayenso anali kugwila nchito yophunzitsa imeneyi. Anthu anali kumudziŵa kuti ndi mphunzitsi. (Yohane 13:13) Iye anali kuphunzitsa gulu la anthu komanso munthu aliyense payekha. Pa nthawi ina, anaphunzitsa khamu la anthu pa Ulaliki wake wochuka wa pa Phili, ndipo “khamu la anthulo linakhudzidwa moti linadabwa ndi kaphunzitsidwe kake.” (Mateyu 5:1, 2; 7:28) M’caka ca 33 C.E.,Yesu anakamba ndi ophunzila ake aŵili pamene anali kuyenda pa njila yopita kumudzi wina pafupi ndi Yelusalemu, ndipo ‘anawafotokozela Malemba momveka bwino.’—Luka 24:13-15, 27, 32.

Ophunzila a Yesu analinso alangizi a Mau a Mulungu. Pa cocitika cina, nduna ya ku Itiyopiya inali kuŵelenga mbali ina ya m’Malemba. Wophunzila Filipo anafikila ndunayo ndi kuifunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuŵelengazo?” Poyankha ndunayo inati: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulila?” Pamenepo Filipo anayamba kumufokokozela tanthauzo la zimene anali kuŵelenga.—Machitidwe 8: 27-35.

THANDIZO LIMENE LILIPO MASIKU ANO

Mofanana ndi aphunzitsi a Baibulo a m’nthawi yakale, Mboni za Yehova masiku ano zikugwila nchito yophunzitsa anthu m’maiko 239 padziko lonse. (Mateyu 28:19, 20) Mlungu uliwonse, Mboni za Yehova zimathandiza anthu oposa 9 miliyoni kumvetsetsa Baibulo. Ambili mwa anthuwa sadziŵa zambili za Cikristu. Kuphunzila Baibulo ndi kwaulele ndipo mungaphunzilile panyumba panu kapena pamalo aliwonse amene mufuna. Ena amaphunzila Baibulo pa foni, pakompyuta kapena pa cipangizo ciliconse cokhala ndi intaneti.

Ngati mufuna kudziŵa zambili za mmene mungapindulile ndi makonzedwe amenewa, funsani wa Mboni za Yehova aliyense. Mudzaona kuti Baibulo si buku lovuta kumvetsetsa, koma ‘ndi lopindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuongola zinthu ndi kulangiza m’cilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenelela bwino ndi wokonzeka mokwanila kucita nchito iliyonse yabwino.’—2 Timoteyo 3:16, 17.