KHALANI MASO!
Nkhondo ya ku Ukraine IIoŵa Caka Caciŵili—Kodi Baibo Ipeleka Ciyembekezo Cotani?
Pofika pa Cisanu, February 24, 2023, n’zacisoni kuti caka cathunthu cidzakhala citakwana, cibukileni nkhondo ku Ukraine. Malipoti akuonetsa kuti asilikali pafupi-fupi 300,000 a ku Ukraine, ndiponso a ku Russia, komanso anthu wamba pafupi-fupi 30,000, aphedwa kapena avulazidwa pa nkhondo imeneyi. Koma ciŵelengelo conse cingapitilile pamenepa.
Tsoka lake n’lakuti, nkhondo imeneyi siioneka kuti idzatha msanga.
“Ngakhale kuti caka cikukwana lomba, magulu a nkhondo a ku Russia ciloŵeleni mu Ukraine, palibe cikuonetsa kuti nkhondoyi ili pafupi kutha. Ndipo pa maiko aŵiliwa, palibe likuoneka kukhala na mangolomela okwanila moti n’kugonjetsa linzake na kupambana, komanso sizikuoneka kuti zingatheke maiko aŵiliwa kukhalilana pansi n’kugwilizana zoleka nkhondoyo.”—NPR (National Public Radio), February 19, 2023.
Anthu akuŵaŵidwa mtima kwambili, poona cisoni na mavuto adzaoneni, amene nkhondoyi komanso nkhondo zina, zabweletsa pa anthu ankhani-nkhani osalakwa. Kodi Baibo imatipatsa ciyembekezo cotani? Kodi nkhondo zidzatha?
Nkhondo imene idzatsilize nkhondo zonse
Baibo imafotokoza za nkhondo imene idzapulumutsa mtundu wa anthu, osati kuuwononga. Nkhondo imeneyo imacedwa nkhondo ya Haramagedo, ndipo imanenedwa kuti ni “nkhondo ya tsiku la likulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Pa nkhondo imeneyi, Mulungu adzafafaniza ulamulilo wa anthu, umene wabweletsa nkhondo zosakaza kwambili. Kuti mudziŵe mmene nkhondo ya Haramagedo idzabweletsele mtendele wosatha, ŵelengani nkhani zotsatilazi: