Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 149

Nyimbo ya Cipambano

Nyimbo ya Cipambano

(Ekisodo 15:1)

  1. 1. Muimbileni Yehova M’lungu wokwezeka.

    Aŵaponya m’nyanja Aigupto onyada.

    Mutamandeni palibe

    Wolingana naye.

    Dzina ni Yehova wapambana

    Pa nkhondo.

    (KOLASI)

    Yehova M’lungu wokwezeka

    Ndimwe mwekha ‘mene simusintha.

    Mudzayeletsadi dzina lanu

    Na kuwononga oipa.

  2. 2. Mitundu yonse, ikutsutsana na Yehova.

    Adzaiwononga ngakhale

    Ni yamphamvu.

    Posacedwapa otsutsa

    Adzawonongedwa.

    Onse adzadziŵa Yehova

    Ni wamphamvu.

    (KOLASI)

    Yehova M’lungu wokwezeka

    Ndimwe mwekha ‘mene simusintha.

    Mudzayeletsadi dzina lanu

    Na kuwononga oipa.

(Onaninso Sal. 2:2, 9; 92:8; Malaki 3:6; Chiv. 16:16.)