Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 23

Ulamulilo wa Yehova Wayamba

Ulamulilo wa Yehova Wayamba

(Chivumbulutso 11:15)

  1. 1. Ufumu wa Yehova,

    Lomba ulamulila.

    Khristu alamulila m’Ziyoni.

    Onse mosangalala,

    Aimbile Mulungu,

    Cifukwa Yesu Khristu,

    ali pampando.

    (KOLASI)

    Ufumu wa Mulungu wathu,

    Udzabweletsa cimwemwe,

    Zoipa zonse zidzasila,

    Tidzakhala kwamuyaya.

    Titamande M’lungu wathu,

    Iye amatikonda.

  2. 2. Lomba Yesu ni Mfumu,

    Adzacotsa zoipa.

    Dziko la Satana idzasila.

    Tilalikile onse.

    Tifufuze ofatsa.

    Asankhe kukhala

    ku mbali ya M’lungu.

    (KOLASI)

    Ufumu wa Mulungu wathu,

    Udzabweletsa cimwemwe,

    Zoipa zonse zidzasila,

    Tidzakhala kwamuyaya.

    Titamande M’lungu wathu,

    Iye amatikonda.

  3. 3. Tilemekeze Mfumu.

    Ndipo tiigwadile.

    Ni Mfumu ya Ufumu wa M’lungu.

    Titumikile M’lungu;

    ise timulambile.

    Posacedwa

    adzalamulila zonse.

    (KOLASI)

    Ufumu wa Mulungu wathu,

    Udzabweletsa cimwemwe,

    Zoipa zonse zidzasila,

    Tidzakhala kwamuyaya.

    Titamande M’lungu wathu,

    Iye amatikonda.

(Onaninso 2 Sam. 7:22; Dan. 2:44; Chiv. 7:15.)