Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 74

Imbani Nafe Nyimbo ya Ufumu!

Imbani Nafe Nyimbo ya Ufumu!

(Salimo 98:1)

  1. 1. Nyimbo iyi ni yacisangalalo;

    Imakweza Yehova Mulungu.

    Mau ake amatilimbikitsa.

    Capamodzi bwelani tiimbe.

    (KOLASI)

    ‘Lambilani M’lungu wathu.

    Dziŵitsani anthu onse

    Kuti Yesu ndiye alamulila;

    Tamandani Yehova Mulungu.’

  2. 2. Na nyimboyi tilengeza Ufumu:

    “Khristu Yesu tsopano ni mfumu.”

    Ndipo mtundu watsopano wabadwa;

    Nawo udzalamulila naye.

    (KOLASI)

    ‘Lambilani M’lungu wathu.

    Dziŵitsani anthu onse

    Kuti Yesu ndiye alamulila;

    Tamandani Yehova Mulungu.’

  3. 3. Odzicepetsa angaiphunzile.

    Mau ake ni otsitsimula.

    M’dziko lonse ambili aphunzila,

    Ndipo nawo aitana ena:

    (KOLASI)

    ‘Lambilani M’lungu wathu.

    Dziŵitsani anthu onse

    Kuti Yesu ndiye alamulila;

    Tamandani Yehova Mulungu.’

(Onaninso Sal. 95:6; 1 Pet. 2:9, 10; Chiv. 12:10.)