Onani zimene zilipo

Kukaona Malo pa Beteli

Tikuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi, amene timayacha kuti Beteli. Maofesi ena a nthambi ali na ma miziyamu yakuti munthu akhoza kudzionela yekha zinthu popanda wina kumutsogolela.

Kuyambilanso Kukayendela Maofesi a Nthambi: Pa June 1, 2023, m'maiko ambili tinayambilanso kulola anthu kukayendela maofesi athu a nthambi. Kuti mumve zambili, funsilani ku ofesi ya nthambi imene mufuna kukayendela. Koma conde, osapitako ngati munapezeka na COVID-19, ngati muli na cimfine, kapena ngati caposacedwa munakhalako pafupi na munthu wodwala COVID-19.

Georgia

Aerodromis Dasahleba 13th Street, No. 10

TBILISI, 0182

GEORGIA

+995 32-276-23-59

Kuona Malo

Pa Mande mpaka pa Cisanu

8:30hrs mpaka 10:30hrs ndi 13:30hrs mpaka 15:30hrs.

Nthawi yoona malo: Mphindi 30

Zimene Timacita

Timamasulila mabuku ofotokoza Baibulo m’Ciazebaijani, Cijojiya, ndi Cikudishi ca Cisililiki. Timapanganso ma CD a zofalitsa ndi mavidiyo m’zinenelo zimenezi.

Tengani kapepala koonetsa malo.