Kodi Niyenela Kupemphela kwa Oyela Mtima?
Yankho la m’Baibo
Ayi. Baibo imaonetsa kuti tiyenela kupemphela kwa Mulungu yekha, m’dzina la Yesu. Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Cifukwa cake pemphelani inu comweci: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeletsedwe.” (Mateyu 6:9, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Iye sanalangizepo ophunzila ake kuti azipemphela kwa oyela mtima, angelo, kapena munthu wina aliyense, koma kwa Mulungu cabe.
Yesu anauzanso ophunzila ake kuti: “Ine ndine njila, coonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.” (Yohane 14:6) Ndipo Mulungu anasakha Yesu yekha kuti tizipeleka mapemphelo athu kupitila mwa iye.—Aheberi 7:25.
Nanga bwanji ngati nimapemphela kwa Mulungu komanso kwa oyela mtima?
Mu Malamulo Khumi amene Mulungu anapatsa anthu ake, iye anakamba kuti: “Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje.” (Ekisodo 20:5,) Kodi Mulungu ni “wansanje” m’njila yotani? Iye amafuna kuti tizilambila iye yekha na kudzipeleka kwa iye. Komanso, amafuna kuti tizipemphela kwa iye yekhabasi.—Yesaya 48:11.
Conco, timalakwila Mulungu ngati tipemphela kwa munthu winawake, ngakhale oyela mtima, kapenanso angelo oyela. Pamene mtumwi Yohane anafuna kulambila mngelo, mngeloyo anam’letsa n’kumuuza kuti: “Usatelo ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ali ndi nchito yocitila umboni za Yesu. Lambila Mulungu”—Chivumbulutso 19:10.