Onani zimene zilipo

Kodi Yehova N’ndani?

Kodi Yehova N’ndani?

Yankho la m’Baibo

 Yehova ndiye Mulungu woona wa Baibo, Mlengi wa zinthu zonse. (Chivumbulutso 4:11) Mneneli Abulahamu na Mose anali kulambila iye monga Yesu. (Genesis 24:27; Ekisodo 15:1, 2; Yohane 20:17) Iye si Mulungu wa gulu limodzi la anthu, koma ni Mulungu wa anthu “padziko lonse lapansi.”—Salimo 47:2.

 Dzina la Mulungu ni Yehova monga mmene Baibo imaonetsela. (Ekisodo 3:15; Salimo 83:18) Licokela ku liwu la Cihebeli limene limatanthauza “kukhala,” ndipo akatswili a Baibo ambili amati dzina limeneli limatanthauza kuti “Iye Amacititsa Kukhala.” Ndipo tanthauzo limeneli niyoyeneleladi Yehova popeza iye ndiye Mlengi, komanso Wokwanilitsa cifunilo cake. (Yesaya 55:10, 11) Baibo imatithandiza kudziŵa bwino mwini wake wa dzina limeneli lakuti Yehova, makamaka za khalidwe lake lalikulu la cikondi.—Ekisodo 34:5-7; Luka 6:35; 1 Yohane 4:8.

 Dzina lakuti Yehova linamasulidwa kucokela ku zilembo zinayi za Cihebeli יהוה (YHWH). kachulidwe ka dzina limeneli m’Cihebeli nikosadziwika. Komabe, kalembedwe ka dzina limeneli lakuti “Yehova” kakhala kakulembedwa conco mbili ya cinenelo ca Cingelezi. Ndipo dzina limeneli linaonekela koyamba m’Baibo ya cingelezi lakuti Tyndale’s Bible translation mu caka ca 1530. *

N’cifukwa ciani kachulidwe ka dzina la Mulungu nikosadziŵika mu Cihebeli cakale?

 M’Cihebeli cakale, anali kulemba popanda ma vawelo, anali kuseŵenzetsa makonsonati cabe. Ndiye munthu wodziŵa kuŵelenga Cihebeli anali kuikamo yekha mavawelo oyenelela. Komabe, Malemba Acihebeli (“Cipangano Cakale”) atamalizidwa kulembedwa, Ayuda ena anayamba kutengela cikhulupililo cabodza cakuti dzina la Mulungu siifunika kuchulidwa. Poŵelenga mokuwa Malemba amene anali na dzina la Mulungu, m’malo mochula dzinalo anali kuchula maina akuti “Ambuye” kapena “Mulungu.” M’kupita kwa zaka, cikhulupililo cimeneco cinafalikila, ndipo kachulidwe ka dzinalo kanataika. *

 Ena anali kukhulupilila kuti dzina la Mulungu linali kuchulidwa kuti “Yahweh,” pamene ena anali kulichula mosiyanako. Mpukutu umene unapezeka ku Nyanja Yakufa, umene uli na mbali ya buku la Levitiko mu Cigiliki, anamasulila dzina la Mulungu kuti lao. Olemba Cigiliki akale anali na malingalilo akuti kachulidwe kake ni Iae, I·a·beʹ, komanso I·a·ou·eʹ. Koma palibe umboni oonetsa kuti awa ndiyo anali machulidwa a m’Cihebeli cakale. *

Maganizo olakwika okhudza dzina la Mulungu m’Baibo

 Maganizo olakwika: Mabaibo amene ali na dzina lakuti “Yehova” anangoliikamo cabe.

 Mfundo yazoona: Zilembo zinayi za dzina la Mulungu m’Cihebeli, zimapezeka maulendo pafupifupi 7,000 mu Baibo. * M’mabaibo ambili anacotsamo dzina la Mulungu na kuikamo dzina laudindo lakuti “Ambuye” popanda zifukwa zomveka.

 Maganizo olakwika: Mulungu Wamphamvuzonse safunika kukhala na dzina lapadela.

 Mfundo yazoona: Mulungu iyemwini ndiye anauzila olemba Baibo kuti alembe dzina lake nthawi zokwana masauzande. Ndipo amauza amene amamulambila kuti aziseŵenzetsa dzina lake. (Yesaya 42:8; Yoweli 2:32; Malaki 3:16; Aroma 10:13) Mulungu anaimba mlandu aneneli onama amene anayesa kupangitsa anthu kuiŵala dzina lake.—Yeremiya 23:27.

 Maganizo olakwika: Tikatsatila mwambo wa Ayuda, dzina la Mulungu lifunika kucotsedwamo m’Baibo.

 Mfundo yazoona: Nzoona kuti alembi ena aciyuda anali kukana kuchula dzina la Mulungu. Ngakhale n’conco iwo sanalicotsemo m’Baibo. Mulimonsemo, Mulungu safuna kuti tizitsatila miyambo ya anthu imene ingatipatutse ku malamulo ake.—Mateyu 15:1-3.

 Maganizo olakwika: Dzina la Mulungu siifunika kukhalamo mu Baibo cifukwa kachulidwe kake n’kosadziŵika kwenikweni mu Cihebeli cakale.

 Mfundo yazoona: Kaganizidwe kameneka kamaonetsa monga kuti Mulungu amafuna ife anthu amene timakamba zitundu zosiyana tizichula dzina lake mofanana. Koma Baibo imaonetsa kuti alambili a Mulungu akale amene anali kukamba zitundu zosiyana-siyana, anali kuchula maina a anthu mosiyana-siyana.

 Mwacitsanzo, ganizilani woweluza wina waciisiraeli dzina lake Yoswa. Akhristu a m’nthawi ya atumwi amene anali kukamba Cihebeli akanachula dzina lake kuti Yehoh·shuʹaʽ, pamene okamba Cigiliki akanaichula kuti I·e·sousʹ. M’Baibo muli dzina la Yoswa la Cihebeli imene anaimasulila m’Cigiliki. Izi zionetsa kuti Akhristu anali kuchula maina a anthu malinga na mmene anali kukambila m’citundu cawo.—Machitidwe 7:45; Aheberi 4:8.

 Mfundo imeneyi ingagwilenso nchito pomasulila dzina la Mulungu. Cofunika kwambili si kachulidwe kolondola ka dzinali, koma kupezeka kwa dzina la Mulungu m’Baibo pamalo oyenela.

^ ndime 3 Tyndale anaseŵenzetsa mawu akuti “Iehouah” m’mabuku 5 woyambilila m’Baibo imene anamasulila. M’kupita kwa nthawi, Cingelezi naconso cinasintha kalembedwe ka dzina la Mulungu. Mwacitsanzo, mu caka ca 1612, Henry Ainsworth anaseŵenzetsa mawu akuti “Iehovah” mu buku la Masalimo pamene anali kuimasulila. Pamene anaimasulilanso buku limeneli mu 1639, anaseŵenzetsa mawu akuti “Yehova.” Mofananamo, amene anamasulila Baibo ya American Standard Version, imene inafalitsidwa mu 1901, anaseŵenzetsa dzina lakuti “Yehova” paliponse pamene dzinali inali kupezeka m’malemba Acihebeli.

^ ndime 4 Buku lakuti New Catholic Encyclopedia, Gawo Laciŵili, voliyumu 14, masamba 883-884, imati: “Pambuyo pomasulidwa ku ukapolo, dzina lakuti Yahweh inayamba kuonedwa kukhala yapadela kwambili, ndipo anayamba kuiseŵenzetsa kwambili m’malo mwa mawu akuti ADONAI kapena ELOHIM.”

^ ndime 5 Kuti mudziŵe zambili, onani zakumapeto A4, pa mutu wakuti “Dzina la Mulungu M’Malemba Achiheberi,” mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika.

^ ndime 7 Onani Theological Lexicon of the Old Testament, voliyumu 2, matsamba 523-524.