1 Mafumu 11:1-43

  • Akazi a Solomo anapotoza mtima wake (1-13)

  • Anthu amene ankalimbana ndi Solomo (14-25)

  • Yerobowamu analonjezedwa mafuko (26-40)

  • Solomo anamwalira; Rehobowamu anakhala mfumu (41-43)

11  Mfumu Solomo inakondanso akazi ena ambiri a mitundu ina+ kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao.+ Inakonda akazi a Chimowabu,+ a Chiamoni,+ a Chiedomu, a Chisidoni+ ndi a Chihiti.+  Akaziwa anali ochokera mʼmitundu imene Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Musamakwatirane nawo komanso musamacheze nawo, chifukwa adzapotoza mitima yanu kuti muzitsatira milungu yawo.”+ Koma Solomo ankakonda anthu amenewa ndipo sanafune kuwasiya.  Iye anali ndi akazi olemekezeka 700 komanso akazi ena apambali 300 ndipo patapita nthawi, akaziwo anapotoza mtima wa Solomo.*  Iye atakalamba,+ akazi akewa anapotoza mtima wake moti Solomo ankatsatira milungu ina+ ndipo sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu ngati mmene anachitira bambo ake Davide.  Solomo anayamba kutsatira Asitoreti,+ mulungu wamkazi wa Asidoni ndi Milikomu,+ mulungu wonyansa wa Aamoni.  Solomo anachita zinthu zoipa pamaso pa Yehova ndipo sanatsatire Yehova ndi mtima wonse ngati mmene bambo ake Davide anachitira.+  Pa nthawiyi mʼpamene Solomo anamangira Kemosi malo okwezeka.+ Kemosi anali mulungu wonyansa wa Amowabu ndipo anamʼmangira malowo paphiri lomwe linali pafupi ndi Yerusalemu. Anamangiranso Moleki,+ mulungu wonyansa wa Aamoni,+ malo okwezeka.  Izi nʼzimene anachitira akazi ake onse a mitundu ina amene ankapereka nsembe zautsi ndi nsembe zina kwa milungu yawo.  Yehova anamukwiyira kwambiri Solomo chifukwa mtima wake unapatuka ndipo anasiya kutsatira Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene anaonekera kwa iye kawiri konse+ 10  komanso anamuchenjeza za nkhani imeneyi, kuti asatsatire milungu ina.+ Koma iye sanamvere zimene Yehova analamula. 11  Ndiyeno Yehova anauza Solomo kuti: “Chifukwa chakuti wachita zimenezi ndipo sunasunge pangano langa ndi malamulo amene ndinakupatsa, ndithu ndidzangʼamba ufumuwu kuuchotsa kwa iwe nʼkuupereka kwa mtumiki wako.+ 12  Komabe, chifukwa cha bambo ako Davide, sindichita zimenezi iwe uli moyo. Ufumuwu ndidzaungʼamba nʼkuuchotsa mʼmanja mwa mwana wako,+ 13  koma sindidzauchotsa wonse.+ Ndidzapereka fuko limodzi kwa mwana wako+ chifukwa cha Davide mtumiki wanga ndiponso chifukwa cha mzinda wa Yerusalemu umene ndausankha.”+ 14  Kenako Yehova anabweretsa munthu woti azilimbana ndi Solomo.+ Munthuyo anali Hadadi wa ku Edomu ndipo anali wa mʼbanja lachifumu ku Edomuko.+ 15  Pa nthawi imene Davide anagonjetsa Edomu,+ Yowabu, mkulu wa asilikali, anapita kukakwirira anthu amene anaphedwa. Kumeneko anayambanso kupha mwamuna aliyense wa ku Edomu. 16  (Yowabu ndi Aisiraeli onse anakhala kumeneko miyezi 6, mpaka pamene anapha mwamuna aliyense mu Edomu.) 17  Koma Hadadi ndi Aedomu ena omwe anali atumiki a bambo ake, anathawira ku Iguputo. Pa nthawiyi nʼkuti Hadadi ali kamnyamata. 18  Iwo ananyamuka ku Midiyani nʼkupita ku Parana.+ Kumeneko anatenga anthu ena nʼkukafika ku Iguputo kwa Farao mfumu ya Iguputo. Faraoyo anapatsa Hadadi nyumba ndi malo komanso ankamupatsa chakudya. 19  Farao ankamukonda kwambiri Hadadi moti mpaka anamʼpatsa mkazi. Mkaziyo anali mngʼono wake wa Tapenesi, mkazi wa Farao. 20  Patapita nthawi, mngʼono wake wa Tapenesi anaberekera Hadadi mwana wamwamuna dzina lake Genubati. Tapenesi anamutenga* nʼkumamulera mʼnyumba ya Farao ndipo Genubati ankakhala mʼnyumba ya Farao pamodzi ndi ana a Farao. 21  Hadadi ali ku Iguputo, anamva kuti Davide, mofanana ndi makolo ake, anamwalira+ ndiponso kuti Yowabu mkulu wa asilikali anamwaliranso.+ Choncho Hadadi anapempha Farao kuti: “Kodi mungandilole kuti ndizipita kwathu?” 22  Koma Farao anamufunsa kuti: “Kodi ukusowa chiyani kuno kuti uzifuna kupita kwanu?” Hadadi anayankha kuti: “Palibe chimene ndikusowa, koma chonde ndiloleni ndizipita.” 23  Mulungu anabweretsa munthu winanso woti azilimbana ndi Solomo.+ Munthuyo anali Rezoni mwana wa Eliyada, yemwe anathawa kwa mbuye wake Hadadezeri,+ mfumu ya Zoba. 24  Davide atagonjetsa* anthu a ku Zoba, Rezoni anasonkhanitsa anthu ndipo anakhala mtsogoleri wa gulu la achifwamba.+ Choncho iye ndi gulu lakelo anapita kukakhala ku Damasiko+ nʼkuyamba kulamulira kumeneko. 25  Rezoni ankalimbana ndi Aisiraeli masiku onse a Solomo, ndipo ankawachitira zoipa kuwonjezera pa zoipa zimene Hadadi ankawachitira. Rezoni ankadana kwambiri ndi Aisiraeli pa nthawi imene iye ankalamulira ku Siriya. 26  Panalinso Yerobowamu,+ mwana wa Nebati, wa fuko la Efuraimu, wa ku Zereda. Iye anali mtumiki wa Solomo.+ Mayi ake anali mkazi wamasiye dzina lake Zeruwa. Nayenso Yerobowamu anayamba kuukira mfumu.+ 27  Iye anaukira mfumu chifukwa chakuti: Solomo anamanga Chimulu cha Dothi*+ ndiponso anatseka mpata umene unali pampanda wa Mzinda wa bambo ake Davide.+ 28  Yerobowamu anali munthu waluso. Ndiyeno Solomo ataona kuti mnyamatayo ndi wolimbikira ntchito, anamʼpatsa udindo woyangʼanira+ anthu ogwira ntchito yokakamiza kunyumba ya Yosefe. 29  Pa nthawiyo, Yerobowamu anatuluka mu Yerusalemu ndipo Ahiya+ wa ku Silo, yemwe anali mneneri, anamʼpeza panjira. Ahiya anali atavala chovala chatsopano ndipo awiriwo anali okhaokha kumeneko. 30  Ndiyeno Ahiya anavula chovala chatsopano chimene anavalacho nʼkuchingʼamba mapisi okwana 12. 31  Atatero, anauza Yerobowamu kuti: “Tengapo mapisi 10, chifukwa Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndikungʼamba ufumuwu kuuchotsa mʼmanja mwa Solomo ndipo iwe ndidzakupatsa mafuko 10.+ 32  Koma fuko limodzi lipitiriza kukhala lake+ chifukwa cha mtumiki wanga Davide+ ndiponso chifukwa cha mzinda wa Yerusalemu umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli.+ 33  Ndichita zimenezi chifukwa iwo andisiya+ nʼkuyamba kugwadira Asitoreti mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu ndi Milikomu mulungu wa Aamoni. Iwo sanayende mʼnjira zanga, sanachite zoyenera pamaso panga ndipo sanatsatire malamulo anga ndi ziweruzo zanga ngati mmene anachitira Davide bambo a Solomo. 34  Koma sindidzachotsa ufumu wonse mʼmanja mwake. Ndidzamulola kukhalabe mtsogoleri masiku onse a moyo wake chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene ndinamusankha,+ popeza Davide anasunga malamulo anga. 35  Koma ndidzachotsa ufumuwu mʼmanja mwa mwana wake nʼkuupereka kwa iwe ndipo ndidzakupatsa mafuko 10.+ 36  Mwana wake ndidzamʼpatsa fuko limodzi kuti mtumiki wanga Davide apitirize kukhala ndi nyale pamaso panga mumzinda wa Yerusalemu+ umene ndausankha kuti ukhale ndi dzina langa. 37  Ndidzakutenga ndipo udzalamulira zonse zimene umalakalaka. Udzakhaladi mfumu ya Isiraeli. 38  Ukamvera malamulo anga onse, kuyenda mʼnjira zanga ndiponso kuchita zoyenera pamaso panga posunga malamulo anga ngati mmene anachitira mtumiki wanga Davide,+ inenso ndidzakhala nawe. Ana ako adzalamulira kwa nthawi yaitali mofanana ndi ana a Davide,+ ndipo ndidzakupatsa Isiraeli. 39  Ndidzachititsa manyazi ana a Davide chifukwa cha zoipa zimene anachita,+ koma osati nthawi zonse.’”+ 40  Solomo ankafuna kupha Yerobowamu koma Yerobowamu anathawira ku Iguputo kwa Sisaki,+ mfumu ya Iguputo.+ Anakhala ku Iguputoko mpaka Solomo atamwalira. 41  Nkhani zina zokhudza Solomo, zonse zimene anachita ndiponso nzeru zake, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya Solomo.+ 42  Solomo analamulira Isiraeli yense ku Yerusalemu kwa zaka 40. 43  Kenako Solomo anamwalira* ndipo anaikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide bambo ake. Ndiyeno mwana wake Rehobowamu,+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “akazi akewo ankamusokoneza kwambiri.”
Mabaibulo ena amati: “anamusiyitsa kuyamwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “atapha.”
Kapena kuti, “Milo.” Amenewa ndi mawu a Chiheberi otanthauza “kudzaza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anagona limodzi ndi makolo ake.”