Kwa Akolose 3:1-25

  • Umunthu wakale komanso watsopano (1-17)

    • Chititsani ziwalo za thupi lanu kukhala zakufa (5)

    • Chikondi chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse (14)

  • Malangizo opita ku mabanja a Chikhristu (18-25)

3  Komabe, ngati munaukitsidwa limodzi ndi Khristu,+ pitirizani kufunafuna zinthu zakumwamba, kumene Khristu wakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+  Pitirizani kuganizira zinthu zakumwamba,+ osati zinthu zapadziko lapansi.+  Chifukwa munafa ndipo moyo wanu wabisidwa limodzi ndi Khristu amene ndi wogwirizana ndi Mulungu.  Khristu, amene ndi moyo wathu,+ akadzaonetsa mphamvu zake,* inunso mudzaonetsa naye limodzi mphamvu zanu mu ulemerero.+  Choncho chititsani ziwalo za thupi lanu+ padziko lapansi kukhala zakufa ku chiwerewere,* zinthu zodetsa, chilakolako chosalamulirika cha kugonana,+ kulakalaka zinthu zoipa komanso dyera limene ndi kulambira mafano.  Mulungu adzasonyeza mkwiyo wake kwa anthu amene akuchita zimenezi.  Inunso munkachita zomwezo, pamene munkakhala moyo wofanana ndi anthu amenewo.+  Koma tsopano muyenera kutaya zonsezo kutali ndi inu. Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa+ komanso mawu achipongwe+ ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.+  Musamanamizane.+ Vulani umunthu* wakale+ pamodzi ndi ntchito zake, 10  ndipo muvale umunthu watsopano+ umene Mulungu amapereka. Umunthu watsopano umenewu ndi wopangidwa mogwirizana ndi chifaniziro cha Mulungu.+ Choncho pamene mukudziwa Mulungu molondola, pitirizani kuchititsa umunthu wanu kukhala watsopano. 11  Mukatero, sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti,* kapolo kapena mfulu, chifukwa Khristu amachita zinthu zonse ndipo ife ndife ogwirizana naye.+ 12  Choncho monga anthu osankhidwa ndi Mulungu,+ oyera ndi okondedwa, valani chifundo chachikulu,+ kukoma mtima, kudzichepetsa,+ kufatsa+ komanso kuleza mtima.+ 13  Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse,+ ngakhale pamene wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.+ Mofanana ndi Yehova* amene anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso muzichita chimodzimodzi.+ 14  Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi,+ chifukwa chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.+ 15  Komanso lolani kuti mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima yanu,+ popeza munaitanidwa ku mtendere umenewu monga ziwalo za thupi limodzi. Ndipo sonyezani kuti ndinu oyamikira. 16  Mawu a Khristu akhazikike mwa inu ndipo akupatseni nzeru zonse. Pitirizani kuphunzitsana ndi kulimbikitsana* ndi masalimo,+ nyimbo zotamanda Mulungu komanso nyimbo zauzimu zoyamikira. Pitirizani kuimbira Yehova* mʼmitima yanu.+ 17  Chilichonse chimene mukuchita mʼmawu kapena mu ntchito, muzichita zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, ndipo muziyamika Mulungu Atate kudzera mwa iye.+ 18  Inu akazi, muzigonjera amuna anu,+ chifukwa zimenezi ndi zoyenera kwa anthu otsatira Ambuye. 19  Inu amuna, pitirizani kukonda akazi anu+ ndipo musamawapsere mtima kwambiri.*+ 20  Ana inu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse,+ chifukwa zimenezi zimasangalatsa Ambuye. 21  Inu abambo, musamakwiyitse* ana anu,+ kuti asakhale okhumudwa. 22  Inu akapolo, muzimvera anthu amene ndi ambuye anu+ pa zinthu zonse, osati pokhapokha pamene akukuonani pongofuna kusangalatsa anthu,* koma moona mtima ndiponso moopa Yehova.* 23  Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse ngati kuti mukuchitira Yehova,*+ osati anthu, 24  chifukwa mukudziwa kuti mphoto imene mudzalandire ndi cholowa chochokera kwa Yehova.*+ Tumikirani Ambuye wanu Khristu monga akapolo. 25  Ndithudi, amene akuchita zolakwa adzalandira chilango chifukwa cha zolakwa zimene akuchitazo,+ chifukwa Mulungu sakondera.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “akadzaonetsedwa.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu.”
Mawu akuti “Msukuti” akutanthauza munthu wachimidzimidzi.
Kapena kuti, “kulangizana.”
Kapena kuti, “ndipo musamawachitire nkhanza.”
Kapena kuti, “musamapsetse mtima.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “osati mwachiphamaso ngati munthu wongofuna kusangalatsa anthu.”