Kalata Yopita kwa Aroma 10:1-21

  • Mmene tingakhalire olungama pamaso pa Mulungu (1-15)

    • Kulengeza poyera (10)

    • Oitana pa dzina la Yehova adzapulumuka (13)

    • Mapazi a anthu olalikira ndi okongola (15)

  • Ena anakana uthenga wabwino (16-21)

10  Abale, chimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pemphero langa lochonderera kwa Mulungu ndi lakuti anthu a mtundu wanga apulumutsidwe.+  Chifukwa ndikuwachitira umboni kuti ndi odzipereka potumikira Mulungu,+ koma sakumudziwa molondola.  Ndipo chifukwa chosadziwa chilungamo cha Mulungu,+ iwo sanagonjere chilungamocho+ koma anafuna kukhazikitsa chawochawo.+  Khristu ndiye kutha kwa Chilamulo,+ kuti aliyense wokhulupirira akhale wolungama.+  Pajatu Mose analemba zokhudza mmene munthu angachitire chilungamo mogwirizana ndi Chilamulo, anati: “Aliyense amene akuchita zimenezi adzakhala ndi moyo chifukwa cha malamulo.”+  Koma za chilungamo chimene chimabwera chifukwa cha chikhulupiriro, Malemba amati: “Mumtima mwako usanene kuti,+ ‘Kodi ndani adzapite kumwamba?’+ kuti akatsitse Khristu.  Kapena, ‘Kodi ndani adzapite kuphompho?’+ kuti akaukitse Khristu.”  Koma kodi lemba limati chiyani? Limati: “Mawu a chilamulowo ali pafupi ndi inu, ali mʼkamwa mwanu ndi mumtima mwanu,”+ amenewa ndi “mawu” a chikhulupiriro amene tikulalikira.  Chifukwa ngati ukulengeza ‘mawu amene ali mʼkamwa mwakowo,’ akuti Yesu ndi Ambuye,+ ndipo mumtima mwako ukukhulupirira kuti Mulungu anamuukitsa, udzapulumuka. 10  Kuti munthu akhale wolungama amayenera kukhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake, koma ndi pakamwa pake amalengeza+ poyera chikhulupiriro chake kuti apulumuke. 11  Paja lemba lina limati: “Palibe wokhulupirira iye amene adzakhumudwe.”+ 12  Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki,+ popeza kwa onsewo Ambuye ndi mmodzi, amene amapereka mowolowa manja kwa onse oitana pa dzina lake. 13  Chifukwa “aliyense woitana pa dzina la Yehova* adzapulumuka.”+ 14  Komabe, kodi angaitane bwanji pa dzina lake ngati samukhulupirira? Angakhulupirire bwanji ngati sanamvepo za iye? Nanga angamve bwanji za iye popanda wina kulalikira? 15  Ndipo angalalikire bwanji ngati sanatumidwe?+ Zili ngati mmene Malemba amanenera kuti: “Mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwambiri.”+ 16  Ngakhale zili choncho, si onse amene anatsatira uthenga wabwino. Chifukwa Yesaya anati: “Yehova,* kodi ndani wakhulupirira zimene anamva kwa ife?”+ 17  Choncho munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.+ Ndipo zimene wamvazo zimachokera mʼmawu onena za Khristu. 18  Koma ndifunse kuti, Kodi kumva sanamve? Pajatu “mawu awo anamveka padziko lonse lapansi, ndipo uthenga wawo unamveka mpaka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.”+ 19  Komanso ndifunse kuti, Kodi si zoona kuti Aisiraeli anadziwa?+ Choyamba Mose anati: “Ndidzakuchititsani nsanje pogwiritsa ntchito anthu omwe si Aisiraeli. Ndidzakukwiyitsani koopsa pogwiritsa ntchito mtundu wopusa.”+ 20  Koma Yesaya analankhula molimba mtima kwambiri kuti: “Anthu amene anandipeza ndi amene sankandifunafuna.+ Ndinadziwika kwa anthu amene sanafunse za ine.”+ 21  Koma ponena za Aisiraeli iye anati: “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu osamvera ndiponso amakani.”+

Mawu a M'munsi