Salimo 19:1-14

  • Zimene Mulungu analenga komanso chilamulo zimachitira umboni

    • “Zinthu zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu” (1)

    • Chilamulo changwiro cha Mulungu chimabwezeretsa mphamvu (7)

    • “Machimo amene ndachita mosadziwa” (12)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 19  Zinthu zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu.+Ndipo mumlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake.+   Tsiku lililonse, mawu awo amamveka,Ndipo usiku uliwonse zimasonyeza nzeru zake.   Sizilankhula kapena kutulutsa mawu.Mawu awo samveka.   Koma mawu awo amveka* padziko lonse lapansi,Ndipo uthenga wawo wamveka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.+ Mulungu wamangira dzuwa tenti kumwamba.   Dzuwalo limaoneka ngati mkwati amene akutuluka mʼchipinda chake,Limasangalala ngati mwamuna wamphamvu amene akuthamanga pampikisano.   Limatuluka kuchokera kumalekezero ena akumwamba,Nʼkuzungulira mpaka kumalekezero enanso.+Ndipo palibe chilichonse chimene sichimva kutentha kwake.   Chilamulo cha Yehova ndi changwiro,+ chimabwezeretsa mphamvu.*+ Zikumbutso za Yehova ndi zodalirika,+ zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.+   Malamulo ochokera kwa Yehova ndi olungama, amasangalatsa mtima.+Chilamulo cha Yehova ndi choyera, chimatsegula maso.+   Kuopa Yehova+ nʼkoyera, ndipo kudzakhalapo kwamuyaya. Zigamulo za Yehova nʼzolondola, ndipo pa mbali iliyonse ndi zolungama.+ 10  Nʼzosilirika kuposa golide,Kuposa golide wambiri woyengeka bwino.+Ndipo nʼzotsekemera kuposa uchi,+ kuposa uchi umene ukukha mʼzisa. 11  Ndiponso mtumiki wanu amachenjezedwa nazo.+Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.+ 12  Ndi ndani amene angazindikire yekha zinthu zimene walakwitsa?+ Mundikhululukire machimo amene ndachita mosadziwa. 13  Ndipo mundiletse kuchita zinthu modzikuza, ine mtumiki wanu.+Musalole kuti kudzikuza kundilamulire.+ Mukatero ndidzakhala wopanda chifukwa,+Komanso ndidzakhala wopanda mlandu wa machimo akuluakulu.* 14  Mawu apakamwa panga komanso zimene ndimaganizira mozama mumtima mwanga,Zizikusangalatsani, inu Yehova,+ Thanthwe langa+ ndiponso Wondiwombola.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “muyeso wawo wamveka.”
Kapena kuti, “chimabwezeretsa moyo.”
Kapena kuti, “wa zolakwa zambiri.”