Yesaya 1:1-31

  • Bambo ndi ana ake opanduka (1-9)

  • Yehova amadana ndi kumulambira mwamwambo (10-17)

  • “Tiyeni tikambirane” (18-20)

  • Ziyoni adzabwezeretsedwa kukhala mzinda wokhulupirika (21-31)

1  Masomphenya amene Yesaya*+ mwana wa Amozi anaona, okhudza Yuda ndi Yerusalemu mʼmasiku a Uziya,+ Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya,+ mafumu a Yuda:+   Imvani inu okhala kumwamba, ndipo tcherani khutu inu okhala padziko lapansi,+Chifukwa Yehova wanena kuti: “Ndalera ana nʼkuwasamalira kuti akule,+Koma iwo andipandukira.+   Ngʼombe yamphongo imadziwa bwino munthu amene anaigula,Ndipo bulu amadziwa chinthu chimene mbuye wake amamudyetseramo.Koma Isiraeli sakundidziwa,*+Anthu anga sachita zinthu mozindikira.”   Tsoka kwa mtundu wochimwa,+Anthu olemedwa ndi zolakwa,Ana a anthu ochita zoipa, ana a makhalidwe oipa. Iwo asiya Yehova.+Achitira Woyera wa Isiraeli zinthu zopanda ulemu.Iwo atembenuka nʼkumusiya.   Kodi mumenyedwanso pati mmene mukupitiriza kupandukamu?+ Mutu wanu uli ndi mabala okhaokha,Ndipo mtima wanu ukudwala.+   Kuyambira kuphazi mpaka kumutu palibe pabwino. Thupi lonse lili ndi mabala, zilonda, ndiponso lanyukanyuka.Zilonda zanuzo sizinatsukidwe,* kumangidwa kapena kuthiridwa mafuta.+   Dziko lanu lawonongedwa. Mizinda yanu yawotchedwa ndi moto. Alendo akudya zokolola zochokera munthaka yanu, inu mukuona.+ Lawonongedwa ngati dziko limene lalandidwa ndi adani.+   Mwana wamkazi wa Ziyoni* wasiyidwa ngati msasa mʼmunda wa mpesa,Ngati chisimba* mʼmunda wa nkhaka,Ndiponso ngati mzinda umene wazunguliridwa ndi adani.+   Yehova wa magulu ankhondo akumwamba akanapanda kutisiyira anthu ochepa opulumuka,Tikanakhala ngati Sodomu,Ndipo tikanafanana ndi Gomora.+ 10  Imvani mawu a Yehova, inu olamulira ankhanza a ku Sodomu.+ Mvetserani malamulo* a Mulungu wathu, inu anthu a ku Gomora.+ 11  Yehova wanena kuti: “Kodi nsembe zanu zambirimbirizo zili ndi phindu lanji kwa ine?+ Nsembe zanu zopsereza za nkhosa zamphongo+ ndiponso mafuta a nyama zodyetsedwa bwino+ zandikwana.Sindikusangalala ndi magazi+ a ngʼombe zazingʼono zamphongo,+ a ana a nkhosa ndiponso magazi a mbuzi.+ 12  Inu mukabwera kudzaonekera pamaso panga,+Kodi ndi ndani amene amakuuzani kuti muchite zimenezi,Ndi ndani amene amakuuzani kuti muzipondaponda mabwalo a panyumba panga?+ 13  Musabweretsenso nsembe zina za mbewu zomwe ndi zopanda phindu. Zofukiza zanu ndi zonyansa kwa ine.+ Mumachita zikondwerero mwezi watsopano ukaoneka,+ mumasunga masabata,+ ndiponso mumaitanitsa misonkhano.+Komanso ine ndatopa kukuonani mukugwiritsira ntchito mphamvu zamatsenga+ mukamachita msonkhano wanu wapadera. 14  Ndikudana ndi zikondwerero zimene mumachita mwezi watsopano ukaoneka komanso zikondwerero zina. Zimenezi zasanduka katundu wolemera kwa ine,Ndatopa ndi kuzinyamula. 15  Ndipo mukatambasula manja anu,Ndimakubisirani maso anga.+ Ngakhale mupereke mapemphero ambiri,+Ine sindimvetsera.+Manja anu adzaza magazi.+ 16  Sambani, dziyeretseni.+Chotsani zochita zanu zoipa pamaso panga.Lekani kuchita zoipa.+ 17  Phunzirani kuchita zabwino, muzichita chilungamo,+Dzudzulani munthu wopondereza ena,Tetezani ufulu wa mwana wamasiye,Ndipo muteteze mkazi wamasiye pa mlandu wake.”+ 18  Yehova wanena kuti: “Bwerani tsopano, tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.+ Ngakhale kuti machimo anu ndi ofiira kwambiri,Adzayera kwambiri.+Ngakhale kuti ndi ofiira ngati magazi,Adzayera ngati thonje. 19  Mukakhala ndi mtima wofuna kundimvera,Mudzadya zinthu zabwino za mʼdziko lanu.+ 20  Koma mukakana nʼkupanduka,Mudzawonongedwa ndi lupanga,+Chifukwa pakamwa pa Yehova mʼpamene panena zimenezi.” 21  Mzinda wokhulupirika+ uja wasanduka hule.+ Unali wodzaza ndi chilungamo+Ndipo zachilungamo zinkakhala mwa iye,+Koma tsopano muli zigawenga zopha anthu.+ 22  Siliva wako wasanduka zonyansa,*+Ndipo mowa* wako wasungunuka ndi madzi. 23  Akalonga ako ndi osamva ndipo amagwirizana ndi anthu akuba.+ Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu ndipo amalakalaka kupatsidwa mphatso.+ Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo,Ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza.+ 24  Choncho Ambuye woona, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,Mulungu Wamphamvu wa Isiraeli, wanena kuti: “Eya! Ndidzachotsa adani anga pamaso panga,Ndipo ndidzabwezera adani anga.+ 25  Ndidzakupatsani chilango,Ndidzakuyengani nʼkuchotseratu zonyansa zanu zonse,Ndidzachotsa zinthu zonse zimene zikuchititsa kuti musakhale oyera.+ 26  Ndidzakupatsaninso oweruzaKomanso alangizi ngati mmene zinaliri poyamba.+ Pambuyo pa zimenezi mudzatchedwa Mzinda Wachilungamo komanso Mzinda Wokhulupirika.+ 27  Ziyoni adzawomboledwa ndi chilungamo+Ndipo anthu ake amene adzabwerere, adzawomboledwanso ndi chilungamo. 28  Anthu opanduka ndi ochimwa adzawonongedwa limodzi,+Ndipo amene akusiya Yehova adzatha.+ 29  Chifukwa iwo adzachita manyazi ndi mitengo ikuluikulu imene munkailakalaka,+Ndipo mudzachititsidwa manyazi chifukwa cha minda imene munasankha.*+ 30  Chifukwa mudzakhala ngati mtengo waukulu umene masamba ake akufota,+Ndiponso ngati munda umene ulibe madzi. 31  Munthu wamphamvu adzakhala ngati udzu wouma,Ndipo ntchito yake idzakhala ngati kamoto kakangʼono.Zonsezi zidzayakira limodziPopanda wozizimitsa.”

Mawu a M'munsi

Kutanthauza kuti, “Chipulumutso cha Yehova.”
Kapena kuti, “sakudziwa mbuye wawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sizinafinyidwe.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Zimenezi ndi zonyansa zotsalira poyenga zitsulo.
Kapena kuti, “mowa wamasese.”
Zikuoneka kuti imeneyi ndi mitengo komanso minda imene ankaigwiritsa ntchito polambira mafano.