Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzisangalala Mukamazunzidwa

Muzisangalala Mukamazunzidwa

Akhristu amayembekezera kuti tsiku lina adzazunzidwa. (Yoh 15:20) Ngakhale kuti kuzunzidwa kumabweretsa nkhawa komanso nthawi zina n’kopweteka, n’zotheka kumasangalala uku tikupirira.​—Mt 5:10-12; 1Pe 2:19, 20.

ONERANI VIDIYO YAKUTI TIKHOZA KUMASANGALALABE NGAKHALE KUTI TIKUZUNZIDWA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

Kodi mwaphunzira chiyani kwa M’bale Bazhenov pa nkhani ya

  • kuwerenga Baibulo tsiku lililonse?

  • kulola kuti abale ndi alongo azikuthandizani? a

  • kupemphera pafupipafupi?

  • kuimba nyimbo za Ufumu?

  • kuuza ena zimene timakhulupirira?

a Tikhoza kumapempherera Akhristu omwe ali m’ndende ngakhalenso powatchula mayina. Koma n’zosatheka kuti ofesi ya nthambi izitumiza kwa Akhristuwa makalata omwe abale ndi alongo amawalembera.