Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Kodi Akhristu Ayenera Kuchita Nawo Zikondwerero Zimene Anthu Ena Amachita?

Kodi Akhristu Ayenera Kuchita Nawo Zikondwerero Zimene Anthu Ena Amachita?

ZIKONDWERERO zambiri zimene anthu amachita, kaya zachipembedzo kapena ayi, sizichokera m’Baibulo. Ndiye kodi zikondwerero zimenezi zinachokera kuti? Ngati mutawerenga mabuku osiyanasiyana mukhoza kudabwa ndi zimene amafotokoza zokhudza mmene zikondwerero zambiri zotchuka zinayambira. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

Isitala. Buku lina limati: “Zimene Baibulo limanena m’Chipangano Chatsopano sizisonyeza kuti anthu nthawi imeneyo ankachita mwambo wa Isitala.” (The Encyclopædia Britannica) Ndiye kodi Isitala inayamba bwanji? Isitala inachokera ku miyambo yachikunja. Ngakhale kuti amene amachita chikondwererochi amanena kuti akukondwerera kuuka kwa Yesu, zimene zimachitika pa mwambowu si zachikhristu. Mwachitsanzo, pa mwambowu amagwiritsa ntchito tizidole ta akalulu. Koma buku lina linati: “Chizindikiro cha kalulu n’chachikunja ndipo nthawi zonse chimaimira kubereka.”—The Catholic Encyclopedia.

Chikondwerero cha Chaka Chatsopano. Mayiko amasiyana mmene amachitira chikondwererochi komanso masiku ake. Pofotokoza mmene chikondwerero cha Chaka Chatsopano chinayambira, buku lina linati: “Mu 46 B.C., Juliasi Kaisara, yemwe anali wolamulira wachiroma, anakhazikitsa tsiku la 1 January kukhala tsiku lokondwerera Chaka Chatsopano. Patsikuli, Aroma ankalambira mulungu wawo wotchedwa Janusi, yemwe anali mulungu wa mageti, zitseko komanso chiyambi cha zinthu. Dzina la mwezi wa January, linachokera ku dzina lakuti Janusi. Mulungu ameneyu anali ndi nkhope ziwiri, ina yoyang’ana kutsogolo, ina kumbuyo.” Choncho Chikondwerero cha Chaka Chatsopano chinayambira ku miyambo yachikunja.

Zikondwerero Zina. Sizingatheke kuti tikambirane zokhudza zikondwerero zonse zimene zimachitika padziko lapansili. Komabe chomwe tiyenera kudziwa n’choti Yehova sasangalala ndi zikondwerero zomwe cholinga chake n’kutamanda anthu kapena mabungwe enaake. (Yeremiya 17:5-7; Machitidwe 10:25, 26) Kumbukirani kuti Mulungu amadana ndi zikondwerero zina chifukwa cha mmene zinayambira. Choncho kudziwa mmene zikondwerero zachipembedzo zinayambira n’kofunika kwambiri kuti muthe kudziwa ngati zikondwererozo zimasangalatsa Mulungu kapena ayi. (Yesaya 52:11; Chivumbulutso 18:4) Mfundo za m’Baibulo zimene zafotokozedwa m’Chaputala 16 cha bukuli, zingakuthandizeni kudziwa mmene Mulungu amaonera zikondwerero zosiyanasiyana zomwe si zachipembedzo.