Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

‘Muyenera kukhala aphunzitsi.’ (Aheb. 5:12) Tangoganizani! Yehova, yemwe ndi Mphunzitsi wabwino kwambiri m’chilengedwe chonse, akutipempha ifeyo kuti tiziphunzitsa anthu za iye. Udindo wophunzitsa anthu za Yehova m’banja lathu, mumpingo kapena mu utumiki ndi wapadera komanso waukulu kwambiri. Kodi tingatani kuti tikhale aphunzitsi abwino?

Zimene mtumwi Paulo anauza Timoteyo zingatithandize kupeza yankho la funsoli. Anamuuza kuti: “Pitiriza kukhala wodzipereka powerenga pamaso pa anthu, powadandaulira, ndi powaphunzitsa.” Ndiye anawonjezera kuti: “Ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.” (1 Tim. 4:13, 16) Mawuwa akusonyeza kuti tifunika kuuza anthu uthenga wopulumutsa moyo. Ndiyeno kabukuka kakonzedwa m’njira yoti kakuthandizeni kuchita zimenezo. Tiyeni tingokambirana pang’ono zimene zili m’kabukuka.

Tsamba lililonse lili ndi lemba limene likusonyeza mfundo ya m’Baibulo yogwirizana ndi phunzirolo kapena chitsanzo cha phunziro limene tiyenera kuligwiritsa ntchito

Yehova ndi ‘Mlangizi Wamkulu.’ (Yes. 30:20) N’zoona kuti kabukuka kangatithandize kukhala ndi luso lowerenga komanso kuphunzitsa. Koma tisamaiwale kuti uthenga wathu ndi wochokera kwa Yehova ndipo iye ndi amene amakoka anthu. (Yoh. 6:44) Choncho tizipempha mzimu wake pafupipafupi. Tizikonda kugwiritsa ntchito Mawu ake. Tizithandiza anthu kuganizira kwambiri za Yehova osati za ifeyo. Cholinga chathu chizikhala kuthandiza anthu kuti azikonda kwambiri Yehova.

Dziwani kuti mwapatsidwa mwayi wophunzitsa anthu uthenga wofunika kwambiri. Sitikukayikira kuti zinthu zidzakuyenderani bwino mukamadalira “mphamvu imene Mulungu amapereka.”​—1 Pet. 4:11.

Ndife aphunzitsi anzanu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova