Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 08

Yehova Akhoza Kukhala Mnzanu

Yehova Akhoza Kukhala Mnzanu

Yehova amafuna kuti mumudziwe bwino. Chifukwa chiyani? Amaona kuti mukadziwa bwino makhalidwe ake, njira zake ndi cholinga chake mungafunitsitse kukhala mnzake. Koma kodi n’zothekadi kukhala mnzake wa Mulungu? (Werengani Salimo 25:14.) Kodi inuyo mungatani kuti mukhale mnzake wa Mulungu? Baibulo limayankha mafunso amenewa ndipo limasonyeza kuti kukhala mnzake wa Yehova ndi kofunika kwambiri kuposa kugwirizana ndi munthu wina aliyense.

1. Kodi Yehova akufuna kuti inuyo muchite chiyani?

Baibulo limanena kuti “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobo 4:8) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? Yehova akukupemphani kuti mukhale mnzake. Anthu ena amaona kuti n’zosatheka kugwirizana ndi munthu amene sangathe kumuona. Choncho amaona kuti Mulungu sangakhale mnzawo. M’Baibulo, Yehova amafotokoza zonse zotithandiza kuti tidziwe makhalidwe ake. Iye amachita zimenezi n’cholinga choti tikhale anzake. Tikamawerenga uthenga umene Yehova watipatsa m’Baibulo, ubwenzi wathu ndi iye umalimba kwambiri ngakhale kuti sitinamuonepo.

2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova angakhale Mnzanu wabwino kwambiri kuposa wina aliyense?

Tikutero chifukwa chakuti Yehova amakukondani kwambiri kuposa munthu wina aliyense. Iye amafuna kuti muzisangalala ndiponso kuti muzipemphera kwa iye nthawi zonse mukakumana ndi mavuto. Baibulo limati muzimutulira “nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Yehova ndi wokonzeka kuthandiza, kutonthoza ndiponso kumvetsera anzake akamalankhula.​—Werengani Salimo 94:18, 19.

3. Kodi Yehova amafuna kuti anzake azichita chiyani?

N’zoona kuti Yehova amakonda anthu onse, koma amakonda kwambiri “anthu owongoka mtima.” (Miyambo 3:32) Yehova amafuna kuti anzake aziyesetsa kuchita zinthu zimene iye amaziona kuti ndi zabwino, n’kumapewa zinthu zimene iye amaziona kuti ndi zoipa. Anthu ena amaona kuti sangakwanitse kuchita zinthu zonse zimene Yehova amafuna komanso kupeweratu zoipa zonse. Koma Yehova ndi Mulungu wachifundo. Iye amalandira aliyense amene amamukonda ndi mtima wonse ndiponso amene amayesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa.​—Salimo 147:11; Machitidwe 10:34, 35.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zina zimene mungachite kuti Yehova akhale mnzanu ndiponso chifukwa chake iye angakhale Mnzanu wabwino kwambiri kuposa wina aliyense.

4. Abulahamu anali mnzake wa Yehova

Nkhani ya m’Baibulo yokhudza Abulahamu (yemwenso ankatchedwa kuti Abulamu) imatithandiza kudziwa mmene zimakhalira munthu akakhala mnzake wa Mulungu. Werengani nkhani ya Abulahamu pa Genesis 12:1-4. Kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi Yehova anapempha Abulahamu kuti achite chiyani?

  • Kodi Yehova anamulonjeza chiyani?

  • Kodi Abulahamu anachita chiyani atamva malangizo a Yehova?

5. Zimene Yehova amafuna kuti anzake azichita

Nthawi zambiri timafuna kuti anzathu azichita zinthu zinazake.

  • Kodi inuyo mumafuna kuti anzanu azikuchitirani zinthu ziti?

Werengani 1 Yohane 5:3, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi Yehova amafuna kuti anzake azichita chiyani?

Kuti timvere Yehova, tingafunike kusintha khalidwe lathu. Werengani Yesaya 48:17, 18, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti anzake asinthe zinthu zina?

Mnzathu wabwino amatikumbutsa zinthu zimene zingatiteteze komanso kutithandiza. Yehova amachitanso chimodzimodzi kwa anzake

6. Zimene Yehova amachitira anzake

Yehova amathandiza anzake kupirira mavuto. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:

  • Muvidiyoyi, kodi Yehova anathandiza bwanji mayi wina kulimbana ndi maganizo oipa?

Werengani Yesaya 41:10, 13, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi Yehova walonjeza kuti adzawachitira zotani anzake onse?

  • Kodi mukuganiza kuti Yehova akhoza kukhala Mnzanu wabwino? N’chifukwa chiyani mukutero?

Anzanu apamtima amakuthandizani mukafunika thandizo. Yehova nayenso adzakuthandizani

7. Kuti Yehova akhale mnzathu, tiyenera kulankhulana

Kulankhulana kumalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Werengani Salimo 86:6, 11, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi tingalankhule bwanji ndi Yehova?

  • Kodi Yehova amalankhula nafe bwanji?

Timalankhula ndi Yehova m’pemphero; iye amalankhula nafe kudzera m’Baibulo

ZIMENE ENA AMANENA: “N’zosatheka kukhala mnzake wa Mulungu.”

  • Kodi mungagwiritse ntchito lemba liti posonyeza kuti n’zotheka kukhala mnzake wa Yehova?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yehova akufuna kuti mukhale Mnzake, ndipo iye akuthandizani kuchita zimenezi.

Kubwereza

  • Kodi Yehova amathandiza bwanji anzake?

  • N’chifukwa chiyani Yehova amauza anzake kuti asinthe zinthu zina?

  • Kodi mukuganiza kuti Yehova amafuna kuti anzake azichita zinthu zomwe n’zovuta kuzikwanitsa? N’chifukwa chiyani mukutero?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Kodi kukhala mnzake wa Mulungu kungakuthandizeni bwanji?

“Yehova Ndiye Mulungu Wofunika Kum’dziwa” (Nsanja ya Olonda, February 15, 2003)

Onani zimene zinapangitsa mayi wina kunena kuti kukhala pa ubwenzi ndi Yehova kunapulumutsa moyo wake.

“Sindinkafuna Kufa!” (Nsanja ya Olonda Na. 1 2017)

Mvetserani pamene achinyamata akufotokoza mmene amaonera Yehova.

Kodi Kukhala Bwenzi la Mulungu Kumatanthauza Chiyani? 1:​46