Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Sizingakhale Zoona!”

“Sizingakhale Zoona!”

MWAMUNA wina wa ku New York (U.S.A.) akusimba kuti: “Mwana wanga Jonathan anakacheza kwa mabwenzi pamtunda wa [makilomita] angapo. Mkazi wanga, Valentina, sankafuna kuti iye adzipita kumeneko. Nthaŵi zonse mkazi wanga ankadera nkhaŵa za galimoto zodutsa. Koma mwanayo anakonda kwambiri zamagetsi, ndipo mabwenzi akewo anali ndi malo ogwirira ntchito kumene ankachita nawo ntchitoyo. Ine ndinali panyumba kumadzulo kwa Manhattan, New York. Mkazi wanga anakachezera achibale ake ku Puerto Rico. ‘Jonathan adzabwera posachedwa,’ ndinalingalira motero. Ndiyeno belu la pakhomo linalira. ‘Ndi iyetu ameneyo.’ Koma sanali iye. Anali apolisi ndi akuchipatala. ‘Kodi laisensi iyi ya galimoto mwaidziŵa?’ anandifunsa wapolisi. ‘Inde, ndi ya mwana wanga Jonathan.’ ‘Tabwera ndi uthenga wachisoni. Kwachitika ngozi, ndipo . . . mwana wanu, . . . mwana wanu wafa.’ Mawu anga oyamba anali akuti, ‘Sizingakhale zoona!’ Chochitika choswa mtima chimenecho chinapanga chilonda m’mitima yathu chimene sichinapolebe, ngakhale pambuyo pa zaka.”

‘Tabwera ndi uthenga wachisoni. Kwachitika ngozi, ndipo . . . mwana wanu, . . . mwana wanu wafa.’

Tate wina mu Barcelona (Spain) akulemba kuti: “Kalelo m’Spain wa m’ma 1960, tinali banja lachimwemwe. Panali María, mkazi wanga, ndi ana athu atatu, David, Paquito, ndi Isabel, a zaka 13, 11, ndi 9 motero.

“Tsiku lina m’March 1963, Paquito anabwera kunyumba kuchokera ku sukulu akudandaula ndi mutu wopweteka kwambiri. Tinadabwa kuti chinauchititsa nchiyani​​—koma posapita nthaŵi tinadziŵa chifukwa chake. Panangopita maola atatu ndipo anamwalira. Kunali kukha mwazi kwa muubongo kumene kunatenga moyo wake mwadzidzidzi.

“Imfa ya Paquito inachitika zaka zoposa 30 zapitazo. Ngakhale zili tero, kupweteka kwakukulu kwa imfayo kudakali nafe kufikira lerolino. Nzosatheka kuti makolo afedwe mwana koma osamva kuti atayikidwa chinthu chimene chili mbali ya iwo eniwo​—mosasamala kanthu za utali wa nthaŵi imene yapitapo kapena unyinji wa ana amene angakhale nawo.”

Zochitika ziŵiri zimenezi, za makolo amene anafedwa ana, zimasonyeza mmene chilonda cha kufedwa mwana chimakhalira chozama ndi chotenga nthaŵi. Ali oona chotani nanga mawu a dokotala yemwe analemba kuti: “Imfa ya mwana nthaŵi zonse imakhala yachisoni ndi yopweteka kwambiri kuposa imfa ya munthu wamkulu chifukwa chakuti mwana samaganiziridwa kuti ndiye angayambe kufa. . . . Imfa ya mwana aliyense imakhala kutayika kwa ziyembekezo za mtsogolo, maubale [mwana, mpongozi wamkazi, adzukulu], zokunana nazo . . . zimene zisinapezedwebe.” Ndipo lingaliro la kutayikidwa kwakukulu limeneli lingakhalenso ndi mkazi aliyense wofedwa khanda mwa kupita padera.

Mkazi wina wofedwa akufotokoza kuti: “Mwamuna wanga, Russell, anatumikira monga dokotala wothandiza m’bwalo lankhondo la Pacific mu Nkhondo Yadziko II. Iye anaona nkhondo zoipitsitsa ndi kuzipulumuka. Anabwerera ku United States ku moyo wamtendere. Pambuyo pake anatumikira monga mtumiki wa Mawu a Mulungu. M’zaka zake za kuchiyambi kwa ma 60 anayamba kukhala ndi zizindikiro za nthenda ya mtima. Anayesa kukhala ndi moyo wokangalika. Ndiyeno, tsiku lina mu July 1988, anadwala nthenda yaikulu ya mtima namwalira. Kutayika kwake mu imfa kunali kosautsa mtima kwambiri. Sindinathe ngakhale kutsazikana naye. Sanali mwamuna wanga chabe. Anali bwenzi langa lapamtima. Tinayanjana limodzi m’moyo wa zaka 40. Tsopano zinaonekera kuti ndikayang’anizana ndi kusukidwa kwa mtundu wina.”

Ameneŵa ali chabe oŵerengeka a masoka zikwi zambiri amene amakantha mabanja kuzungulira dziko lonse tsiku lililonse. Monga momwe anthu ambiri olira angakuuzireni, pamene imfa itenga mwana wanu, mwamuna wanu, mkazi wanu, kholo lanu, bwenzi lanu, imakhaladi “mdani wotsiriza,” molingana ndi mmene mlembi Wachikristu Paulo anaitchera. Kaŵirikaŵiri, choyamba chimene munthu amachita mwachibadwa akamva uthenga wachisoni ndicho kukana, “Sizingakhale zoona! Sindikukhulupirira zimenezo.” Ndiyeno pamatsatira machitidwe ena, monga momwe tidzaonera.​—1 Akorinto 15:25, 26.

Komabe, tisanafotokoze mmene malingaliro achisoni amakhalira, tiyeni tiyankhe mafunso ena ofunika. Kodi imfa imatanthauza mapeto a munthuyo? Kodi pali chiyembekezo chilichonse chakuti tikhoza kuonanso okondedwa athu?

Pali Chiyembekezo Chenicheni

Wolemba Baibulo Paulo anapereka chiyembekezo cha kumasuka ku “mdani wotsiriza,” imfa. Iye analemba kuti: “Imfa idzawonongedwa.” (NW) “Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.” (1 Akorinto 15:26) Kodi nchifukwa ninji Paulo anali wotsimikiza motero pazimenezo? Chifukwa chakuti anaphunzitsidwa ndi uyo amene anaukitsidwa kwa akufa, Yesu Kristu. (Machitidwe 9:3-19) Ndicho chifukwa chake Paulo analembanso kuti: “Pakuti monga imfa inadza mwa munthu [Adamu], kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu [Yesu Kristu]. Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo.”​—1 Akorinto 15:21, 22.

Yesu anagwidwa ndi chisoni kwambiri pamene anakumana ndi mkazi wamasiye wa ku Naini ndi kuona mwana wake wakufayo. Cholembedwa cha Baibulo chimatiuza kuti: “Ndipo pamene [Yesu] anayandikira ku chipata cha mudziŵo [Naini], onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri a kumudzi anali pamodzi naye. Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire. Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka. Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake. Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.” Onani mmene Yesu anasonkhezeredwera ndi chifundo, kwakuti anaukitsa mwana wa mkazi wamasiyeyo! Ha, talingalirani zimene zimenezo zikusonyeza ponena za mtsogolo!​—Luka 7:12-16.

Pamenepo, pamaso pa mboni zoona ndi maso, Yesu anachita chiukiriro chosaiŵalika. Chinali chizindikiro cha chiukiriro chimene anali ataneneratu kumbuyoko zimenezi zisanachitike, kubwezeretsedwa ku moyo padziko lapansi pansi pa “miyamba yatsopano.” Pa chochitika chimenecho Yesu anati: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [achikumbukiro, NW] adzamva mawu ake, nadzatulukira.”​—Chivumbulutso 21:1, 3, 4; Yohane 5:28, 29; 2 Petro 3:13.

Mboni zina zoona ndi maso kuukako zinaphatikizapo Petro, limodzi ndi ena pakati pa 12 omwe ankatsagana ndi Yesu pamaulendo ake. Iwo anamumvadi Yesu woukitsidwayo akulankhula m’mphepete mwa Nyanja ya Galileya. Cholembedwacho chimatiuza kuti: “Yesu ananena nawo, Idzani mufisule. Koma palibe mmodzi wa akuphunzira anatha kumfunsa Iye, Ndinu yani? podziŵa kuti ndiye Ambuye. Yesu anadza natenga mkate napatsa iwo, momwemonso nsomba. Imeneyo ndi nthaŵi yachitatu yakudzionetsera Yesu kwa akuphunzira ake, mmene atauka kwa akufa.”​—Yohane 21:12-14.

Chifukwa chake, Petro analemba ndi chikhutiro chonse kuti: “Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu.”​—1 Petro 1:3.

Mtumwi Paulo anasonyeza chiyembekezo chake chodalirika pamene anati: “Ndi kukhulupira zonse ziri monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri; ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu chimene iwo okhanso achilandira, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”​—Machitidwe 24:14, 15.

Motero mamiliyoni akhoza kukhala ndi chiyembekezo champhamvu cha kuonanso okondedwa awo ali amoyo padziko lapansi koma m’mikhalidwe yosiyana kwambiri. Kodi mikhalidweyo idzakhala yotani? Mfundo zowonjezereka za chiyembekezo cha okondedwa athu akufawo chozikidwa pa Baibulo zidzafotokozedwa m’chigawo chotsirizira cha brosha lino, cha mutu wakuti “Chiyembekezo Chotsimikizirika cha Akufa.”

Koma poyamba tiyeni tilingalire mafunso amene mungakhale nawo ngati muli ndi chisoni cha imfa ya wokondedwa: Kodi nkwachibadwa kumva chisoni mwanjira imeneyi? Kodi ndingakhale motani ndi chisoni changa? Kodi ena angachitenji kuti andithandize kupirira? Kodi ndingathandize motani ena omwe ali ndi chisoni? Ndipo kwenikweni, Kodi Baibulo limanenanji za chiyembekezo chotsimikizirika cha akufa? Kodi ndidzawaonanso konse okondedwa anga? Ndipo kuti?