Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 58

Mzinda wa Yerusalemu Unawonongedwa

Mzinda wa Yerusalemu Unawonongedwa

Nthawi zambiri, Ayuda ankasiya Yehova n’kumalambira milungu ina. Yehova anayesetsa kuwathandiza kwa zaka zambiri. Ankawatumizira aneneri kuti awachenjeze koma iwo sankamvera. M’malomwake ankangowaseka. Kodi Yehova anathetsa bwanji vuto lolambira mafanoli?

Nebukadinezara, yemwe anali mfumu ya Babulo, ankagonjetsa mayiko ambiri. Pa ulendo woyamba umene anagonjetsa Yerusalemu, anagwira Mfumu Yehoyakini, akalonga, asilikali ndiponso anthu ena aluso. Onsewa anapita nawo ku Babulo. Anatenganso chuma chonse chimene chinali m’kachisi wa Yehova. Kenako, Nebukadinezara anasankha Zedekiya kuti akhale mfumu ya Yuda.

Poyamba, Zedekiya ankamvera Nebukadinezara. Koma kenako anthu a m’mayiko apafupi komanso aneneri abodza anamuuza kuti asiye kumvera ulamuliro wa Babulo. Koma Yeremiya anamuuza kuti: ‘Mukasiya kumvera Ababulo, anthu anu ambiri aphedwa ndipo m’dziko lino mukhala njala ndi matenda.’

Zedekiya atangolamulira zaka 8, anasiya kumvera Ababulo. Iye anapempha asilikali a ku Iguputo kuti amuthandize. Ndiyeno Nebukadinezara anatumiza asilikali ake kuti akawononge mzinda wa Yerusalemu. Asilikaliwo atazungulira mzindawo, Yeremiya anauza Zedekiya kuti: ‘Mukangouza Ababulo kuti mwagonja, mzindawu komanso anthu anu apulumuka. Koma mukachita makani, Ababulo awotcha mzindawu ndipo inuyo apita nanu ku ukapolo.’ Zedekiya anayankha kuti: ‘Sindingayerekeze n’komwe kuwauza Ababulo kuti ndagonja!’

Patangopita zaka zitatu ndi hafu, asilikali a Babulo analowa mumzindawo n’kuuwotcha. Iwo anawotcha kachisi, kupha anthu ambiri n’kutenga ena kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.

Zedekiya anayamba kuthawa koma asilikali a ku Babulo anamuthamangitsa. Anamugwira pafupi ndi Yeriko n’kupita naye kwa Nebukadinezara. Mfumuyi inapha ana a Zedekiya iye akuona. Kenako anamuchotsa maso n’kumutsekera m’ndende ndipo anafera momwemo. Koma Yehova anauza Ayuda kuti: ‘Pakatha zaka 70 ndidzakubwezeretsani ku Yerusalemu.’

Kodi ukuganiza kuti achinyamata amene anapita ku Babulo zinakawathera bwanji? Kodi iwo anakhalabe okhulupirika kwa Yehova?

“Yehova Mulungu, inu Wamphamvuyonse, zigamulo zanu n’zoona ndi zolungama.”​—Chivumbulutso 16:7