Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ukapolo Ndi Khalidwe Lankhanza Lomwe Lidakalipobe

Ukapolo Ndi Khalidwe Lankhanza Lomwe Lidakalipobe

Ukapolo Ndi Khalidwe Lankhanza Lomwe Lidakalipobe

KODI ukapolo unatha? Anthu ambiri angakonde zitakhala choncho. Tikangomva chabe mawu ameneŵa timakumbukira zinthu zoopsa zankhanza ndiponso zosautsa kwambiri. Komabe anthu ambiri amaganiza kuti zimenezi n’zochitika zakalekale. Mwachitsanzo, ena amaganizira zombo zoweyeseka zakalekale za akapolo, zitanyamula anthu ochuluka mopitirira muyeso ogwidwa mantha, akukhala mwa uve wosaneneka.

Inde, n’zoona kuti m’nyanja zamasiku ano simudzapezamo mukuyenda zombo zoterozo ndipo mayiko anagwirizana zothetsa ukapolo woterowo. Komabe sitinganene n’komwe kuti ukapolo unatheratu. Bungwe loona zaufulu wa anthu la Anti-Slavery International linaŵerengetsera kuti anthu 200 miliyoni adakali paukapolo mwanjira inayake. Amagwira ntchito m’mavuto amene mwina angapose a akapolo amene analipo zaka mazana angapo kumbuyoku. Kwenikweni, anthu ena oona mmene zinthu zikuyendera ananena kuti “anthu ambiri masiku ano ali paukapolo kuposa nthaŵi ina iliyonse m’mbiri.”

Nkhani zokhudza akapolo amasiku anoŵa n’zomvetsa chisoni kwambiri. Kanji, * yemwe ali ndi zaka khumi zokha, amaŵeta ng’ombe za mabwana ankhanza tsiku lililonse omwe amam’menya nthaŵi zonse. Iye anafotokoza kuti, “Ndikachita mwayi ndimapeza mkute, apo ayi ndiye kuti tsiku lonse limatha osadya kena kalikonse. Chiyambireni sindinalipidweko kena kalikonse pantchito yangayi chifukwa chakuti ndine kapolo ndiponso ndine katundu wawo wapakhomo. . . . Ana amsinkhu wanga amaseŵera ndi anzawo, ndipo ine ndikanakonda nditangofa mmalo moti ndizingokhalabe ndi moyo wosautsawu.”

Mofanana ndi Kanji, akapolo amasiku ano nthaŵi zambiri amakhala ana kapena akazi. Amagwira kwambiri ntchito zimene iwo sakufuna, monga kuluka makapeti, kukonza misewu, kudula nzimbe, mwinanso ngakhale kugwira ntchito ya uhule. Ndipo akhoza kuwagulitsa pa ndalama zochepa kwambiri mwina zongokwana madola 10 basi. Ana ena amathanso kugulitsidwa ndi makolo awo kuti akakhale akapolo n’cholinga choti makolowo abweze ngongole zimene zikuwavuta kubweza.

Kodi nkhani zoterezi zikukuipirani? Si inu nokha amene zikukuipirani. Wolemba mabuku wina dzina lake Kevin Bales analemba ndemanga iyi m’buku lake lakuti Disposable People: “Ukapolo ndicho chinthu choipa kwambiri. Sikuti kumangokhala kum’gwiritsa ntchito munthu kwaulere, koma kumakhalanso kuba moyo wake wonse wa munthuyo.” Poona zochita za anthu zauchinyama zimene amachitira anthu anzawo, kodi pali chifukwa chotani chokhulupirira kuti nkhanza yaukapolo imeneyi idzatha? Mwina mungafulumire kuganiza kuti funsoli silikukhudza inuyo mwachindunji, koma ndithu likutero.

Monga mmene tionere, sikuti pali ukapolo wamtundu umodzi wokha. Ukapolo ulipo wamitundu yosiyanasiyana, ndipo mitundu ina imakhudza munthu wina aliyense. Choncho tonsefe tifunika kudziŵa ngati anthu onse adzapezedi mtendere weniweni. Koma poyamba, tiyeni tione kaye mwachidule mbiri ya malonda a ukapolo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Dzinali si lake.

[Zithunzi patsamba 19]

Kuyambira kale azimayi ndi ana osauka akhala akuvutika chifukwa cha malonda a ukapolo

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi chapamwambapa: UN PHOTO 148000/Jean Pierre Laffont

Chinthunzi cha U.S. National Archives