Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mzimu Woyera Ndi Munthu?

Kodi Mzimu Woyera Ndi Munthu?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mzimu Woyera Ndi Munthu?

KODI mzimu woyera wa Mulungu n’chiyani? Baibulo, m’mawu ake oyambirira, limanena kuti mzimu woyera, womwe umatchedwanso “mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu,” “unalinkufungatira pamwamba pa madzi.” (Genesis 1:2) Paubatizo wa Yesu, ngakhale kuti nkhani yake imasonyeza kuti Mulungu anali ‘kumwamba,’ koma imanenanso kuti mzimu woyera unaoneka ‘ukutsika ngati nkhunda’ nutera pa Yesu. (Mateyu 3:16, 17) Komanso, Yesu ananena kuti mzimu woyera ndi “Nkhoswe,” kapena kuti mthandizi.—Yohane 14:16.

Mavesi amenewa limodzi ndi mavesi ena m’Baibulo achititsa anthu ena kuganiza kuti mzimu woyera ndi munthu, ngati mmene Mulungu, Yesu, ndiponso angelo alili anthu auzimu. Ndipo kwa zaka zambirimbiri, zina mwa zipembedzo zikuluzikulu zachikristu zakhala zikunena kuti mzimu woyera ndi munthu. Ngakhale kuti mfundoyi yakhala ikuphunzitsidwa kuyambira kale, anthu ambiri opembedza akupitirizabe kusokonezeka maganizo, ndipo ena amafika potsutsana ndi atsogoleri a tchalitchi chawo. Mwachitsanzo, malinga ndi kafukufuku wina yemwe anachitika posachedwapa, anthu 61 pa anthu 100 alionse anafotokoza kuti amakhulupirira kuti mzimu wa Mulungu ndi “chizindikiro chakuti pali Mulungu kapena chizindikiro cha mphamvu yake, si munthu ayi.” Komano kodi Baibulo limati chiyani?

Zimene Baibulo Limanena

Aliyense wowerenga Baibulo ndi mtima wofuna kuphunzira sangalephere kuona kuti mzimu woyera ndi wosiyana ndi mmene matchalitchi amaufotokozera kuti uli munthu. Taonani nkhani zotsatirazi za m’Baibulo.

1. Mariya, amayi a Yesu, atakaona msuweni wawo, Elisabeti, Baibulo limanena kuti mwana wosabadwa wa m’mimba mwa Elisabeti analumpha, “ndipo Elisabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera.” (Luka 1:41) Kodi n’zomveka kuganiza kuti munthu ‘anadzazidwa’ ndi munthu wina?

2. Yohane Mbatizi atafotokozera ophunzira ake kuti Yesu ndiye amene adzamulowe m’malo, iye anati: “Inetu ndikubatizani inu ndi madzi . . . koma iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera.” (Mateyu 3:11) N’zosatheka kuti Yohane anali kunena kuti mzimu woyera ndi munthu pamene anatchula kuti adzabatiza nawo anthu.

3. Ali m’kati mocheza ndi mkulu wa ankhondo wa Aroma ndi banja lake, mtumwi Petro ananena kuti Yesu anadzozedwa ndi Mulungu “ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu.” (Machitidwe 10:38) Patangotha nthawi yochepa, ‘Mzimu Woyera unagwa pa’ banja la mkulu wa ankhondoyo. Nkhaniyi imati ambiri anadabwa “chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.” (Machitidwe 10:44, 45) Apanso, kafotokozedwe kake sikakugwirizana ndi mfundo yakuti mzimu woyera ndi munthu.

Sizachilendo kuti Mawu a Mulungu afotokoze zinthu zomwe si munthu kuti ndi munthu. Achita zimenezi ndi zinthu zina monga nzeru, kuzindikira, uchimo, imfa, ndi chisomo. (Miyambo 8:1–9:6; Aroma 5:14, 17, 21; 6:12) Yesu weniweniyo ananena kuti “nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ake onse,” kapena kuti zotsatira zake zabwino. (Luka 7:35) N’zodziwikiratu kuti nzeru si munthu yemwe ali ndi ana enieni ayi. N’chimodzimodzinso ndi mzimu woyera. Sikuti ndi munthu chifukwa choti m’malo ena umafotokozedwa ngati munthu.

Nangano Mzimu Woyera N’chiyani?

M’Baibulo, mzimu woyera wa Mulungu umafotokozedwa kuti ndi mphamvu ya Mulungu yomwe Mulungu amagwiritsa ntchito. Motero, kumasulira molondola mawu a Chihebri a m’Baibulo kumasonyeza kuti mzimu wa Mulungu ndi “mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu.” (Genesis 1:2, NW) Baibulo lonse limagwirizana ndi mfundo imeneyi.—Mika 3:8; Luka 1:35; Machitidwe 10:38.

Mulungu sakhala paliponse panthawi zonse, ndipo mfundo imeneyi ikusiyana kwambiri ndi maganizo omwe anthu ambiri ali nawo. Koma ‘amakhala kumwamba’ kumalo a mizimu. (1 Mafumu 8:39; 2 Mbiri 6:39) Malemba amatchulanso malo amene Mulungu amakhala komwenso kuli “mpando wake wachifumu.” (1 Mafumu 22:19; Yesaya 6:1; Danieli 7:9; Chivumbulutso 4:1-3) Komabe, ali ‘kumwamba komwe amakhalako,’ iye angathe kugwiritsa ntchito mphamvu yake yogwira ntchito imeneyi kufika kulikonse, kumalo a mizimu ndiponso m’chilengedwe chonse chomwe timaonachi.—Salmo 139:7.

Kalekale mu 1879, katswiri wa maphunziro a za Baibulo, Charles L. Ives, anafotokoza bwino kwambiri kuti Mulungu amatha kugwiritsa ntchito mphamvu yake ali pamalo amodzi. Analemba kuti: “Mwachitsanzo, timanena kuti, ‘Tsekulani mawindo kuti dzuwa lilowe.’ Sitikhala tikutanthauza dzuwa lenileni ayi, koma cheza cha dzuwalo.” Mofanana ndi zimenezi, palibe chifukwa choti Mulungu achite kuyenda kupita kumalo omwe akufuna kugwiritsa ntchito mphamvu yake. Amangogwiritsa ntchito mzimu wake woyera, womwe ungafike kulikonse m’chilengedwechi. Kumvetsa mfundo yakuti mzimu woyera ndi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, kungakuthandizeni kukhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti mzimu woyera ndi munthu?—Machitidwe 10:44, 45.

▪ Kodi mzimu woyera n’chiyani?—Genesis 1:2.

▪ Kodi mphamvu ya Mulungu ya mzimu woyera imafika mpaka kuti?—Salmo 139:7.