Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

4. Ndi Lolondola Pankhani za Sayansi

4. Ndi Lolondola Pankhani za Sayansi

Chifukwa Chake Tiyenera Kukhulupirira Baibulo

4. Ndi Lolondola Pankhani za Sayansi

Sayansi yapita patsogolo kwambiri masiku ano. Choncho, mfundo zimene asayansi ankanena kalelo zasintha, ndipo zalowedwa m’malo ndi mfundo zatsopano. Zinthu zimene anthu kale ankakhulupirira kuti ndi zoona, panopa zikuonedwa kuti ndi nthano chabe. N’chifukwa chake nthawi zambiri mabuku a sayansi amawalembanso.

BAIBULO si buku la sayansi. Koma pankhani za sayansi, Baibulo ndi lolondola osati kokha pa zimene limanena komanso pa zimene silinena.

Lilibe mfundo za sayansi zolakwika. M’masiku amakedzana anthu ambiri ankakhulupirira zinthu zambiri zolakwika. Ankakhulupirira kuti dziko lapansi ndi lathyathyathya ndiponso kuti limachirikizidwa ndi zinthu zinazake kuti lisagwe. Asayansi asanaphunzire za mmene matenda amafalira ndi kapewedwe kake, madotolo ena ankagwiritsa ntchito njira zamankhwala zosathandiza ngakhalenso zakupha kumene. Koma Baibulo silinanenepo ngakhale kamodzi m’machaputala ake onse okwana 1,100 kuti mfundo kapena njira zimenezo n’zabwino.

Mfundo zogwirizana ndi sayansi. Zaka zoposa 3,500 zapitazo, Baibulo linanena kuti dziko linalenjekeka “pachabe.” (Yobu 26:7) Ndiponso zaka za m’ma 700 B.C.E., Yesaya ananena za “dziko lapansi [lozungulira, NW].” (Yesaya 40:22) Kodi zimene Baibulo linanena kuti dziko ndi lozungulira komanso kuti silinachirikizidwe ndi chilichonse, sizikumveka zamakono?

Chilamulo cha Mose (chopezeka m’mabuku asanu oyambirira a Baibulo), chomwe chinalembedwa cha mu 1500 B.C.E., chinali ndi malamulo othandiza onena za kupatula odwala, zoyenera kuchita munthu akagwira mtembo, ndi kutaya zonyansa.—Levitiko 13:1-5; Numeri 19:1-13; Deuteronomo 23:13, 14.

Kugwiritsa ntchito makina amphamvu kwambiri oonera zakuthambo, ndi chinthu china chimene chathandiza asayansi kuona kuti dziko ndi zinthu zina zonse zinachita kuyamba nthawi inayake. Koma asayansi ena sasangalala ndi mfundo imeneyi chifukwa cha zimene ingatanthauze. Pulofesa wina anati: “Kunena kuti dziko ndi zinthu zonse zinachita kuyamba, kumafuna kuti pakhale winawake amene anaziyambitsa; chifukwa nanga zinthu zingayambe bwanji popanda woziyambitsa?” Koma kale kwambiri, kulibe makina oonera zakuthambo, vesi loyambirira lenileni la Baibulo linali litanena momveka bwino kuti: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1.

Ngakhale kuti ndi lakale kwambiri komanso limanena nkhani zambirimbiri, Baibulo lilibiretu mfundo za sayansi zolakwika. Kodi buku lotere si lofunika kuliwerenga? *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Kuti muone zitsanzo zina za mmene Baibulo limagwirizanira ndi sayansi, onani chaputala 8 cha buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 8]

Mosiyana ndi zimene asayansi kalelo ankakhulupirira, Baibulo linanena molondola kuti dziko ndi lozungulira ndiponso ndi lolenjekeka “pachabe”

[Mawu a Chithunzi]

U.S. Fish & Wildlife Service, Washington, D.C./NASA