Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mapazi a Nalimata

Mapazi a Nalimata

Analengedwa Mwaluso

Mapazi a Nalimata

▪ Asayansi amachita chidwi kwambiri ndi luso la nalimata lotha kuyenda bwinobwino pakhoma kapena kudenga lanyumba koma osagwa. Kodi buluzi waluso lodabwitsali amatha bwanji zimenezi?

Baibulo limati buluzi “amagwira ndi manja ake.” (Miyambo 30:28, NW) Mapazi a nalimata ali ngati manja, ndipo amathandiza kuti nalimata aziyenda bwinobwino pa malo a see. Chala chilichonse cha nalimata chimakhala chokakala ndipo chimakhala ndi titsitsi tambirimbiri. Katsitsi kalikonse kali ndi timphanda tambirimbiri tosaoneka ndi maso athu. Timphanda timeneti tili ndi mphamvu zomata zimene zimathandiza kuti nalimatayo azitha kuyenda bwinobwino pakhoma, kudenga, ngakhalenso pa galasi koma osagwa.

Ofufuza akufuna kupanga zomatira zogwira ntchito ngati mapazi a nalimata, kuti zizitha kumatirira ngakhale pa zinthu zosalala. * Magazini ina inati: “Mwa zina, zomatirazi angathe kumazigwiritsira ntchito kuchipatala. Mwachitsanzo, angathe kupangira mabandeji otha kumata ngakhale atanyowa. Angathenso kupangira zinthu zina zomatira pachilonda m’malo mosokapo.”—Science News.

Mfundo zochepa zimene taonazi zikusonyeza kuti nalimata analengedwadi mwaluso n’chifukwa chake amatha kuchita zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Asayansi akufufuzanso mitundu ina ya nkhanu zimene zimatulutsa timadzi tonanda, tothandiza kuti nkhanuzi zizitha kumamatira ku zinthu zosiyanasiyana m’madzi.

[Chithunzi patsamba 26]

Mmene nalimata amaonekera kumimba kwake

[Chithunzi patsamba 26]

Titsitsi tosaoneka ndi maso ta m’mapazi a nalimata

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

Gecko: Breck P. Kent; close-up: © Susumu Nishinaga/Photo Researchers, Inc.