Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ndingakwanitse kukakhala pandekha?

Kodi ndingakwanitse kukakhala pandekha?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi ndingakwanitse kukakhala pandekha?

“Nthawi zina ndimaona kuti anthu amandinyoza chifukwa chakuti ndikukhalabe ndi makolo anga ngakhale kuti ndili ndi zaka 19. Iwo amaganiza kuti sindingakhwime maganizo ngati ndikukhalabe ndi makolo anga.”—Anatero Katie. *

“Panopa ndili ndi zaka pafupifupi 20 ndipo sindisangalala chifukwa nthawi zambiri ndimakhalira kuuzidwa zochita. Ndikufuna kuchoka pakhomo pa makolo anga chifukwa sandilola kuchita zimene ndikufuna ndipo amangokhalira kundiuza kuti iwowo amadziwa zambiri.”—Anatero Fiona.

MUNTHU amayamba kulakalaka kuchoka panyumba pa makolo ake nthawi yoti angakwanitsedi kukakhala payekha ili kutali kwambiri. Maganizo amenewa si olakwika chifukwa kuyambira pachiyambi, Mulungu anafuna kuti achinyamata akakula azisiya makolo awo n’kukayamba banja lawo. (Genesis 2:23, 24; Maliko 10:7, 8) Koma kodi kufuna kukhala ndi ufulu wochita zimene mukufuna ndi chizindikiro chakuti mwakonzeka kukakhala panokha? Mwina, koma si nthawi zonse. Ndiye kodi mungadziwe bwanji kuti mwakonzeka kuchoka pakhomo pa makolo anu? Dzifunseni mafunso atatu ofunika awa. Funso loyamba ndi lakuti:

Kodi Ndikufuna Kuchoka Chifukwa Chiyani?

Kuti mudziwe bwinobwino zifukwa zimene mukufuna kuchokera, taganizirani zifukwa zotsatirazi. Ndiyeno lembani manambala kuyambira ndi chifukwa chachikulu chimene mukufuna kuchokera.

․․․ Kuthawa mavuto panyumba

․․․ Kukhala ndi ufulu wochita zimene ndikufuna

․․․ Anzanga azindilemekeza

․․․ Kukakhala ndi mnzanga amene akusowa wokhala naye

․․․ Kukagwira ntchito yongodzipereka kwinakwake

․․․ Kuphunzira kukhala ndekha

․․․ Makolo anga apume kundisamalira

․․․ Zifukwa zina

Zifukwa zimene zili pamwambazi pazokha ndi zabwinobwino. Komabe, cholinga chimene mungachokere pakhomo pa makolo anu chingapangitse kuti mukakhale wosangalala kapena ayi. Mwachitsanzo, ngati mwachoka pakhomo pa makolo anu n’cholinga chongofuna kuthawa mavuto kapena chifukwa chongofuna kukhala ndi ufulu wochita zofuna zanu, mungakadabwe kuti zimene mumayembekezera si zimene zikuchitika.

Danielle, yemwe anachoka pakhomo pa makolo ake kwa kanthawi ali ndi zaka 20, anaphunzira zambiri atachoka. Iye anati: “Ngakhale utakhala wekha, sungakwanitse kuchita chilichonse chimene umafuna chifukwa cha kuchuluka kwa ntchito komanso mavuto a ndalama.” Carmen, yemwe anasamukira ku dziko lina kwa miyezi 6, anati: “Ndinasangalala kupita dziko lina, koma nthawi zambiri ndinkakhala wotanganidwa kwambiri. Ndikakhala kunyumba kwanga ndinkagwira ntchito zambiri monga kusesa ndi kukolopa, kukonza zipangizo zowonongeka, kusamala panja, kuchapa zovala, ndi zina zotero.”

N’zoona kuti kuchoka panyumba pa makolo anu kungakuthandizeni kukhala ndi ufulu wochita zofuna zanu komanso mwina anzanu angayambe kukulemekezani. Koma dziwani kuti mukamakhala panokha, mumafunika kulipira nokha mabilu, kuphika, kusesa ndi kukolopa m’nyumba komanso nthawi zina mungamasowe wocheza naye. Choncho, musalole kuti winawake akuumirizeni kuchita zinthu mopupuluma. (Miyambo 29:20) Ngakhale mutakhala ndi zifukwa zomveka zochokera panyumba, ndi bwino kudikirabe. Musanachoke, muyenera kuphunzira zinthu zina zofunika. Zimenezi zikutifikitsa ku funso lachiwiri lakuti:

Kodi Ndakonzeka Kuchoka?

Kuchoka pakhomo pa makolo anu kuli ngati kuyamba ulendo wopita kunkhalango muli nokhanokha. Kodi mungayambe ulendo umenewu musakudziwa kusonkha moto, kuphika zakudya, kapena kugwiritsa ntchito mapu? Ayi. Komabe achinyamata ambiri amachoka pakhomo pa makolo awo asanaphunzire zinthu zambiri.

Mfumu yanzeru Solomo inanena kuti: “Wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) Kuti mudziwe ngati muli wokonzeka kuchoka pakhomo pa makolo anu, Chongani luso limene muli nalo ndipo thethani luso limene mufunika kukhala nalo pa mitu imene ili m’munsiyi.

◯ Kusamala ndalama. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Serena, anati: “Ndimaopa kuchoka pakhomo pa makolo chifukwa ndimaona kuti sindingathe kusamala ndalama.” Kodi inuyo mungaphunzire bwanji kusamala ndalama?

Baibulo limanena kuti: “Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka.” (Miyambo 1:5, NW) Choncho mungachite bwino kufunsa makolo anu kuti akuuzeni ndalama zimene munthu mmodzi angawononge mwezi uliwonse polipira lendi, kugula chakudya, ndiponso kusamala galimoto kapena kulipira basi. Kenako pemphani makolo anuwo kuti akuphunzitseni kulemba bajeti ndi kulipira mabilu. N’chifukwa chiyani ndi bwino nthawi zonse kutsatira bajeti? Mnyamata wina wazaka 20, dzina lake Kevin, anati: “Mukayamba kukhala nokha, mumawononga ndalama zambiri kuposa zimene mumayembekezera. Kupanda kusamala, mukhoza kuyamba kugwira ntchito mopitirira malire n’cholinga choti mulipirire zinthu zosiyanasiyana.”

Kodi mukufuna kuti musanachoke pakhomo pa makolo anu, muyese kaye kudzilipirira nokha chilichonse? Ngati muli pantchito, kwa nthawi yochepa yesani kupatsa makolo anu ndalama zimene amawononga pokupatsani chakudya, malo ogona ndi zinthu zina mwezi uliwonse. Ngati simungathe kapena simukufuna kulipira zinthu zimenezi, ndiye kuti simunakonzeke kukakhala panokha.—2 Atesalonika 3:10, 12.

◯ Ntchito zapakhomo. Brian, yemwe ali ndi zaka 17, ananena kuti chimene amaopa kwambiri akaganizira zochoka pakhomo pa makolo ake n’chakuti azikachapa yekha zovala. Kodi mungadziwe bwanji kuti mwakonzeka kukadzisamalira nokha? Aron, yemwe ali ndi zaka 20, ananena zinthu zomwe zingakuthandizeni kudziwa ngati mwakonzeka. Iye anati: “Kwa mlungu umodzi, yesani kudzichitira chilichonse ngati kuti mukukhala nokha. Muziphika nokha chakudya, muzikagula nokha zinthu kumsika komanso muzigwiritsa ntchito ndalama zanu. Muzichapa ndi kusita nokha zovala. Muzisesa ndi kukolopa nokha m’nyumba. Ndipo mukafuna kupita ku ulendo winawake, muzipita nokha popanda wina kukakusiyani kapena kukakutengani pa galimoto.” Kutsatira malangizo amenewa kungakuthandizeni m’njira ziwiri: (1) mungaphunzire kugwira ntchito ndiponso (2) mungayambe kuyamikira kwambiri zimene makolo anu amakuchitirani.

◯ Kukhala bwino ndi anthu. Kodi mumagwirizana ndi makolo komanso abale anu? Ngati simugwirizana nawo, n’zovuta kukagwirizana ndi mnzanu amene mukufuna kukakhala naye. Taganizirani zimene mtsikana wina wazaka 18, dzina lake Eve, ananena: “Anzanga ena awiri ankagwirizana kwambiri, koma atayamba kukhala limodzi anasiya kugwirizana. Iwo anali osiyana kwambiri chifukwa wina anali waukhondo pamene wina anali wauve. Wina anali wokonda Mulungu, pamene wina sankakonda Mulungu kwenikweni. Choncho, zinthu sizinkayenda.”

Erin, wazaka 18, amafuna kuchoka pakhomo pa makolo ake. Komabe iye anati: “Munthu angaphunzire zambiri zokhudza mmene angakhalire ndi anthu pamene ali pakhomo pa makolo ake. Angaphunzire mmene angathetsere mavuto komanso kukhala ndi mtima wololera. Ndazindikira kuti anthu amene amathawa pakhomo pa makolo awo pofuna kupewa kukangana, saphunzira kuthetsa kusamvana. Iwo amangophunzira kuthawa mavuto.”

◯ Kuchita nokha zinthu zauzimu. Ena amachoka pakhomo pa makolo awo kuti apewe kuchita zinthu zauzimu zimene makolowo amakonda. Ena akachoka amakapitirizabe kuphunzira Baibulo ndiponso kulambira Mulungu koma pasanapite nthawi amasiya n’kuyamba kuchita zinthu zoipa. Kodi mungatani kuti ‘chikhulupiriro chanu chisasweke ngati ngalawa’?—1 Timoteyo 1:19.

Musamangotsatira zimene makolo anu amakhulupirira popanda kuganiza panokha. Yehova Mulungu amafuna kuti tonsefe titsimikizire kuti zimene timakhulupirira ndi zoona. (Aroma 12:1, 2) Choncho, khalani ndi ndandanda yophunzirira Baibulo panokha komanso yochitira zinthu zina zauzimu ndipo muziitsatira. Mungalembe pakalendala masiku omwe mukufuna kumachita zimenezi, n’kuyesetsa kutsatira kwa mwezi umodzi popanda kuchita kuuzidwa ndi makolo anu.

Pomaliza, ganizirani funso lachitatu ili:

Kodi Ndikulowera Kuti?

Ena amachoka pakhomo pa makolo awo chifukwa chofuna kuthawa mavuto kapena chifukwa chosafuna kuti makolo awo aziwauza zochita. Iwo amangoganizira za mavuto amene akuwasiya osaganizira za mavuto amene akakumane nawo. Koma kuchita zimenezi n’chimodzimodzi ndi munthu woyendetsa galimoto amene akungoyang’ana kumene akuchokera osati kumene akupita. Munthu wochita zimenezo, akhoza kuchita ngozi chifukwa sangaone zimene zili kutsogolo. Choncho, kuti zinthu zikuyendereni bwino musangoganizira zochoka pakhomo pa makolo anu koma muziganiziranso za zimene mukachite mukachoka.

Achinyamata ena a Mboni za Yehova achoka pakhomo pa makolo awo n’cholinga chokalalikira kumadera ena, m’dziko lawo lomwelo kapena kumayiko ena. Ena amachoka kuti akagwire nawo ntchito yomanga malo olambirira kapena kukagwira ntchito pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Enanso amaona kuti ndi bwino kukhala paokha kwa kanthawi asanakwatire. *

Lembani m’munsimu chinthu chimene mungafune kuchita mukachoka pakhomo pa makolo anu. ․․․․․

Anthu ena amatha kukhala pakhomo pa makolo awo nthawi yaitali koma osakhwima maganizo kapena kuphunzira zinthu zimene zingawathandize atakakhala paokha. Komabe, musathamangire kuchoka. Muyenera kuganizira nkhaniyi mofatsa. Baibulo limati: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphawi.” (Miyambo 21:5) Muyeneranso kumvera malangizo a makolo anu. (Miyambo 23:22) Mungachite bwino kupemphera kuti Mulungu akupatseni nzeru. Ndipo kuti muchite zinthu mwanzeru, muyeneranso kuganizira mfundo za m’Baibulo zimene takambirana m’nkhaniyi.

Chotero mukamaganizira funso lakuti, ‘Kodi ndingathe kukakhala pandekha?’ muyeneranso kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingakwanitse kuchita zinthu zonse zimene munthu amafunika kuchita akamakhala payekha?’ Ngati mungayankhe kuti inde, ndiye kuti ndinu okonzeka kukakhala panokha.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.ps8318.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha mayina ena m’nkhani ino.

^ ndime 33 Zikhalidwe zimasiyanasiyana. M’zikhalidwe zina, mwana makamaka wamkazi sachoka pakhomo pa makolo ake mpaka pamene adzakwatiwe. Baibulo silinena zambiri pa nkhani imeneyi.

ZOTI MUGANIZIRE

● Ngakhale kuti mwina mukukumana ndi mavuto ambiri panyumba, kodi kukhalabe pakhomo pa makolo anu kwa kanthawi kungakuthandizeni bwanji?

● Pa nthawi imene mukukhala ndi makolo anu, kodi mungachite chiyani chimene chingathandize banja lanu lonse komanso kukuthandizani inuyo kukonzekera kukakhala panokha?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

“Makolo anu akamakupatsani ntchito zinazake kuti mugwire, zimenenso mungafunike kugwira mutakhala kuti mukukhala panokha, zimakupatsani mwayi woti muphunzire bwinobwino mmene mungadzakhalire nokha m’tsogolo.”

“Sikulakwa kufuna kukhala panokha. Koma ngati cholinga chanu chochokera ndi chakuti muthawe malamulo a makolo anu, ndiye kuti simunakonzeke kukakhala panokha.”

[Zithunzi]

Sarah

Aron

[Bokosi patsamba 13]

MAWU KWA MAKOLO

Serena, amene tinamutchula kale uja, amaona kuti adzavutika akadzachoka pakhomo pa makolo ake. Chifukwa chiyani? Iye anati: “Ngakhale pamene ndikufuna kugula chinachake ndi ndalama zanga, bambo anga amandiletsa. Amati imeneyo ndi ntchito yawo. Choncho ndimaona kuti ndidzavutika ndikadzayamba kulipira zonse ndekha.” Mwina bambo a Serena amachita zimenezi chifukwa chomukonda mwana wawoyo. Koma kodi mukuganiza kuti zimenezi zingamuthandize Serena kuti adzakwanitse kukhala payekha?—Miyambo 31:10, 18, 27.

Kodi ana anu munawazoloweza kuwachitira chilichonse, zimene zingachititse kuti adzavutike akadzakhala paokha? Kodi mungadziwe bwanji zimenezi? Taganizirani ngati ana anu akudziwa zinthu zinayi zimene tafotokoza munkhani ili pamwambayi.

Kusamalira ndalama. Kodi ana anu okulirapo angathe kulipira okha msonkho kapena kudziwa zimene angachite kuti atsatire malamulo a boma okhudza msonkho? (Aroma 13:7) Kodi amadziwa kuipa kokhala ndi ngongole zambiri? (Miyambo 22:7) Kodi amatha kuchita bajeti n’kumagula zinthu zogwirizana ndi ndalama zimene amapeza? (Luka 14:28-30) Kodi anayamba agulapo chinthu ndi ndalama zimene azipeza okha? Kodi amawononga nthawi ndiponso ndalama zawo kuti athandize anthu ena, n’kuona chimwemwe chimene munthu amakhala nacho akamathandiza ena?—Machitidwe 20:35.

Ntchito zapakhomo. Kodi ana anu aakazi ndiponso aamuna amatha kuphika? Kodi munawaphunzitsa kuchapa ndi kusita zovala? Ngati ana anu amayendetsa galimoto, kodi amatha kusamalira galimotoyo pochita zinthu zing’onozing’ono monga kusintha tinthu tina tikapsa, kusintha mafuta akada, kapena kusintha matayala?

Kukhala bwino ndi anthu. Ana anu okulirapo akayambana, kodi nthawi zonse inuyo ndi amene mumawagwirizanitsa powauza zochita kuti mkanganowo uthe? Kapena kodi munawaphunzitsa ana anuwo kuti akayambana azithetsa okha nkhaniyo mwamtendere, kenako azikuuzani mmene aithetsera?—Mateyo 5:23-25.

Kuchita zinthu zauzimu. Kodi ana anu mumangowauza zimene akuyenera kukhulupirira, kapena mumawathandiza kuti okha afike pokhulupirira zimene mukuwauzazo? (2 Timoteyo 3:14, 15) M’malo momangowayankha nthawi zonse mafunso amene angakhale nawo pa nkhani za chipembedzo ndi za makhalidwe abwino, kodi mukuwaphunzitsa kukhala ndi luso la “kulingalira” ndiponso “kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika”? (Miyambo 1:4; Aheberi 5:14) Kodi mumafuna kuti ana anu azingotsatira mmene inuyo mumaphunzirira Baibulo, kapena mungafune kuti azichita zabwinopo kuposa mmene inuyo mumachitira?

N’zoona kuti kuphunzitsa ana zinthu zimenezi kumafuna nthawi ndiponso khama. Komabe, kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri chifukwa ana anu akamadzachoka pakhomo panu, simudzadandaula kwambiri podziwa kuti munawakonzekeretsa bwino.

[Chithunzi patsamba 12]

Kuchoka pakhomo pa makolo anu kuli ngati kuyamba ulendo wopita kunkhalango. Muyenera kuphunzira zinthu zina zofunika musanayambe ulendo umenewu