Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

5—Muzikhala Wokonzeka Kusintha

5—Muzikhala Wokonzeka Kusintha

5​—Muzikhala Wokonzeka Kusintha

“Aliyense wochenjera amachita zinthu mozindikira.” (Miyambo 13:16) Kuphunzira zinthu zokhudza thanzi lanu kungakuthandizeni ndi kukulimbikitsani kuti musinthe zinthu zina ndi zina pa moyo wanu ndi wa banja lanu, kuti mukhale ndi thanzi labwino.

Pitirizani kuphunzira. M’mayiko ambiri, mabungwe a boma ndi mabungwe ena amaphunzitsa anthu ndiponso kufalitsa mabuku osiyanasiyana onena za umoyo. Muzipatula nthawi yophunzira zinthu zimenezi kuti mudziwe zina ndi zina zomwe mungachite kuti mukhale ndi thanzi labwino kapenanso kuti musawononge thanzi lanu. Muzikhala wokonzeka kuphunzira zinthu zatsopano komanso kusintha ngati mukufunikira kutero.

Zinthu zabwino zimene mungaphunzire n’kumatsatira pa moyo wanu zingathandizenso ana anu ndi ana awo. Makolo akamapereka chitsanzo chabwino pa nkhani zokhudza kudya zakudya zoyenera, kukhala aukhondo, kugona mokwanira, kuchita masewera olimbitsa thupi, ndiponso kupewa matenda, nthawi zambiri ana awo amatengera zomwezo.—Miyambo 22:6.

Kodi n’chiyaninso chimene muyenera kuchita? Kuti munthu ayambe kuchita zinthu zimene zingamuthandize kukhala ndi thanzi labwino, n’kupitirizabe kuzichita, pamafunika zambiri kuposa kungokhala ndi chidwi. Kusiya zizolowezi zoipa zimene munthu wakhala nazo kwa nthawi yaitali n’kovuta kwambiri. Ndipo kuti munthu asinthe ngakhale zinthu zing’onozing’ono pa moyo wake, amafunika kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuchita zimenezo. Anthu ena safuna kusintha ngakhale adziwe kuti zimene akuchita zikhoza kuwadwalitsa kapena kuwapha. Kodi n’chiyani chimene chingathandize anthu amenewa kuti asinthe? Mofanana ndi tonsefe, ayenera kukhala ndi cholinga chenicheni pa moyo wawo.

Anthu amene ali pabanja amafunika kukhala athanzi ndi amphamvu kuti apitirizebe kuthandizana. Makolo amafuna kuti akhalebe ndi moyo kuti apitirize kusamalira ndi kuphunzitsa ana awo. Ana achikulire amafuna kusamalira achibale awo amene akukalamba. Komanso anthu ambiri amafuna kuti akhale nzika zodalirika zimene zingathandize dziko lawo m’malo mokhala anthu obwezeretsa chitukuko m’mbuyo. Kuti munthu akhale ndi maganizo onsewa, amafunika kukhala wachikondi ndiponso wodera nkhawa anthu ena.

Chinthu china chachikulu chimene chimachititsa anthu kufuna kusamalira thanzi lawo ndicho kuyamikira Mlengi wawo ndiponso kudzipereka kwa iye. Anthu amene amakhulupirira Mulungu amafuna kusamalira mphatso yamtengo wapatali ya moyo imene anawapatsa. (Salimo 36:9) Ngati tili ndi thanzi labwino, tikhozanso kutumikira Mulungu mwamphamvu. Chimenechi ndiye chinthu chachikulu ndiponso chofunika kwambiri chimene chimachititsa anthu kufuna kusamalira thanzi lawo.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Mukamasamalira thanzi lanu mumasangalala ndi moyo