Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chigoba cha Nkhono ya M’madzi

Chigoba cha Nkhono ya M’madzi

Kodi Zinangochitika Zokha?

Chigoba cha Nkhono ya M’madzi

● Tizilombo tambiri timene timapezeka pansi pa nyanja timawala ndipo tina mwa tizilombo timeneti ndi nkhono. Pali nkhono za mtundu winawake zimene zimagwiritsa ntchito kuwala kumeneku podziteteza. Mwachitsanzo nkhanu yam’madzi ikafuna kugwira nkhono ya mtundu umenewu, nkhonoyi imalowetsa thupi lake lonse m’chigoba, kenako imawala mpaka kuopseza nkhanuyo. Koma kodi zimatheka bwanji kuti kuwalako kuzionekera kunja kwa chigobacho?

Taganizirani izi: M’malo moti chigoba cha nkhonoyi chizitchinga kuwala, chimathandiza kuti nkhonoyi ikamawala ili mkati mwa chigoba chake, kuwalako kuzionekera patali. Dimitri Deheyn ndi Nerida Wilson ndi akatswiri omwe amagwira ntchito ku dipatimenti yoona zamoyo za m’nyanja, pa yunivesite ya California, yomwe ili ku San Diego, m’dziko la America. Iwo atachita kafukufuku, anapeza kuti kuwala kumene nkhonoyi imatulutsa kumafalikira m’chigoba chonsecho. Kenako chigobacho chimachititsa kuti kuwalako kuwonjezeke kuwirikiza ka 10 kuposa kuwala kwa galasi la getsi, limene limathandiza kuti getsilo liziwala kwambiri. (Galasili limakhala lokhuthala mainchesi 0.02 ndi mamilimita 0.5) Iwo anapezanso kuti kuwala kumene nkhonoyi imatulutsa ndi kwamphamvu kwambiri kuwirikiza ka 8 kuposa kuwala kwa magetsi. Koma chochititsa chidwi n’chakuti nkhono za mtundu wokhawu ndi zimene zimatulutsa kuwala. Ndipotu chigoba cha nkhonoyi chimatulutsa kuwala kumene kumaonekera patali kwambiri m’madzi.

Dr. Deheyn ananena kuti kudziwa zimene nkhonoyi imachita “kuthandiza kwambiri akatswiri kuti apange zomangira zimene zingathandize kuti magetsi aziwala kwambiri.” Zingawathandizenso kupanga zipangizo zachipatala zodziwira matenda amene munthu akudwala pogwiritsa ntchito kuwala. Ndiponso zimene nkhonoyi imachita zingathandize akatswiri kupanga zipangizo zowala kwambiri koma zogwiritsa ntchito mphamvu yochepa yamagetsi.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi chigoba cha nkhono imeneyi chinachita kusintha kuchokera ku chinthu china kapena ndi umboni wakuti pali winawake amene anachipanga?

[Chithunzi patsamba 18]

Chithunzi cha nkhonoyi ikakhala kuti siikuwala

[Chithunzi patsamba 18]

Mmene nkhonoyi imaonekera ikamawala

[Mawu a Chithunzi patsamba 18]

Left: www.robastra.com; center and right: Courtesy of Dr. D. Deheyn, Scripps Institution of Oceanography, UC San Diego