Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mulungu Amalanga Anthu Pogwiritsa Ntchito Masoka Achilengedwe?

Kodi Mulungu Amalanga Anthu Pogwiritsa Ntchito Masoka Achilengedwe?

ANTHU ena amakhulupirira kuti masiku ano Mulungu amagwiritsa ntchito masoka achilengedwe kuti alange anthu oipa. Koma ena sagwirizana ndi mfundo imeneyi, pomwe ena nkhani imeneyi imawasokoneza maganizo ndipo sadziwa zoona zenizeni. Pulofesa wina wa payunivesite ya ku Virginia, ananena kuti: “Zipembedzo zambiri zimavomereza kuti palibe amene anganene motsimikiza kuti Mulungu ndi amene amachititsa masoka achilengedwe.”

Koma Baibulo limanena zoona zenizeni pa nkhani imeneyi. Limafotokoza ngati ndi zoona kuti Mulungu ndi amene amachititsa masoka achilengedwe kapena ayi. Limafotokozanso zimene zimachititsa kuti anthu azivutika.

Malemba Amatithandiza Kupeza Yankho

Baibulo limanena mfundo ziwiri zofunika kwambiri zokhudza Mulungu yemwe dzina lake ndi Yehova. Mfundo yoyamba ndi yakuti iye ndi Mlengi ndipo ali ndi ulamuliro pa mphamvu za m’chilengedwe. (Chivumbulutso 4:11) Yachiwiri ndi yakuti zimene amachita zimagwirizana ndi makhalidwe ake komanso mfundo zake. Pa Malaki 3:6, Mulungu anati: “Ine ndine Yehova, sindinasinthe.” Poganizira mfundo ziwiri zimenezi, tiyeni tione zimene zinachitika m’mbuyomu pa nthawi ya chigumula komanso ya chilala. Mu nkhani zimenezi tiona kuti pamene Mulungu ankagwiritsa ntchito mphamvu ya m’chilengedwe polanga anthu, ankachita zotsatirazi: (1) ankawachenjeza (2) ankanena chifukwa chake akuwalanga komanso (3) ankateteza atumiki ake okhulupirika.

Chigumula cha M’nthawi ya Nowa

Anawachenjeza kaye.

Kutatsala zaka zambiri kuti chigumula chichitike, Yehova anauza Nowa kuti: “Koma ine ndidzabweretsa chigumula chamadzi padziko lapansi, kuti chiwononge chamoyo chilichonse.” (Genesis 6:17) Nowa yemwe anali “mlaliki wa chilungamo,” anachenjeza anthu za chigumulacho koma anthuwo “ananyalanyaza.”—2 Petulo 2:5; Mateyu 24:39.

Anawauza chifukwa chake.

Yehova ananena kuti: “Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse, popeza dziko lapansi ladzaza ndi chiwawa chifukwa cha iwo.”—Genesis 6:13.

Anateteza atumiki ake okhulupirika.

Yehova anapatsa Nowa malangizo a mmene angapangire chingalawa choti adzalowemo pa nthawi yachigumula. Baibulo limati: “Nowa yekha, pamodzi ndi amene anali naye limodzi m’chingalawacho, anapulumuka.”—Genesis 7:23.

Chilala cha ku Isiraeli

Anawachenjeza kaye.

Yehova Mulungu asanabweretse chilala ku Isiraeli anauza mneneri Eliya kulengeza kuti: “Sikugwa mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine [Mulungu] nditalamula.”—1 Mafumu 17:1.

Anawauza chifukwa chake.

Yehova anabweretsa chilala chifukwa choti Aisiraeli ankalambira Baala yemwe anali mulungu wonyenga. Pofotokoza chifukwa chake Mulungu adzabweretse chilala, Eliya ananena kuti: “Chifukwa anthu inu munasiya kutsatira malamulo a Yehova n’kuyamba kutsatira Abaala.”—1 Mafumu 18:18.

Anateteza atumiki ake okhulupirika.

Pa nthawi yonse ya chilalacho, Yehova ankapereka chakudya kwa atumiki ake okhulupirika.—1 Mafumu 17:6, 14; 18:4; 19:18.

Zimene Umboni Ukusonyeza

Masiku ano palibe umboni wosonyeza kuti Mulungu amalanga anthu pogwiritsa ntchito masoka achilengedwe. Yehova ndi Mulungu wachilungamo, choncho ‘sangawononge olungama pamodzi ndi oipa.’ (Genesis 18:23, 25) Iye ankapulumutsa anthu amene ankamumvera. Koma masiku ano masoka achilengedwe sasankha, amapha aliyense.

Mulungu si amene amachititsa masoka achilengedwe omwe amavutitsa anthu osalakwa

Choncho n’zoonekeratu kuti Mulungu si amene akuchititsa masoka achilengedwe masiku ano. Komanso mmene masokawa amachitikira, sizigwirizana ndi makhalidwe a Mulungu. Lemba la Yakobo 1:13, limanena kuti Mulungu sayesa anthu ndi zoipa ndipo lemba la 1 Yohane 4:8, limanena za khalidwe lalikulu la Mulungu. Lembalo limati: “Mulungu ndiye chikondi.” Choncho Mulungu si amene amachititsa masoka achilengedwe monga mphepo yamkuntho ndi zivomezi zomwe zimavutitsa anthu osalakwa. Koma kodi mavuto amenewa adzatha?

Mavuto Onsewa Adzatha

Polenga anthu, Yehova Mulungu sanafune kuti anthu azidzavutika ndi masoka achilengedwe. Cholinga cha Mulungu n’choti anthu adzakhale ndi moyo wosatha padziko lapansi mwamtendere. Mofanana ndi m’nthawi ya Nowa, Yehova adzawononga anthu oipa. Monga mmene wakhala akuchitira m’mbuyo monsemu akafuna kuwononga anthu oipa, Yehova Mulungu akuchititsa kuti uthenga wochenjeza anthu ulengezedwe padziko lonse n’cholinga choti anthu omvera uthengawo adzapulumuke.—Salimo 37:9, 11, 29; Mateyu 24:14.