Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Thanzi Lathu

Thanzi Lathu

Kodi Mulungu amafuna kuti tizisamalira bwanji thanzi lathu?

“Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambiri, ndiponso pakati pa anthu odya nyama mosusuka.”—Miyambo 23:20.

DZIWANI IZI

Baibulo si buku la zachipatala komanso silimapereka malangizo pa nkhani zonse zokhudza thanzi lathu. Komabe limafotokoza zimene Mulungu amafuna kuti tizichita posamalira thanzi lathu.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

M’Baibulo muli malemba osiyanasiyana osonyeza zimene Mulungu amafuna kuti tizichita posamalira thanzi lathu. Mwachitsanzo, Baibulo limaletsa kuchita zinthu mopitirira muyezo komanso kumwa ndi kudya mosadziletsa. (Miyambo 23:20) M’chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa ana a Isiraeli, munali malangizo omwe ankawathandiza kuti asatenge kapena kufalitsa matenda. Munalinso malamulo omwe ankawateteza kuti asachite ngozi. (Deuteronomo 22:8) Zimenezi zikusonyeza kuti m’Baibulo muli malangizo omwe angatithandize kusamalira thanzi komanso kupewa matenda.

 Kodi Baibulo limanena kuti timadwala chifukwa chiyani?

“Uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo.”Aroma 5:12.

ZIMENE ANTHU AMAGANIZA

Anthu ena amaganiza kuti anthufe timadwala chifukwa choti nthawi imene Mulungu anatilembera yakwana pomwe ena amaganiza kuti timadwala chifukwa choti ena atilodza.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limasonyeza kuti anthufe timadwala chifukwa chakuti Adamu sanamvere Mulungu. (Aroma 5:12) Asanachimwe, Adamu ndi Hava, anali angwiro ndipo sankadwala koma ankadziwa kuti ngati atachimwira Mulungu akhoza kufa. (Genesis 2:16, 17) Komabe, iwo anasankha mwadala kusamvera Mulungu zomwe zinachititsa kuti asakhalenso naye pa ubwenzi komanso kuti akhale opanda angwiro. *

Choncho, tonsefe tinatengera kupanda ungwiro kwa Adamu ndi Hava. N’chifukwa chake timadwala ngakhale kuti anthu ayesetsa kuthetsa matenda.

ZIMENE MUNGACHITE

Baibulo limanena kuti ngati mumamvera malamulo a Mulungu, mudzakhala ndi moyo wathanzi komanso wangwiro m’Paradaiso. (Yesaya 33:24) Mulungu walonjeza kuti adzathetsa mavuto, matenda ndi imfa.—Chivumbulutso 21:3, 4.

Kodi Baibulo limaletsa kumwa mankhwala?

“Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”Mateyu 9:12.

ZIMENE ANTHU AMAGANIZA

Anthu ena amakhulupirira kuti munthu akadwala amafunika kungomupempherera kuti achire.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kale, Mulungu ankalola kuti anthu odziwa zachipatala azithandiza anthu. (Genesis 38:28; Akolose 4:14) Baibulo silisonyeza kuti Mulungu ankadana ndi zoti anthu azigwiritsa ntchito mankhwala azitsamba, mafuta, zakudya zina komanso njira zina zochizira matenda. Ndipotu Yesu anachita kunena momveka bwino kuti “anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”—Mateyu 9:12.

Koma sikuti Baibulo limavomereza njira iliyonse yochizira matenda. Mwachitsanzo, Baibulo silivomereza kuti anthu azingodalira mapemphero kuti wodwalayo achire. Komanso Mulungu amadana ndi njira zochizira matenda zomwe zimalimbikitsa kukhulupirira mizimu. (Agalatiya 5:19-21) Njira yabwino yochizira matenda ndi kupeza thandizo lachipatala mwamsanga ngati n’zotheka m’dera lanu.

^ ndime 10 M’nkhani ino, mawu akuti “ungwiro” akutanthauza moyo wopanda mavuto monga matenda ndi imfa, womwe Adamu ndi Hava anali nawo asanachimwire Mulungu.