Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | MWAMUNA NDI MKAZI WAKE

Zimene Mungachite Ngati Mumacheza Kwambiri ndi Munthu Amene si Mwamuna Kapena Mkazi Wanu

Zimene Mungachite Ngati Mumacheza Kwambiri ndi Munthu Amene si Mwamuna Kapena Mkazi Wanu

ZIMENE ZIMACHITIKA

Mwina mumacheza kwambiri komanso momasuka ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wanu. Mukamacheza mumaganiza kuti, ‘Ndi mnzanga chabe.’ Koma si zimene mwamuna kapena mkazi wanu angaganize atamva zimene mumakambirana.

Ngati zili choncho ndiye kuti muyenera kuchitapo kanthu. Koma choyamba, mufunika kudziwa chimene chinayambitsa kuti muzicheza kwambiri ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu.

ZIMENE ZIMACHITITSA

Kusakhutitsidwa. Kunena zoona, mwamuna aliyense amamva bwino akachitiridwa zinthu zabwino ndi mkazi, mkazinso amamva bwino akachitiridwa zinthu zabwino ndi mwamuna. Aliyense akachitiridwa zimenezi amadziona kuti ndi wofunika. Koma ngati mwakhala m’banja kwa nthawi yaitali, mwina mwayamba kumasangalala mukamacheza ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wanu. Koma mfundo yoti mudziwe ndi yakuti: Kuchita zimenezi kumabweretsa mavuto. Mukamacheza kwambiri ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu, chikondi chanu pa mwamuna kapena mkazi wanu chimayamba kuchepa. Mumakhala kuti mukusonyeza mnzanuyo chikondi chomwe mumayenera kuchisonyeza kwa mwamuna kapena mkazi wanu.

• Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndi zinthu ziti zimene ndimasangalala kuchita ndi mnzangayu zimene ndiyenera kumachita ndi mwamuna kapena mkazi wanga?’

Kusowa wocheza naye. Baibulo limasonyeza kuti anthu okwatirana amakhala ndi “nsautso.” (1 Akorinto 7:28) Mwachitsanzo, nthawi zina mungaone kuti mwamuna kapena mkazi wanu sakukukondani ngati mmene ankakukonderani kale kapena mwina mudakali okwiya chifukwa munasemphana maganizo pa nkhani inayake. N’kutheka kuti mwamuna kapena mkazi wanu safuna kuti muzikambirana za nkhanizi ndipo zimenezi zingakuchititseni kuti muzikhala wokhumudwa komanso muzisowa wocheza naye. Akatswiri ena amanena kuti ngati anthu okwatirana safuna kukambirana nkhani zofunika kwambiri, banja lawo likhoza kukhala losasangalala, mwinanso kutha kumene.

• Dzifunseni kuti, ‘Kodi n’chiyani chimandichititsa kuti ndizifuna kucheza ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wanga?’

 ZIMENE MUNGACHITE

Muziganizira mavuto ake. Baibulo limati: “Kodi munthu anganyamule makala a moto pachifuwa pake, zovala zake osapsa?” (Miyambo 6:27) Mfundo ya palembali ndi yakuti, kuyamba kukondana ndi munthu wina muli kale pa banja kumabweretsa mavuto aakulu. (Yakobo 1:14, 15) Musamangoganizira kwambiri za mavuto amene angabwere pambuyo pake. Muziganizira zimene zachitika kale. Mukamasonyeza chikondi kwa munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu, mumakhala mukumulakwira mwamuna kapena mkazi wanu chifukwa chikondi chimene mukusonyeza winayo mumafunika kumusonyeza iyeyo.

Musamadzinamize. Mukamacheza kwambiri ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu mukhoza kumaona kuti mukanachita bwino mukanakwatirana naye. Koma kuchita zimenezi n’kulakwa chifukwa mumakhala kuti mukuyerekezera zimene mnzanuyo amachita bwino ndi zimene mwamuna kapena mkazi wanu amalakwitsa. Muzikumbukiranso kuti mmene mumamvera mukakhala ndi mnzanuyo ndi mmenenso munkamvera poyamba mukakhala ndi mwamuna kapena mkazi wanu.—Lemba lothandiza: Yeremiya 17:9.

Dziikireni malire. Anthu amatchera alamu m’galimoto kapena m’nyumba n’cholinga choti asaberedwe. Mukhozanso kuchita chimodzimodzi ndi banja lanu. Baibulo limati: “Uteteze mtima wako.” (Miyambo 4:23) Kodi mungachite bwanji zimenezi? Mwina mungayese kuchita zotsatirazi:

  • Muzichita zinthu zothandiza anthu kudziwa mosavuta kuti muli pa banja. Mwachitsanzo, kuntchito mungaike zithunzi za mwamuna kapena mkazi wanu pamalo oonekera.—Lemba lothandiza: Genesis 2:24.

  • Muzisankhiratu zomwe mungachite komanso zomwe simungachite ndi munthu wina yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu. Mwachitsanzo, sichingakhale chanzeru kumakambirana ndi munthuyo mavuto a m’banja mwanu. Simuyeneranso kupita kokadya ndi munthu amene mumagwira naye ntchito yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzanu.

  • Ngati mumacheza kwambiri ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzanu, muyenera kusiya. Ngati mukuona kuti n’zovuta, dzifunseni kuti mukuona choncho chifukwa chiyani. M’malo modera nkhawa kwambiri za kucheza kwanu ndi mnzanuyo, muziganizira kwambiri za mwamuna kapena mkazi wanu ndipo muziyesetsa kuteteza banja lanu.—Lemba lothandiza: Miyambo 5:18, 19.