Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumachita “Phwando Nthawi Zonse”?

Kodi Mumachita “Phwando Nthawi Zonse”?

“Masiku onse a munthu wosautsika amakhala oipa, koma munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.”—Miyambo 15:15.

KODI mawu amenewa amatanthauza chiyani? Mawu amenewa akutanthauza mmene munthu amamvera mumtima mwake. “Munthu wosautsika” amangoganizira za zinthu zomwe sizikuyenda bwino zomwe zimachititsa kuti masiku ake akhale “oipa.” Pamene “munthu wamtima wosangalala” amayesetsa kuona zinthu zabwino ndipo zimenezi zimachititsa kuti azisangalala, kapena kuti m’maganizo mwake azikhala ngati ali pa “phwando nthawi zonse.”

Tonsefe timakumana ndi mavuto amene amatilepheretsa kusangalala. Komabe tikhoza kuchita zinthu zina zimene zingatithandize kukhalabe osangalala pamene zinthu sizikutiyendera bwino. Taonani zimene Baibulo limanena.

  • Musamade nkhawa ndi zinthu zomwe sizinachitike. Yesu Khristu anati: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”—Mateyu 6:34.

  • Yesetsani kumaganizira zinthu zimene zikukuyenderani bwino pa moyo wanu. Mukakhumudwa, mungachite bwino kulemba zinthu zonse zimene zikukuyenderani. Muyeneranso kupewa kumangoganizira zimene munalakwitsa kalekale. Muzingoona zimene mwaphunzira pa zimene munalakwitsazo, koma zisamakulepheretseni kuchita zinthu zina. Muzichita ngati dilaivala yemwe amayang’ana pagalasi loonera kumbuyo koma samayang’ana pagalasipo kwa nthawi yaitali. Muzikumbukiranso kuti ‘Mulungu amakhululukadi.’—Salimo 130:4.

  • Mukakhumudwa muzifotokoza mavuto anu kwa munthu amene akhoza kukulimbikitsani. Lemba la Miyambo 12:25 limanena kuti: “Nkhawa” imaweramitsa mtima wa munthu, “koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.” “Mawu abwino” amenewa angachokere kwa munthu wa m’banja mwanu kapena mnzanu. Muyenera kusankha munthu amene samangoganizira za zinthu zimene sizikuyenda bwino koma amene ‘amakukondani nthawi zonse.’—Miyambo 17:17.

Mawu anzeru omwe ali m’Baibulo athandiza anthu ambiri kukhala osangalala ngakhale pamene akukumana ndi mavuto. Tikukhulupirira kuti nanunso mawu amenewa angakuthandizeni.