Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?

Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?

DIANA * amaoneka kuti ndi mtsikana wanzeru, wansangala komanso wokonda kucheza ndi anthu. Koma ngakhale amaoneka chonchi, ali ndi mavuto aakulu amene amam’chititsa kuti nthawi zambiri azivutika maganizo. Iye anati: “Tsiku silidutsa ndisanaganize zoti kuli bwino nditangofa. Ndimaona kuti ngakhale nditamwalira, palibe amene angandisowe chifukwa ndine wosafunika.”

Nyuzipepala ina ya ku Canada inanena kuti: “Kafukufuku wina anasonyeza kuti pa anthu 200 amene amafuna kudzipha, mmodzi amadziphadi ndipo pa anthu 400 amene amaganiza zoti adzadzipha, m’modzi amadzadziphadi.”—THE GAZETTE, MONTREAL, CANADA.

Diana amanena kuti sangayerekeze n’komwe kudzipha. Komabe, nthawi zina amaona kuti palibe chifukwa chokhalira ndi moyo. Iye ananena kuti: “Ndimalakalaka patachitika ngozi inayake ine n’kufa. Kwa ine imfa si mdani, ndipo sindiiopa.”

Anthu ambiri amaganiza zofanana ndi zimene Diana amaganizazi, ndipo ena amaganiza zodzipha pamene ena anayesapo kudzipha. Koma akatswiri amanena kuti anthu ambiri amene amafuna kudzipha sikuti kwenikweni amafunadi kufa, koma amangoona kuti kudzipha ndi njira imene angathetsere mavuto awo. Mwachidule tingati, anthu amenewa amaona kuti pali zifukwa zokwanira zoti kuli bwino angofa, choncho amafunika kuwatsimikira kuti palinso zifukwa zomveka zokhalira ndi moyo.

Kodi zifukwa zimenezi ndi ziti? Taonani mfundo zitatu zimene zatchulidwa m’nkhani yotsatirayi.

^ ndime 3 Si dzina lake lenileni.