Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PACHIKUTO | KODI MOYO UNAYAMBA BWANJI?

Mafunso Awiri Omwe Tiyenera Kudziwa Mayankho Ake

Mafunso Awiri Omwe Tiyenera Kudziwa Mayankho Ake

1 Kodi Moyo Unayamba Bwanji?

ZIMENE ANTHU AMANENA: Zinthu zamoyo zinachokera ku zinthu zopanda moyo.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA SAKHULUPIRIRA ZIMENEZI? Panopa asayansi amadziwa zambiri zokhudza mmene zinthu zamoyo zimapangidwira, koma amalephera kumvetsa mmene chinthu chopanda moyo chingasinthire n’kukhala chamoyo. Komanso pali kusiyana kwakukulu pakati pa zamoyo ndi zopanda moyo.

Akatswiri asayansi sadziwa bwino mmene zinthu padzikoli zinalili zaka mabiliyoni apitawo. Ndipo amasiyana maganizo pa nkhani ya kumene moyo unayambira. Ena amaganiza kuti unayambira pa chiphalaphala chochokera pansi pa nthaka. Pomwe ena amaganiza kuti unayambira pansi pa nyanja. Enanso amakhulupirira kuti moyo unayambira m’mlengalenga ndipo unafika padzikoli kudzera m’miyala yomwe inagwa kuchokera m’mlengalengamo. Koma zimenezi sizikuyankha funso lakuti moyo unayamba bwanji. Zikungosonyeza malo amene asayansi amaganiza kuti moyo unayambira.

Asayansiwa amaganiza kuti panali tizinthu tinatake totchedwa mamolekyu tokhala ndi malangizo okhudza mmene chinthu chiyenera kuonekera tomwe tinasintha n’kukhala mamolekyu amene tikuwadziwa masiku ano. Amakhulupirira kuti kenako mamolekyuwa omwe anali a zinthu zopanda moyo ankatha kusintha komanso kuchulukana. Komabe asayansi amalephera kupeza umboni woti mamolekyuwa analipodi ndipo ayeserapo kupanga mamolekyu ngati amenewa koma alephera.

Zamoyo n’zosiyana kwambiri ndi zopanda moyo chifukwa zili ndi maselo omwe amatha kusunga ndi kugwiritsa ntchito malangizo. Maselo amatha kusamutsa, kutanthauzira komanso kusunga malangizo okhudza mmene chinthu chiyenera kuonekera. Asayansi ena amaona kuti malangizowa ali ngati pulogalamu ya pakompyuta ndipo maselo ali ngati kompyutayo. Koma amene amakhulupirira kuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, amalephera kufotokoza kuti malangizowa amachokera kuti.

Kuti selo lizigwira bwino ntchito limafunika mamolekyu okhala ndi mapuloteni. Puloteni iliyonse imakhala ndi tizinthu tinanso ndipo tizinthu timeneti timasanjidwa mogometsa kwambiri. Zimenezi zimapangitsa kuti puloteniyo izigwira bwino ntchito. Poona zonsezi asayansi ena amaona kuti sizingangochitika zokha kuti puloteni ipangidwe mogometsa chonchi. Wasayansi wina, dzina lake Paul Davies anati: “Poganizira mmene selo lilili komanso mmene limagwirira ntchito, zingakhale zosamveka kuganiza kuti zimenezi zinangochitika zokha.”

MFUNDO YAKE: Pambuyo pofufuza kwa zaka zambiri, asayansi alephera kupeza umboni woti zamoyo zinachokera ku zinthu zopanda moyo.

2 Kodi Mitundu Yosiyanasiyana ya Zamoyo Inachokera Kuti?

ZIMENE ANTHU AMANENA: Chinthu chamoyo choyambirira chinayamba kusintha pang’onopang’ono n’kukhala zamoyo zosiyanasiyana kuphatikizapo anthufe. Ndipo zimenezi zinkachitika potengera nyengo komanso mmene zinthu zinalili pamalowo.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA SAKHULUPIRIRA ZIMENEZI? Chinthu chilichonse chamoyo chimakhala ndi maselo wamba komanso maselo ena ogometsa kwambiri. Anthu amene amakhulupirira zoti zamoyo zinachokera ku zinthu zina amati maselo wamba amatha kusintha n’kukhala maselo ogometsa kwambiri. Pa mfundoyi, buku lina linanena kuti zoti selo wamba lingasinthe n’kukhala selo logometsa “n’zosamvetsetseka chifukwa moyo umakhala utayambika kale.”

Asayansi apeza kuti mamolekyu a mu selo, amagwira ntchito zosiyanasiyana. Ntchito zake ndi monga kusintha chakudya kuti chikhale mphamvu, kukonza mbali za maselo zomwe zawonongeka komanso kupereka mauthenga ku selo. Ndiye kodi zingakhale zomveka kunena kuti maselo omwe amachita zinthu zonsezi anachita kusintha kuchokera ku zinthu zina? Ambiri amaona kuti zimenezi n’zosatheka.

Anthu komanso nyama zimakula kuchokera ku dzira lomwe lakumana ndi umuna. Dziralo limakhala ndi maselo ndipo maselowo amayamba kuchulukana. Zikatere, maselowo amayamba kuoneka mosiyanasiyana ndipo amapanga mbali za thupi. Koma amene amakhulupirira kuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, amalephera kufotokoza kuti zimenezi zimachitika bwanji.

Panopa asayansi atulukira zoti, kuti chinthu chamoyo chisinthe n’kukhala china, pangafunike kuti mamolekyu a maselo a chinthucho asinthe. Ndiyetu zingakhale zosamveka kuti chinthu chamoyo choyambirira chinasintha pang’onopang’ono n’kukhala zamoyo zomwe timaona masiku ano. Anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, sangafotokoze bwino mmene ngakhale selo wamba limapangidwira. Wasayansi wina dzina lake, Michael Behe anati: “Tikachita kafukufuku pa zinthu zamoyo, zimene timapeza zimakhala zodabwitsa kwambiri. Ambirife timaona kuti zimenezi sizingangochitika zokha. Payenera kuti pali winawake amene anazilenga.”

Anthu amaganiza kwambiri kuposa nyama komanso ali ndi makhalidwe monga kuwolowa manja ndiponso kudzipereka. Amathanso kudziwa zoyenera ndi zosayenera kuchita. Anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachokera ku chinthu chamoyo choyambirira chomwe chinayamba kusintha pang’onopang’ono, sangathe kufotokoza kuti zinatheka bwanji kuti anthu akhale ndi makhalidwe amenewa.

MFUNDO YAKE: Ngakhale kuti asayansi ambiri amakhulupirira kuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina, asayansi ena sakhulupirira zimenezi. Zili choncho chifukwa zimene amanena asayansi amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina, siziyankha momveka funso lakuti, kodi moyo unayamba bwanji? ndi lakuti, kodi mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo inachokera kuti?