Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KUCHEZA NDI | ANTONIO DELLA GATTA

N’chifukwa Chiyani Wansembe Anasiya Chipembedzo Chake?

N’chifukwa Chiyani Wansembe Anasiya Chipembedzo Chake?

ANTONIO DELLA GATTA anachita maphunziro aunsembe ku Rome kwa zaka 9. Kenako mu 1969 anaikidwa kukhala wansembe. Patapita nthawi anakhala mkulu pasukulu ina ya ansembe yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Naples ku Italy. Ali kumeneko, anachita kafukufuku pa zomwe chipembedzo cha Katolika chimaphunzitsa ndipo anaona kuti si zochokera m’Baibulo. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe zambiri za moyo wake.

Kodi munabadwira kuti?

Ndinabadwira ku Italy m’chaka cha 1943. M’banja mwathu tinalipo ana 7 ndipo tinali a Katolika. Tinkakhala m’mudzi winawake waung’ono. Bambo anga anali mlimi komanso kalipentala.

N’chiyani chinakupangitsani kukhala wansembe?

Ndili mnyamata, ndikamamvetsera ansembe akulalikira zinkandisangalatsa kwambiri. Ndinkachita chidwi ndi mmene mawu awo ankamvekera komanso miyambo yomwe ankachita. Zimenezi zinapangitsa kuti ndiyambe kuganiza zodzakhala wansembe. Ndili ndi zaka 13, mayi anga anandipititsa kusukulu yogonera konko yomwe inkaphunzitsa anyamata kuti adzakhale ansembe.

Kodi kusukuluko munkaphunziranso Baibulo?

Osati kwenikweni. Ndili ndi zaka 15, aphunzitsi anga ena anandipatsa Kabaibulo kokhala ndi Mauthenga Abwino okha basi ndipo ndinakawerenga kangapo. Ndili ndi zaka 18, ndinapita ku Rome kukaphunzira payunivesite inayake yomwe imayang’aniridwa ndi papa. Ndinkaphunzira Chilatini, Chigiriki, mbiri yakale, nzeru za anthu, komanso maphunziro a zachipembedzo. Tinkanena mavesi a m’Baibulo omwe tinaloweza komanso tinkamvetsera Baibulo likuwerengedwa pa maulaliki a Lamlungu. Komabe sindinganene kuti tinkaphunzira Baibulo.

Ndiyeno mutakhala wansembe munkaphunzitsanso anthu?

Nthawi zina ndinkaphunzitsa zomwe ndauzidwa ndi akuluakulu a ku Vatican. Koma nthawi zambiri ndinkagwira ntchito ya muofesi.

N’chifukwa chiyani munayamba kukayikira zomwe chipembedzo cha Katolika chimaphunzitsa?

Pali zinthu zitatu zimene zinkandikayikitsa. Choyamba, tchalitchichi chimalowerera ndale. Chachiwiri, chimalekerera akuluakulu ake akamachita makhalidwe oipa. Ndipo chachitatu, zinthu zina zimene tchalitchichi chimaphunzitsa, sizichokera m’Baibulo. Mwachitsanzo, zingatheke bwanji kuti Mulungu, yemwe ndi wachikondi azilanga anthu powawotcha pamoto kwamuyaya? Komanso kodi n’zoona kuti Mulungu amafuna kuti tizingobwereza pemphero lomwelomwelo kambirimbiri pogwiritsa ntchito korona? *

Ndiye munatani?

Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize, misozi ili mbwembwembwe m’maso mwanga. Ndinagulanso Baibulo linalake lachikatolika lomwe linali litangosindikizidwa kumene m’Chitaliyana ndipo ndinayamba kuliwerenga. Kenako Lamlungu lina m’mawa titamaliza mwambo wa Misa, a Mboni awiri anafika kumene ndinkakhala. Tinacheza kwanthawi ndithu ndipo tinakambirana zokhudza Baibulo komanso zimene limaphunzitsa pa nkhani ya chipembedzo choona.

N’chiyani chinakuchititsani chidwi ndi a Mboniwo?

Ndinachita chidwi ndi mmene ankalankhulira akamafotokoza mavesi a m’Baibulo langa lija. Ankaoneka kuti amakhulupirira ndi mtima wonse zomwe Baibulo limanena ndipo ankafotokoza mosatekeseka. Kenako ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi wa Mboni wina, dzina lake Mario. Iye anali woleza mtima ndipo ankabwera Loweruka lililonse cha m’ma 9 koloko m’mawa, zivute zitani.

Kodi ansembe ena anatani ataona kuti mukuphunzira ndi a Mboni?

Analibe nazo chidwi kwenikweni. Ndinapempha ena kuti tiziphunzirira limodzi, koma palibe amene anapitiriza. Koma ineyo ndinkasangalala kwambiri ndi zimene ndinkaphunzira. Ndinapeza yankho la funso lomwe linkandizunguza mutu kwa nthawi yaitali. Funso lake linali loti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthufe tizivutika komanso kuti zoipa zizichitika padzikoli?’

Kodi akuluakulu a chipembedzo chanu sanakuletseni kuphunzira Baibulo?

Mu 1975, ndinapita kangapo konse ku Rome kukawafotokozera maganizo anga. Akuluakuluwa anayesetsa kundiuza kuti ndisinthe maganizo, koma palibe anagwiritsa ntchito Baibulo. Kenako pa 9 January 1976, ndinalemba kalata yowauza kuti si inenso Mkatolika. Patatha masiku awiri ndinachoka kumene ndinkakhala kuja n’kukwera sitima kupita kukasonkhana ndi a Mboni za Yehova. Poyamba sindinkadziwa kuti msonkhanowo ndi waukulu, womwe pamakhala mipingo ya Mboni za Yehova yambiri. Zimene ndinaona pamsonkhanowo zinali zosiyana kwambiri ndi zomwe zinkachitika kutchalitchi kwathu. Pafupifupi onse anali ndi Baibulo ndipo wokamba nkhani akatchula vesi, aliyense ankatsegula Baibulo lake n’kumatsatira akamawerenga.

Kodi achibale anu anatani atamva zimenezi?

Ambiri sanasangalale nazo ndipo ankanditsutsa koopsa. Koma kenako ndinamva kuti mng’ono wanga wina ankaphunziranso ndi a Mboni m’chigawo cha Lombardy. Ndinapita kukamuona ndipo a Mboni a kumeneko anandithandiza kupeza ntchito komanso malo okhala. Kumapeto kwa chaka chomwecho ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

Ndikuona kuti ndili pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu

Kodi mumanong’oneza bondo ndi zomwe munachitazi?

Ayi ndithu. Ndikuona kuti ndili pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu chifukwa ndikumudziwa bwino kuchokera pa zomwe ndaphunzira m’Baibulo, osati pongotengera nzeru za anthu kapena miyambo yachipembedzo. Panopa ndikamaphunzitsa anthu ndimasangalala chifukwa ndimadziwa kuti zomwe ndikuwaphunzitsazo n’zoona.

^ ndime 13 M’Baibulo muli mayankho a mafunsowa ndi enanso ambiri. Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO.