Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Nkhani za ku Africa

Nkhani za ku Africa

Mabungwe ndi anthu ambiri akuyesetsa kuti anthu a ku Africa akhale ndi moyo wabwino. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri a ku Africa akukumanabe ndi mavuto adzaoneni.

Kupha Zipembere Popanda Chilolezo

M’chaka cha 2013, zipembere 1,004 zinaphedwa popanda chilolezo ku South Africa. Chiwerengerochi ndi chokwera kwambiri poyerekeza ndi zipembere 13 zokha zomwe zinaphedwa mu 2007. Ngakhale kuti anthu akupha zipembere zambiri chonchi kuti apeze nyanga zake, anthu ambiri akufunabe nyangazi. Zimenezi zapangitsa kuti kilogalamu imodzi ya nyangazi izidula kwambiri kuposa kilogalamu ya golide. Nyanga imodzi akumatha kuigulitsa pa mtengo wa madola 500,000.

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA: Kodi mayiko angakwanitse kuthetseratu khalidwe lophwanya malamulo?—Yeremiya 10:23.

Anthu Sakuulula Khalidwe la Ziphuphu

Bungwe lina linanena kuti mayiko a kum’mawa kwa Africa ndi ena mwa mayiko omwe kukuchitika kwambiri ziphuphu. (Transparency International) Koma zikuoneka kuti anthu ambiri amene aona munthu akulandira ziphuphu, saulula za khalidweli. Mneneri wa bungweli wa ku Kenya anati: “Anthu ambiri akadziwa za anthu omwe akuchita ziphuphu, saulula chifukwa amaona kuti boma silichitapo chilichonse.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Chiphuphu chimachititsa khungu anthu amaso akuthwa.”—Ekisodo 23:8.

Ku Africa Anthu Akugwiritsa Ntchito Intaneti Kwambiri

Bungwe lina linati, anthu ankaganiza kuti pofika kumapeto kwa chaka cha 2014, anthu 20 pa 100 alionse a ku Africa ndi amene azidzagwiritsa ntchito Intaneti. (International Telecommunication Union) Koma zikuoneka kuti chiwerengero cha anthu a ku Africa omwe akugwiritsa ntchito Intaneti chikukwera kwambiri koposa mmene chikukwerera cha padziko lonse.